Genesis 35:1-29
35 Zitatero, Mulungu anauza Yakobo kuti: “Nyamuka, pita ku Beteli ukakhale kumeneko.+ Ukamangire guwa lansembe Mulungu woona, amene anaonekera kwa iwe pamene unali kuthawa Esau m’bale wako.”+
2 Ndiyeno Yakobo anauza anthu a m’banja lake ndi onse amene anali naye kuti: “Chotsani milungu yachilendo imene ili pakati panu.+ Dziyeretseni ndipo sinthani zovala zanu.+
3 Mukatero, tinyamuke tipite ku Beteli. Kumeneko ndikamangira guwa lansembe Mulungu woona, amene anandimvera m’tsiku la kusautsika kwanga,+ posonyeza kuti anali nane pa ulendo wanga.”+
4 Choncho anthuwo anapereka kwa Yakobo milungu yachilendo+ yonse imene anali nayo, ndi ndolo* zimene anavala m’makutu. Kenako Yakobo anafotsera+ zinthuzo pansi pa mtengo waukulu pafupi ndi Sekemu.
5 Atatero anachoka, ndipo anthu a m’mizinda yowazungulira anagwidwa ndi mantha ochokera kwa Mulungu,+ moti sanatsatire ana a Yakobo kuti akawathire nkhondo.
6 Potsirizira pake Yakobo anafika ku Luzi+ komwe ndi ku Beteli, m’dziko la Kanani. Iye anafika kumeneko pamodzi ndi anthu onse amene anali naye.
7 Anamanga guwa lansembe kumeneko, n’kutchula malowo kuti Eli-beteli.* Malowo anawatcha dzinali chifukwa Mulungu woona anaonekera kwa iye kumeneko, pa nthawi imene anali kuthawa m’bale wake.+
8 Pambuyo pake Debora+ mlezi wa Rabeka anamwalira, ndipo anamuika ku Beteli m’munsi mwa phiri, pansi pa mtengo waukulu. Choncho mtengowo anautcha kuti Aloni-bakuti.*
9 Tsopano Mulungu anaonekeranso kwa Yakobo pamene anali kubwerera kwawo kuchokera ku Padana-ramu,+ n’kumudalitsa.+
10 Mulungu anamuuza kuti: “Iwe dzina lako ndi Yakobo.+ Koma kuyambira tsopano, dzina lako silikhalanso Yakobo, ukhala Isiraeli.” Choncho anayamba kumutchula kuti Isiraeli.+
11 Mulungu anamuuzanso kuti: “Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse.+ Ubereke ndipo ukhale ndi ana ambiri. Mitundu ndi mafuko ambiri adzatuluka mwa iwe, ndipo mafumu adzatuluka m’chiuno mwako.+
12 Dziko limene ndinalipereka kwa Abulahamu ndi Isaki, ndidzalipereka kwa iwe ndi kwa mbewu yako+ yobwera pambuyo pako.”+
13 Kenako Mulungu anachoka pamwamba pamene anaima polankhula ndi Yakobo.+
14 Zitatero, Yakobo anaimika mwala wachikumbutso pamalo pamene anali kulankhula nayepo,+ kenako pamwalawo anathirapo nsembe yachakumwa ndi mafuta.+
15 Ndiyeno Yakobo anapitiriza kutchula malo amene Mulungu analankhula nayewo kuti Beteli.+
16 Kenako ananyamuka kuchoka ku Beteliko. Padakali mtunda wautali ndithu kuti afike ku Efurata,+ inafika nthawi yoti Rakele abereke, koma poberekapo anali kuvutika kwambiri.+
17 Pamene kubereka kunafika popweteka kwambiri, mzamba* anamuuza kuti: “Usaope, pakuti ubereka mwana wina wamwamuna.”+
18 Pomalizira pake, pamene moyo wake+ unali kutayika (pakuti anamwalira),+ anatcha mwanayo dzina lakuti Beni-oni.* Koma bambo ake anamutcha Benjamini.*+
19 Umu ndi mmene Rakele anamwalirira, ndipo anamuika m’manda ali m’njira popita ku Efurata, komwe ndi ku Betelehemu.+
20 Yakobo anaika mwala pamandapo. Mwala umenewo ulipobe mpaka lero pamanda a Rakele.+
21 Pambuyo pake, Isiraeli ananyamuka n’kukamanga hema wake chapatsogolo ndithu kupitirira nsanja ya Ederi.+
22 Isiraeli atamanga msasa+ m’dziko limenelo, Rubeni anagona ndi Biliha mkazi wamng’ono* wa bambo ake, ndipo Isiraeli anamva zimene zinachitikazo.+
Yakobo anali ndi ana aamuna 12.
23 Ana aamuna amene Leya anaberekera Yakobo anali Rubeni+ mwana wake woyamba, Simiyoni, Levi, Yuda, Isakara ndi Zebuloni.
24 Ana amene Rakele anaberekera Yakobo anali Yosefe ndi Benjamini.
25 Ana amene Biliha kapolo wa Rakele anaberekera Yakobo anali Dani ndi Nafitali.
26 Ana amene Zilipa kapolo wa Leya anaberekera Yakobo anali Gadi ndi Aseri. Amenewa ndiwo ana aamuna a Yakobo amene anabereka ku Padana-ramu.
27 Potsirizira pake Yakobo anafika kwa bambo ake Isaki ku Mamure,+ m’dera la Kiriyati-ariba,+ komwe ndi ku Heburoni. Uku n’kumenenso Abulahamu ndi Isaki anakhalako monga alendo.+
28 Masiku onse a Isaki anakwana zaka 180.+
29 Kenako Isaki anamwalira, ndipo anaikidwa m’manda n’kugona ndi makolo ake. Anamwalira ali wokalamba, wokhutira ndi masiku ake.+ Ana ake, Esau ndi Yakobo, anamuika m’manda.+
Mawu a M'munsi
^ Ena amati, “masikiyo.”
^ Dzina lakuti “Eli-beteli” limatanthauza kuti “Mulungu wa Beteli.”
^ Dzina lakuti “Aloni-bakuti” limatanthauza “Chimtengo Chachikulu Cholirirapo.”
^ “Mzamba” ndi munthu amene amathandiza amayi pobereka. Ena amamutcha “namwino.”
^ Dzina lakuti “Beni-oni” limatanthauza “Mwana wa Chisoni Changa.”
^ Dzina lakuti “Benjamini” limatanthauza “Mwana wa Dzanja Langa Lamanja.”
^ “Mkazi wamng’ono” ameneyu anali mdzakazi wa Rakele.