Genesis 11:1-32
11 Tsopano dziko lonse lapansi linali ndi chilankhulo chimodzi ndipo anthu anali kugwiritsa ntchito mawu ofanana.
2 Pamene anthuwo analowera chakum’mawa, anapeza chigwa m’dera la Sinara+ n’kukhazikika kumeneko.
3 Kenako anauzana kuti: “Tiyeni tiumbe njerwa tiziotche.” Atatero, anayamba kumanga ndi njerwa, n’kumagwiritsa ntchito phula ngati matope omangira.+
4 Ndiyeno anati: “Tiyeni timange mzinda wathuwathu, ndipo nsanja yake ikafike m’mwamba mwenimweni.+ Tikatero tidzipangira dzina loti titchuke nalo,+ ndipo sitibalalikana padziko lonse lapansi.”+
5 Kenako, Yehova anatsikirako kukaona mzinda ndi nsanja imene ana a anthu anali kumanga.+
6 Pamenepo Yehova anati: “Taonani! Izi n’zimene anthuwa ayamba kuchita popeza ndi amodzi ndipo onse ali ndi chilankhulo chimodzi.+ Mmene zililimu, angathe kuchita chilichonse chimene akuganiza.+
7 Choncho, tiyeni+ tipiteko kuti tikasokoneze+ chilankhulo chawo, kuti asamamvane polankhula.”+
8 Motero, Yehova anawabalalitsa pamalopo, kuti afalikire padziko lonse lapansi.+ Zitatero, iwo anasiya pang’onopang’ono kumanga mzindawo.+
9 Mzindawo unatchedwa Babele,+ chifukwa kumeneko, Yehova anasokoneza chilankhulo cha anthu onse, ndipo Yehova anabalalitsira+ anthuwo padziko lonse lapansi.
10 Tsopano iyi ndi mbiri ya Semu.+
Semu anali ndi zaka 100 pamene anabereka Aripakisadi,+ patapita zaka ziwiri pambuyo pa chigumula.
11 Atabereka Aripakisadi, Semu anakhalabe ndi moyo zaka zina 500. Pa zaka zimenezi, anabereka ana aamuna ndi aakazi.+
12 Aripakisadi atakhala ndi moyo zaka 35, anabereka Shela.+
13 Atabereka Shela, Aripakisadi anakhalabe ndi moyo zaka zina 403. Pa zaka zimenezi, anabereka ana aamuna ndi aakazi.
14 Shela atakhala ndi moyo zaka 30, anabereka Ebere.+
15 Atabereka Ebere, Shela anakhalabe ndi moyo zaka zina 403. Pa zaka zimenezi, anabereka ana aamuna ndi aakazi.
16 Ebere atakhala ndi moyo zaka 34, anabereka Pelegi.+
17 Atabereka Pelegi, Ebere anakhalabe ndi moyo zaka zina 430. Pa zaka zimenezi, anabereka ana aamuna ndi aakazi.
18 Pelegi atakhala ndi moyo zaka 30, anabereka Reu.+
19 Atabereka Reu, Pelegi anakhalabe ndi moyo zaka zina 209. Pa zaka zimenezi, anabereka ana aamuna ndi aakazi.
20 Reu atakhala ndi moyo zaka 32, anabereka Serugi.+
21 Atabereka Serugi, Reu anakhalabe ndi moyo zaka zina 207. Pa zaka zimenezi, anabereka ana aamuna ndi aakazi.
22 Serugi atakhala ndi moyo zaka 30, anabereka Nahori.+
23 Atabereka Nahori, Serugi anakhalabe ndi moyo zaka zina 200. Pa zaka zimenezi, anabereka ana aamuna ndi aakazi.
24 Nahori atakhala ndi moyo zaka 29, anabereka Tera.+
25 Atabereka Tera, Nahori anakhalabe ndi moyo zaka zina 119. Pa zaka zimenezi, anabereka ana aamuna ndi aakazi.
26 Tera anakhala ndi moyo zaka 70, kenako anabereka Abulamu,+ Nahori+ ndi Harana.
27 Tsopano iyi ndi mbiri ya Tera.
Tera anabereka Abulamu, Nahori ndi Harana. Harana anabereka Loti.+
28 Pambuyo pake Harana anamwalira mumzinda wa Akasidi+ wa Uri,+ kumene anabadwira. Anamwalira bambo ake Tera adakali ndi moyo.
29 Abulamu ndi Nahori anakwatira. Mkazi wa Abulamu anali Sarai,+ pamene mkazi wa Nahori anali Milika,+ mwana wa Harana. Harana ameneyu analinso bambo ake a Yisika.
30 Koma Sarai anali wosabereka,+ choncho analibe mwana.
31 Pambuyo pake Tera anatenga mwana wake Abulamu, mdzukulu wake+ Loti mwana wa Harana, Sarai+ mpongozi wake, mkazi wa mwana wake Abulamu, ndi kunyamuka kuchoka mumzinda wa Akasidi wa Uri, kupita kudziko la Kanani.+ Kenako, anafika ku Harana+ ndipo anakhala kumeneko.
32 Choncho masiku a Tera anakwana zaka 205. Kenako, iye anamwalira ku Harana.