Genesis 50:1-26

50  Pamenepo Yosefe anakumbatira mtembo wa bambo ake+ ndipo analira kwambiri n’kuupsompsona.+  Kenako Yosefe analamula atumiki ake omwe anali madokotala, kuti akonze mtembo wa bambo ake ndi mankhwala kuti usawonongeke.+ Choncho madokotalawo anakonza mtembo wa Isiraeli.  Anatenga masiku 40 kukonza thupi lake, pakuti kukonza mtembo kunali kutenga masiku ochuluka choncho. Aiguputowo anamulirabe Isiraeli kwa masiku 70.+  Masiku olira maliro a Yakobo atatha, Yosefe anauza a m’nyumba ya Farao kuti: “Ngati mungandikomere mtima,+ chonde ndilankhulireni kwa Farao kuti,  ‘Bambo anga anandilumbiritsa+ kuti: “Inetu ndikufa.+ Ukandiike m’manda+ amene ndinadzikonzera m’phanga kudziko la Kanani.”+ Ndiye chonde, ndiloleni ndipite ndikaike bambo anga, pambuyo pake ndikabweranso.’”  Pamenepo Farao anayankha kuti: “Pita ukaike bambo ako monga anakulumbiritsira.”+  Choncho Yosefe anapita kukaika bambo ake. Atumiki onse a Farao, akuluakulu+ a m’nyumba yake, ndi akuluakulu onse a m’dziko la Iguputo anam’perekeza.  Onse a m’nyumba ya Yosefe, abale ake, ndi a m’nyumba ya bambo ake,+ anapita naye limodzi. Ku Goseni kunangotsala ana awo aang’ono, nkhosa, mbuzi ndi ng’ombe zawo.  Anatenganso magaleta+ ndi a pamahatchi, moti gululo linakhala lalikulu kwambiri. 10  Kenako anafika pamalo opunthira mbewu+ a Atadi m’chigawo cha Yorodano.+ Kumeneko, anthuwo analira ndi kubuma kwakukulu, ndipo Yosefe anachita nawo miyambo yolirira maliro a bambo ake kwa masiku 7.+ 11  Akanani amene anali kukhala m’dzikolo anaona miyambo yolirira maliro imene inali kuchitikira pamalo opunthira mbewu a Atadi. Ataona choncho, iwo anati: “Maliro amene agwera Aiguputowa ndi aakulu!” N’chifukwa chake malowo anawatcha Abele-miziraimu,* ndipo ali m’chigawo cha Yorodano.+ 12  Ana a Yakoboyo anam’chitira zonse monga mmene iye anawalamulira.+ 13  Anamunyamula n’kupita naye kudziko la Kanani. Kumeneko anakamuika m’phanga m’munda wa Makipela, woyang’anana ndi munda wa Mamure.+ Mundawo ndi umene Abulahamu anagula kwa Efuroni Mhiti, kuti akhale ndi manda. 14  Yosefe ataika bambo ake m’manda, anabwerera ku Iguputo limodzi ndi abale ake ndi onse amene anam’perekeza pokaika bambo ake. 15  Bambo awo atamwalira, abale ake a Yosefe anayamba kunena kuti: “Mwina Yosefe anatisungira chidani,+ ndipo ndithu atibwezera pa zoipa zonse zimene tinam’chitira.”+ 16  Choncho iwo anauza Yosefe kuti: “Bambo anu asanamwalire anatisiyira mawu. Anatiuza kuti, 17  ‘Mukamuuze Yosefe kuti: “Chonde ndikukupempha, ukhululuke+ chiwembu cha abale ako, ndi kuchimwa kwawo pa zoipa zimene anakuchitira.”’+ Ndiye chonde, tikhululukireni ife akapolo a Mulungu wa bambo anu.”+ Atamuuza zimenezi, Yosefe analira kwambiri. 18  Kenako abale akewonso anafika, n’kudzigwetsa pansi pamaso pake, n’kunena kuti: “Tikudzipereka kwa inu ngati akapolo anu.”+ 19  Pamenepo Yosefe anawauza kuti: “Musaope ayi. Kodi ine ndatenga malo a Mulungu?+ 20  Inu munali ndi cholinga chondichitira zoipa. Koma Mulungu anali ndi cholinga chabwino, kuti apulumutse miyoyo ya anthu ambiri ngati mmene akuchitira panomu.+ 21  Choncho musachite mantha. Ine ndipitiriza kukugawirani chakudya limodzi ndi ana anu.”+ Anawalimbikitsa n’kuwatsimikizira motero. 22  Yosefe anakhalabe ku Iguputoko limodzi ndi a m’nyumba ya bambo ake. Zaka za moyo wa Yosefe zinali 110 zonse pamodzi. 23  Yosefe anakhalabe ndi moyo mpaka kuona ana a Efuraimu a m’badwo wachitatu.+ Anaonanso ana a Makiri+ mwana wa Manase. Onsewo anabadwira pamiyendo pa Yosefe.+ 24  Potsirizira pake, Yosefe anauza abale ake kuti: “Ine ndikufa, koma Mulungu adzakucheukirani,+ ndipo adzakutulutsani ndithu m’dziko lino. Adzakupititsani kudziko limene analonjeza polumbira kwa Abulahamu, kwa Isaki ndi kwa Yakobo.”+ 25  Tsopano Yosefe analumbiritsa ana a Isiraeliwo, kuti: “Ndithu Mulungu adzakucheukirani. Akadzatero mudzanyamule mafupa anga pochoka kuno.”+ 26  Patapita nthawi, Yosefe anamwalira ali ndi zaka 110. Thupi lake analikonza ndi mankhwala kuti lisawonongeke,+ ndipo analiika m’bokosi ku Iguputoko.

Mawu a M'munsi

Dzina lakuti “Abele-miziraimu” limatanthuza kuti, “Kulira Maliro kwa Aiguputo.”