Genesis 6:1-22

6  Pamene anthu anayamba kuchuluka padziko lapansi, kunabadwa ana aakazi.+  Ndiyeno ana a Mulungu+ woona anayamba kuona+ kuti ana aakazi a anthu anali okongola. Chotero, anayamba kudzitengera okha akazi alionse amene anawasankha.  Pambuyo pake, Yehova anati: “Mzimu wanga+ supitiriza mpaka kalekale kulezera mtima anthu,+ popeza alinso athupi.+ Choncho, masiku a moyo wawo adzangokhala zaka 120.”+  M’masiku amenewo ndiponso kupita m’tsogolo, padziko lapansi panali Anefili.* Pa nthawiyo, ana a Mulungu woona anali kugona ndi ana aakazi a anthu ndipo anawaberekera ana. Anawo anali ziphona zakalelo, amuna otchuka.  Pamenepo, Yehova anaona kuti kuipa kwa anthu kwachuluka padziko lapansi, ndipo malingaliro+ onse a m’mitima ya anthu anali oipa okhaokha nthawi zonse.+  Chotero, Yehova anamva chisoni+ kuti anapanga anthu padziko lapansi, ndipo zinam’pweteka kwambiri mumtima.+  Choncho Yehova anati: “Ndidzaseseratu padziko lapansi anthu amene ndinawalenga.+ Kuyambira munthu, nyama yoweta, nyama yokwawa, mpaka cholengedwa chouluka m’mlengalenga,+ chifukwa ndikumva chisoni kuti ndinazipanga.”+  Koma Nowa anayanjidwa ndi Yehova.  Tsopano nayi mbiri ya Nowa. Nowa anali munthu wolungama.+ Iye anali wopanda cholakwa pakati pa anthu a m’nthawi yake. Nowa anayenda ndi Mulungu woona.+ 10  M’kupita kwa nthawi, Nowa anabereka ana aamuna atatu, Semu, Hamu ndi Yafeti.+ 11  Koma dziko lapansi linali litaipa pamaso pa Mulungu woona,+ ndipo linadzaza ndi chiwawa.+ 12  Chotero, Mulungu poyang’ana dziko lapansi anaona kuti laipa,+ chifukwa njira za anthu onse zinali zitaipa.+ 13  Pambuyo pake, Mulungu anauza Nowa kuti: “Nthawi yafika yakuti ndiwononge anthu onse,+ popeza dziko lapansi ladzaza ndi chiwawa chifukwa cha iwo. Choncho ndiwawonongera limodzi ndi dziko lapansi.+ 14  Udzipangire chingalawa cha mtengo wa mnjale.+ Uchigawe zipindazipinda, ndipo uchimate ndi phula+ mkati ndi kunja komwe. 15  Uchipange motere: M’litali chikhale mikono*+ 300, m’lifupi mikono 50, ndipo kutalika kwake kuyambira pansi mpaka pamwamba chikhale mikono 30. 16  Chingalawacho uchiike windo.* Windolo likhale la mpata wa mkono umodzi kuchokera kudenga* lake. Khomo la chingalawacho uliike m’mbali mwake.+ Chikhale cha nyumba zosanjikiza zitatu, yapansi, yapakati, ndi yapamwamba. 17  “Koma ine ndidzabweretsa chigumula+ chamadzi padziko lapansi, kuti chiwononge chamoyo+ chilichonse cha pansi pa thambo, chimene chili ndi mphamvu ya moyo* m’thupi mwake. Chilichonse cha m’dziko lapansi chidzafa.+ 18  Ndipo ndikupanga pangano ndi iwe. Iweyo udzalowe m’chingalawacho limodzi ndi ana ako, mkazi wako, ndi akazi a ana ako.+ 19  Udzalowetsenso m’chingalawacho chamoyo chilichonse cha mtundu uliwonse.+ Udzazilowetse ziwiriziwiri, champhongo ndi chachikazi, kuti zidzasungike zamoyo limodzi nawe.+ 20  Udzalowe nazo ziwiriziwiri za mtundu uliwonse. Zolengedwa zouluka monga mwa mitundu yawo, nyama zoweta monga mwa mitundu yawo,+ nyama zonse zokwawa panthaka monga mwa mitundu yawo, kuti zidzasungike zamoyo.+ 21  Koma iweyo udzatenge chakudya cha mtundu uliwonse chodyedwa.+ Udzachisonkhanitse kuti chidzakhale chakudya chanu ndi cha zamoyo zinazo.”+ 22  Ndipo Nowa anachita zonse motsatira zimene Mulungu anamulamula. Anachitadi momwemo.+

Mawu a M'munsi

Mawu akuti “Anefili” amatanthauza “ogwetsa anzawo.”
“Mkono umodzi” ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu.
Mawu achiheberi ndi “tsoʹhar,” ndipo angatanthauze “windo” kapenanso “denga.”
Kapena kuti “tsindwi.”
Onani Zakumapeto 4.