Genesis 30:1-43
30 Ndiyeno Rakele ataona kuti sanaberekere Yakobo mwana, anayamba kuchitira nsanje m’bale wake. Iye anauza Yakobo+ kuti: “Mundipatse ana, apo ayi kuli bwino ndingofa.”+
2 Pamenepo Yakobo anamupsera mtima kwambiri Rakele n’kumuyankha kuti:+ “Kodi ine ndine Mulungu amene akukulepheretsa kuberekayo?”+
3 Kenako Rakele anati: “Nayu kapolo wanga Biliha.+ Mugone naye kuti andiberekere mwana woti akhale wanga,* kuti ineyonso ndikhale ndi ana kuchokera kwa iye.”+
4 Choncho Rakele anapereka Biliha kapolo wake kwa Yakobo, ndipo Yakobo anagona nayedi.+
5 Chotero Biliha anakhala ndi pakati ndipo patapita nthawi anam’berekera Yakobo mwana wamwamuna.+
6 Zitatero, Rakele anati: “Mulungu wakhala monga woweruza+ wanga ndipo wamvera mawu anga, choncho wandipatsa mwana wamwamuna.” N’chifukwa chake Rakele anatcha mwanayo dzina lakuti Dani.*+
7 Biliha kapolo wa Rakele anakhalanso ndi pakati moti patapita nthawi anam’berekera Yakobo mwana wina wamwamuna.
8 Ndiyeno Rakele anati: “Ndalimbana mwamphamvu ndi m’bale wanga ndipo ndapambananso.” Chotero anatcha mwanayo dzina lakuti Nafitali.*+
9 Leya ataona kuti wasiya kubereka, anapereka kapolo wake Zilipa kwa Yakobo kuti akhale mkazi wake.+
10 Patapita nthawi, Zilipa kapolo wa Leya anaberekera Yakobo mwana wamwamuna.
11 Pamenepo Leya anati: “Ndachita mwayi!” Chotero anatcha mwanayo dzina lakuti Gadi.*+
12 Kenako, Zilipa kapolo wa Leya anaberekera Yakobo mwana wina wamwamuna.
13 Mwanayo atabadwa, Leya anati: “Ndasangalala kwambiri! Akazi adzanditcha wodala.”+ Chotero Leya anatcha mwanayo dzina lakuti Aseri.*+
14 Pa nthawi yokolola tirigu,+ Rubeni+ anapita kutchire kukayenda. Kumeneko anapezako zipatso za mandereki,* ndipo anawatenga n’kupita nawo kwa Leya mayi ake. Ndiyeno Rakele anapempha Leya kuti: “Chonde, ndigawireko mandereki+ a mwana wakowa.”
15 Pamenepo, Leya anayankha Rakele kuti: “Kodi ukuyesa ndi nkhani yaing’ono kuti iweyo unatenga mwamuna wanga?+ Tsopano ukufuna kutenganso mandereki a mwana wanga?” Ndipo Rakele anati: “Pa chifukwa chimenechi, usiku walero mwamunayu agona ndi iwe kuti tisinthane ndi mandereki a mwana wakowa.”
16 Pamene Yakobo anali kuchokera kumunda madzulo,+ Leya anakamuchingamira n’kumuuza kuti: “Lero mugona ndi ine, chifukwa ine ndakugulani ndithu ndi mandereki a mwana wanga.” Usiku umenewo Yakobo anagonadi ndi Leya.+
17 Mulungu anamvera Leya n’kumuyankha, ndipo anakhala ndi pakati. Patapita nthawi, Leya anaberekera Yakobo mwana wamwamuna wachisanu.+
18 Mwanayo atabadwa, Leya anati: “Mulungu wandipatsa mphoto chifukwa ndapereka kapolo wanga kwa mwamuna wanga.” Chotero Leya anatcha mwanayo dzina lakuti Isakara.*+
19 Leya anakhalanso ndi pakati, moti patapita nthawi anaberekera Yakobo mwana wamwamuna wa 6.+
20 Ndiyeno Leya anati: “Mulungu wandipatsadi mphoto yabwino. Tsopano mwamuna wanga ayamba kukondwera nane,+ chifukwa ndam’berekera ana aamuna 6.”+ Chotero Leya anatcha mwanayo dzina lakuti Zebuloni.*+
21 Kenako, Leya anabereka mwana wamkazi ndipo anamutcha kuti Dina.+
22 Potsirizira pake, Mulungu anakumbukira Rakele ndipo anamumvera n’kumuyankha mwa kum’patsa mphamvu zobereka.+
23 Rakele anakhala ndi pakati n’kubereka mwana wamwamuna. Ndiyeno iye anati: “Mulungu wandichotsera chitonzo.”+
24 Chotero Rakele anatcha mwanayo dzina lakuti Yosefe,*+ ndipo anati: “Yehova wandiwonjezera mwana wina wamwamuna.”
25 Rakele atabereka Yosefe, nthawi yomweyo Yakobo anauza Labani kuti: “Ndiloleni ndizipita kwathu, kudziko lakwathu.+
26 Ndipatseni akazi anga ndi ana anga amene ndakugwirirani ntchito kuti ndizipita, pakuti inuyo mukudziwa ntchito imene ndakugwirirani.”+
27 Koma Labani anauza Yakobo kuti: “Ngati wandikomera mtima, ungokhala konkuno. Ndaombeza maula ndipo ndapeza kuti Yehova akundidalitsa chifukwa cha iwe.”+
28 Anatinso: “Ndiuze malipiro ako ndipo ndikupatsa.” +
29 Yakobo anamuyankha Labani kuti: “Inuyo mukudziwa ntchito imene ndakugwirirani, ndiponso mmene ndasamalira ziweto zanu.+
30 Mukudziwa kuti ine ndisanabwere munali ndi zochepa. Tsopano onani mmene Yehova wakudalitsirani ndi mmene zachulukira kuchokera pamene ndinabwera.+ Ndiye kodi ineyo ndidzayamba liti kugwirira ntchito banja langa?”+
31 Kenako Labani anati: “Ndikupatse chiyani?” Yakobo anayankha kuti: “Musandipatse kanthu.+ Koma mukachita zimene ndikupempheni pano, ndiyambiranso kuweta ziweto zanu,+ ndipo ndipitiriza kuziyang’anira.+
32 Ine ndipita kukayenda pakati pa ziweto zanu zonse lero. Inuyo mukapatule nkhosa iliyonse yamathothomathotho kapena yamawangamawanga, ndi nkhosa iliyonse yaing’ono yamphongo yofiirira, ndi mbuzi iliyonse yaikazi yamawangamawanga kapena yamathothomathotho. Ngati ziweto zoterozo zidzabadwe pambuyo pake, ndizo zidzakhale malipiro anga.+
33 Tsiku lililonse limene mudzabwere kudzaona malipiro+ anga, mudzaona chilungamo changa. Mukadzapeza mbuzi iliyonse yaikazi yopanda mathothomathotho kapena mawangamawanga, ndi nkhosa iliyonse yaing’ono yamphongo yomwe si yofiirira ili ndi ine, imeneyo ndiye kuti ndaba.”+
34 Pamenepo Labani anati: “Chabwino, zikhale monga waneneramo.”+
35 Chotero tsiku lomwelo, Labani anapatula mbuzi zamphongo zamizeremizere ndi zamawangamawanga, ndiponso mbuzi zonse zazikazi zamathothomathotho ndi zamawangamawanga pakati pa ziweto zake. Anapatulanso nkhosa iliyonse imene inali ndi banga loyera ndi nkhosa iliyonse yamphongo yaing’ono yofiirira, n’kuzipereka kwa ana ake.
36 Atatero anapita ndi ziweto zakezo kumalo amene anali pamtunda woyenda masiku atatu kuchokera pamene panali ziweto za Yakobo. Yakobo anapitiriza kuweta ziweto zotsala za Labani.
37 Ndiyeno Yakobo anatenga timitengo+ tatiwisi ta mtengo wa mlanje,+ ta mtengo wa amondi+ ndi ta mtengo wa katungulume,+ n’kutisenda makungwa mwa apo ndi apo, mwakuti choyera chamkati mwake chinaonekera.
38 Potsirizira pake, anatenga timitengo timene anatisendasenda tija n’kutiika m’ngalande zimene ziweto zimamwera madzi.+ Anatiika mmenemo kuti ziweto zikabwera kudzamwa madzi, zazikazi zikaona timitengoto zizitentha thupi kukonzekera kutenga bere.
39 Motero ziweto zazikazi zikaona timitengoto zinali kutenthadi thupi kukonzekera kutenga bere. Zikatero, zinali kuswa ana amizeremizere ndi amawangamawanga.+
40 Kenako, Yakobo anachotsapo nkhosa zamphongo zing’onozing’ono n’kuziika pazokha. Atatero, anapatula nkhosa zonse zamizeremizere ndi zofiirira zimene zinali pakati pa ziweto za Labani. Kenako anatembenuza nkhosa zotsalazo kuti ziyang’ane zamizeremizere ndi zofiirira zija. Iye anaika ziweto zake pazokha, ndipo sanaziphatikize ndi ziweto za Labani.
41 Nthawi zonse ziweto zazikazi zamphamvu+ zikatentha thupi, Yakobo anali kuika timitengo tija m’ngalande momwera madzi+ kuti nkhosazo zitiyang’ane pamene zili zotentha thupi.
42 Koma nkhosazo zikakhala zofooka, iye sanali kuika timitengo tija momwera madzimo. Chotero, nthawi zonse nkhosa zofooka zinali za Labani koma zamphamvu zinali za Yakobo.+
43 Chuma cha Yakobo chinapitirira kuwonjezeka. Iye anakhala ndi ziweto zambiri, antchito aakazi ndi aamuna, ngamila ndi abulu.+
Mawu a M'munsi
^ Mawu ake enieni, “aberekere pamawondo anga.”
^ Dzina lakuti “Dani” limatanthauza “Woweruza.”
^ Dzina lakuti “Nafitali” limatanthauza “Ndalimbana Nazo.”
^ Dzina lakuti “Gadi” limatanthauza “Mwayi.”
^ Dzina lakuti “Aseri” limatanthauza “Kusangalala” ndiponso “Chisangalalo.”
^ “Mandereki” ndi chitsamba cha m’gulu la mbatata, chimene chimabereka zipatso.
^ Dzina lakuti “Isakara” limatanthauza “Iye Ndi Malipiro” ndiponso kuti, “Amabweretsa Malipiro.”
^ Dzina lakuti “Zebuloni” limatanthauza “Malo Okhala,” kapenanso “Kulolera.”
^ Dzina lakuti “Yosefe” limatanthauza “Woonjezera.”