Genesis 33:1-20

33  Tsopano Yakobo anakweza maso ake n’kuona Esau akubwera limodzi ndi amuna 400.+ Ataona choncho, anagawa ana ake n’kuwapereka kwa Leya, kwa Rakele, ndi kwa akapolo ake awiri aja.+  Akapolowo ndi ana awo anawaika patsogolo penipeni,+ Leya ndi ana ake anawaika pakati,+ ndipo Rakele ndi Yosefe anawaika pambuyo.+  Koma iyeyo anapita patsogolo pawo, n’kuyamba kugwada, n’kumaweramitsa nkhope yake pansi mpaka nthawi 7. Anachita zimenezi mpaka kufika pafupi ndi m’bale wakeyo.+  Esau anathamanga kudzakumana naye,+ ndipo anamukumbatira+ ndi kum’psompsona. Atakumbatirana, onse awiri anagwetsa misozi kwambiri.  Kenako, Esau anakweza maso ake n’kuona akazi ndi ana. Ndiyeno anafunsa Yakobo kuti: “Nanga amene uli nawowa ndani?” Iye anayankha kuti: “Amenewa ndi ana amene Mulungu wapatsa ine kapolo wanu.”+  Pamenepo akapolo aja anafika pafupi limodzi ndi ana awo n’kugwada pansi.  Nayenso Leya anafika pafupi limodzi ndi ana ake n’kugwada pansi. Potsirizira pake, Yosefe ndi Rakele anafika pafupi, nawonso n’kugwada pansi.+  Tsopano Esau anafunsa kuti: “Nanga n’chifukwa chiyani watumiza khamu lonse limene ndakumana nalo lija?”+ Poyankha iye anati: “Ndachita zimenezi kuti mundikomere mtima mbuyanga.”+  Ndiyeno Esau anati: “Ziweto ndili nazo zambiri, m’bale wanga.+ Zako ndi zako, ukhale nazo.” 10  Koma Yakobo anati: “Ayi chonde, musatero. Ngati mwandikomeradi mtima,+ landirani mphatso yangayi, popeza cholinga chake chinali chakuti ndione nkhope yanu, ndipo ndaionadi. Zili ngati ndaona nkhope ya Mulungu, chifukwa mwandilandira ndi manja awiri.+ 11  Chonde, landirani mphatso yokufunirani mafuno abwinoyi kuchokera kwa ine,+ chifukwa Mulungu wandikomera mtima, ndipo wandipatsa chilichonse.”+ Anamuumirizabe mpaka analandira mphatsoyo.+ 12  Pambuyo pake Esau anati: “Tiye tinyamuke tizipita, ine nditsogole.” 13  Koma Yakobo anati: “Monga mukudziwa mbuyanga, anawa ndi osakhwima, komanso ndili ndi nkhosa ndi ng’ombe zoyamwitsa.+ Tikaziyendetsa mofulumira kwambiri, ngakhale tsiku limodzi lokha, ndithu zifa zonse.+ 14  Chonde mbuyanga, tsogolani. Ine kapolo wanu ndizibwera m’mbuyo mwanu. Ndiziyenda pang’onopang’ono mogwirizana ndi mayendedwe a ziwetozi+ ndi kuyenda kwa anawa.+ Ndikakupezani ku Seiri, mbuyanga.”+ 15  Ndiyeno Esau anati: “Chabwino, ndiye ndikupatseko ena mwa anyamata angawa kuti akuthandize.” Koma iye anati: “Ayi musachite kutero. Musavutike mbuyanga,+ ndiyenda bwinobwino.” 16  Choncho, Esau anatembenuka kubwerera ku Seiri tsiku lomwelo. 17  Tsopano Yakobo ananyamuka ulendo wopita ku Sukoti.+ Kumeneko anamanga nyumba yake ndi makola a ziweto zake.+ N’chifukwa chake malowo anawatcha kuti Sukoti.* 18  Patapita nthawi, Yakobo anafika bwinobwino kumzinda wa Sekemu,+ m’dziko la Kanani,+ akuchokera ku Padana-ramu.+ Atafika, anamanga msasa pafupi ndi mzindawo. 19  Kenako anagula malo ndipo anamangapo msasa. Anawagula ndi ndalama zasiliva 100, kwa ana a Hamori, bambo wake wa Sekemu.+ 20  Atatero, anamangapo guwa lansembe n’kulitcha Mulungu, Mulungu wa Isiraeli.+

Mawu a M'munsi

Dzina lakuti “Sukoti” limatanthauza “Makola” ndiponso “Makola Adenga.”