Genesis 39:1-23

39  Tsopano Yosefe uja, Aisimaeli+ anapita naye ku Iguputo,+ ndipo kumeneko anakam’gulitsa kwa Potifara.+ Potifara anali Mwiguputo, yemwe anali nduna ya panyumba ya Farao, komanso mkulu wa asilikali olondera mfumu.  Koma Yehova anakhalabe ndi Yosefe, ndipo iye anakhala wopambana m’zochita zake zonse.+ Anakhalanso munthu waudindo m’nyumba ya mbuye wake, Mwiguputoyo.  Mbuye wakeyo anaona kuti Yehova anali ndi mnyamatayo, ndi kuti chilichonse chimene anali kuchita, Yehova anali kuchidalitsa.  Potifara anapitiriza kumukonda Yosefe pamene anali kum’tumikira, moti anamusankha kukhala woyang’anira nyumba yake.+ Zonse zimene Potifara anali nazo anazipereka m’manja mwa Yosefe.  Kuyambira pamene Potifara anasankha Yosefe kukhala woyang’anira nyumba yake ndi zinthu zake zonse, Yehova anapitiriza kudalitsa nyumba ya Mwiguputoyo chifukwa cha Yosefe. Yehova anadalitsa zonse za m’nyumba ya Potifara ndi zakumunda zomwe.+  Potsirizira pake, Potifara anasiya zinthu zake zonse m’manja mwa Yosefe,+ moti sanali kudera nkhawa chilichonse kupatulapo chakudya chimene ankadya. Komanso, Yosefe anali wokongola m’maonekedwe ndi wa thupi loumbika bwino.  Kenako, mkazi wa mbuyake anayamba kuyang’ana Yosefe momusirira,+ moti anali kumuuza kuti: “Ugone nane.”+  Koma Yosefe anali kukana+ ndi kuuza mkazi wa mbuye wakeyo kuti: “Chifukwa cha ine, mbuye wanga sadera nkhawa za chilichonse m’nyumba muno, ndipo chilichonse chimene iye ali nacho wachipereka m’manja mwanga.+  M’nyumba muno mulibe woyang’anira woposa ine, ndipo mbuye wanga anaika chilichonse m’manja mwanga kupatulapo inuyo, chifukwa ndinu mkazi wake.+ Ndiye ndingachitirenji choipa chachikulu chonchi n’kuchimwira Mulungu?”+ 10  Mkaziyo anali kulankhula ndi Yosefe tsiku ndi tsiku, koma iye sanamvere zoti agone pambali pake, kuti agone naye.+ 11  Monga mwa masiku onse, tsiku lina Yosefe analowa m’nyumba kukagwira ntchito yake, ndipo m’nyumbamo munalibe antchito ena.+ 12  Pamenepo mkaziyo anam’gwira malaya+ mnyamatayo n’kumuuza kuti: “Ugone nane basi!”+ Koma mnyamatayo anangovula malayawo n’kuwasiya m’manja mwa mkaziyo n’kuthawira panja.+ 13  Mkaziyo ataona kuti mnyamatayo wasiya malaya ake m’manja mwake n’kuthawira panja, 14  anayamba kufuulira antchito ena a m’nyumbamo, kuti: “Taonani! Anatibweretsera mwamuna uyu, Mheberi, kuti adzatichite chipongwe kuti anthu atiseke. Anabwera kwa ine kuti adzandigwiririre, koma ndinakuwa mwamphamvu.+ 15  Ndiye ataona kuti ndayamba kukuwa, anasiya malaya ake pambali pangapa n’kuthawira panja.” 16  Atatero, anasunga malaya a mnyamatayo pambali pake kufikira mwamuna wake atabwera kunyumbako.+ 17  Mwamuna wake atafika, mkaziyo anamuuza kuti: “Wantchito wachiheberi amene munam’bweretsa kwa ife uja, anabwera kwa ine kuti andichite zachipongwe. 18  Koma ataona kuti ndayamba kukuwa, anasiya malaya ake pambali pangapa n’kuthawira panja.”+ 19  Mbuye wa mnyamatayo atamva zimene mkazi wake anamuuza zakuti: “Wantchito wanu anachita zakutizakuti,” mkwiyo wake unayaka.+ 20  Pamenepo, mbuye wake wa Yosefe anatenga Yosefeyo n’kumupereka kundende ya akaidi a mfumu, ndipo anakhala kumeneko.+ 21  Koma Yehova anapitirizabe kukhala ndi Yosefe ndi kumusonyeza kukoma mtima kosatha. Ndipo anachititsa mkulu wa ndende kum’konda Yosefe.+ 22  Choncho, mkulu wa ndendeyo anaika Yosefe kukhala woyang’anira akaidi onse m’ndendemo, ndi chilichonse chimene chinali kuchitika mmenemo.+ 23  Mkulu wa ndendeyo sanali kuyang’aniranso chilichonse chimene chinali m’manja mwake. Zinali choncho chifukwa Yehova anali ndi Yosefe, ndipo chilichonse chimene iye anali kuchita Yehova anali kuchidalitsa.+

Mawu a M'munsi