Genesis 29:1-35
29 Kenako, Yakobo ananyamuka n’kupitiriza ulendo wake wopita Kum’mawa.+
2 Atafika pamalo enaake anaona chitsime, ndipo panali magulu atatu a nkhosa zitagona pansi, chifukwa m’pamene anthu ankamwetsapo ziweto.+ Pachitsimepo+ panali potseka ndi mwala waukulu.
3 Nkhosa zonse zikafika pamalopo, abusa anali kugubuduza mwala kuuchotsa pachitsimepo n’kutungira nkhosazo madzi kuti zimwe. Akamaliza, anali kubwezeretsa mwalawo pachitsimepo.
4 Pamenepo Yakobo anawafunsa kuti: “Abale anga, kodi mwachokera kuti?” Iwo anayankha kuti: “Tachokera ku Harana.”+
5 Iye anawafunsanso kuti: “Kodi Labani+ mdzukulu wa Nahori+ mumam’dziwa?” Iwo anati: “Inde timam’dziwa.”
6 Ndiyeno iye anawafunsa kuti: “Kodi iye ali bwino?”+ Iwo anayankha kuti: “Ali bwino. Komanso mwana wake Rakele,+ suyo akubwera apoyo ndi nkhosa?”+
7 Kenako Yakobo anawauza kuti: “Inotu si nthawi yosonkhanitsa ziweto, ndi masanatu ano. Zimwetseni madzi, kenako mupite nazo kubusa.”+
8 Iwo anayankha kuti: “Sitiloledwa kutero kufikira magulu onse a nkhosa atafika pano. Zikatero mwala wa pachitsimewu umachotsedwa, ndiyeno m’pamene timazimwetsa madzi nkhosazi.”
9 Akulankhula nawo choncho, Rakele+ anafika ndi nkhosa za bambo ake, popeza anali m’busa wamkazi.+
10 Yakobo ataona Rakele mwana wa Labani, mlongo wa mayi ake, ndiponso nkhosa za Labaniyo, nthawi yomweyo anapita pachitsime paja, n’kugubuduza mwalawo kuuchotsa pachitsimepo. Atatero anatungira madzi nkhosa za Labani, mlongo wa mayi ake.+
11 Ndiyeno Yakobo anapsompsona+ Rakele, n’kulira mofuula+ misozi ili mbwembwembwe.
12 Kenako anayamba kuuza Rakele kuti iye ndi wachibale+ wa bambo ake, ndiponso kuti ndi mwana wa Rabeka. Pamenepo Rakele anathamanga kukauza bambo ake.+
13 Tsopano Labani atangomva za Yakobo, mwana wa mlongo wake, anathamanga kukakumana naye.+ Atafika, anam’kumbatira ndi kum’psompsona, n’kupita naye kunyumba kwake.+ Kumeneko, Yakobo anafotokozera Labani zinthu zonse.
14 Ndiyeno Labani anamuuza kuti: “Ndithu, iwe ndiwe fupa langa ndi mnofu wanga.”+ Choncho anakhala naye mwezi wathunthu.
15 Kenako Labani anafunsa Yakobo kuti: “Kodi ukufuna undigwirire ntchito yaulere+ chifukwa chakuti ndiwe m’bale wanga?+ Ndiuze, kodi ndidzakulipire chiyani?”+
16 Labani anali ndi ana aakazi awiri, wamkulu Leya,+ wamng’ono Rakele.
17 Leya anali ndi maso ofooka, pamene Rakele+ anali chiphadzuwa.+
18 Koma Yakobo anakonda Rakele, ndiye anati: “Ndine wokonzeka kukugwirirani ntchito zaka 7, kuti mudzandipatse Rakele mwana wanu wamng’onoyu.”+
19 Pamenepo Labani anati: “Kuli bwino Rakeleyu ndikupatse iweyo, kusiyana n’kuti ndipatse munthu wina.+ Uzikhalabe ndi ine.”
20 Yakobo anagwira ntchito zaka 7 kuti atenge Rakele.+ Koma iye anangoziona zakazo ngati masiku ochepa chabe, chifukwa anam’konda kwambiri mtsikanayo.+
21 Kenako Yakobo anauza Labani kuti: “Ndipatseni mkazi wanga, chifukwa masiku anga akwana, kuti ndim’kwatire.”*+
22 Pamenepo Labani anasonkhanitsa anthu onse a kumeneko n’kuchita phwando.+
23 Koma madzulo kutada, Labani anatenga Leya mwana wake n’kupita naye kwa Yakobo, ndipo iye anagona naye.
24 Labani anatenganso Zilipa+ kapolo wake, n’kumupereka kwa mwana wake Leya, kuti akhale kapolo wake.
25 Koma kutacha m’mawa, Yakobo anadabwa kuona kuti ali ndi Leya! Ataona zimenezi anakafunsa Labani kuti: “Ndiye chiyani mwachitachi? Kodi si Rakele amene ndakugwirirani ntchito? N’chifukwa chiyani mwandipusitsa chonchi?”+
26 Labani anayankha kuti: “Kwathu kuno, mwambo sulola kukwatitsa wamng’ono mkulu wake asanakwatiwe.
27 Usangalale+ mokwanira ndi mkaziyu mlungu wonse wokondwerera ukwati wake. Kenako ndidzakupatsa mkazi winayu, komatu udzandigwirira ntchito zaka zina 7.”+
28 Chotero Yakobo anasangalaladi mokwanira ndi Leya mlungu wonse wokondwerera ukwati wake. Kenako, Labani anam’patsa mwana wake Rakele ngati mkazi wake.
29 Anaperekanso kapolo wake Biliha+ kwa mwana wake Rakele kuti akhale kapolo wake.
30 Ndiyeno Yakobo anagonanso ndi Rakele, ndipo anam’konda kwambiri Rakele kuposa Leya.+ Motero anagwiriranso ntchito Labani zaka zina 7.+
31 Yehova ataona kuti Leya sanali kukondedwa kwenikweni, anam’patsa mphamvu zobereka,+ koma Rakele anali wosabereka.+
32 Kenako Leya anakhala ndi pakati n’kubereka mwana wamwamuna. Mwanayo anamutcha Rubeni,*+ popeza anati: “N’chifukwa chakuti Yehova waona kusautsika kwanga,+ ndipo tsopano mwamuna wanga ayamba kundikonda kwambiri.”
33 Leya anakhalanso ndi pakati n’kubereka mwana wamwamuna, ndipo anati: “Yehova wandipatsa mwana wina chifukwa wandimvera+ kuti sindikukondedwa kwenikweni.” Choncho mwanayo anamutcha Simiyoni.*+
34 Anakhalanso ndi pakati pena n’kubereka mwana wamwamuna, ndipo anati: “Apa tsopano mwamuna wanga andikonda basi, chifukwa ndamuberekera ana aamuna atatu.” Choncho mwanayo anamutcha Levi.*+
35 Anakhalanso ndi pakati pena n’kubereka mwana wamwamuna, ndipo anati: “Tsopano nditamanda Yehova.” Choncho Leya anatcha mwanayo, Yuda.*+ Atabereka mwana ameneyu, anayamba waleka kubereka.
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti “kuti ndigone naye.”
^ Dzina lakuti “Rubeni” limatanthauza “Onani, ndi Mwana Wamwamuna!”
^ Dzina lakuti “Simiyoni” limatanthauza “Kumvedwa.”
^ Dzina lakuti “Levi” limatanthauza “Kuphatika,” “Kulumikiza,” kapenanso “Kukonda.”
^ Dzina lakuti “Yuda” limatanthauza “Tamandika,” ndiponso “Wotamandika.”