Genesis 20:1-18

20  Tsopano Abulahamu anasamutsa msasa wake+ n’kupita kudziko la Negebu. Kenako anakakhala monga mlendo ku Gerari+ pakati pa Kadesi+ ndi Shura.+  Kumeneko Abulahamu anabwerezanso kunena za Sara mkazi wake kuti: “Ndi mlongo wanga.”+ Abimeleki* mfumu ya ku Gerariko atamva zimenezo, anaitanitsa Sara kuti abwere kwa iye.+  Pambuyo pake Mulungu anafikira Abimeleki usiku m’maloto n’kumuuza kuti: “Ufatu iwe chifukwa cha mkazi amene watengayu,+ pakuti ndi mkazi wa mwini.”+  Koma Abimeleki anali asanagone naye Sarayo.+ Chotero iye anati: “Yehova, kodi mudzapha mtundu wosalakwa?+  Kodi mwamunayu sanandiuze yekha kuti, ‘Ndi mlongo wanga’? Ndipo mkaziyunso sananene yekha kuti, ‘Ndi mlongo wanga’? Zimenezitu ndachita popanda mtima wanga kunditsutsa, komanso mosadziwa kuti ndikulakwa.”+  Pamenepo Mulungu woona anamuuza m’malotomo kuti: “Inenso ndinadziwa kuti mtima wako sunakutsutse pochita zimenezi,+ ndipo ndinakutchinga kuti usandichimwire.+ Ndiye chifukwa chake sindinakulole kuti umukhudze mkaziyu.+  Tsopano bweza mkaziyo kwa mwamuna wake. Mwamunayo ndi mneneri,+ ndipo adzakupempherera.+ Ukatero udzakhala ndi moyo. Koma ukapanda kumubweza, udziwe kuti, iweyo ndi anthu ako onse mufa ndithu.”+  Kenako Abimeleki anadzuka m’mawa kwambiri n’kuitana antchito ake onse n’kuwauza zonsezi ndipo anthuwo anachita mantha kwambiri.  Tsopano Abimeleki anaitana Abulahamu, n’kumufunsa kuti: “N’chiyani wachita kwa ifechi? Ndakuchimwira chiyani ine, kuti ubweretse tchimo lalikulu+ chonchi pa ine ndi ufumu wanga? Wandichitira zinthu zosayenera kuchita.”+ 10  Abimeleki anapitiriza kufunsa Abulahamu kuti: “Cholinga chako chinali chiyani makamaka pochita zimenezi?”+ 11  Abulahamu anayankha kuti: “Ndachita zimenezi poganiza kuti, ‘Ndithu anthu a kuno saopa Mulungu,+ andipha ndithu chifukwa cha mkazi wangayu.’+ 12  Komabe, ndi mlongo wangadi ameneyu. Bambo athu ndi amodzi, tinangosiyana mayi, ndipo ndinam’kwatira.+ 13  Mulungu atandichotsa kunyumba kwa bambo anga+ kuti ndiyambe kuyendayenda, ndinauza mkazi wangayu kuti, ‘Undisonyeze kukoma mtima kosatha+ motere: Kumalo alionse kumene tizifika, uziuza anthu za ine kuti: “Ndi mlongo wanga.”’”+ 14  Tsopano Abimeleki anatenga nkhosa, ng’ombe, ndiponso antchito aamuna ndi aakazi n’kumupatsa Abulahamu, ndi kumubwezeranso mkazi wake Sara.+ 15  Abimeleki ananenanso kuti: “Dziko lonseli ndi langa. Ungathe kukhala kulikonse kumene ungakonde.”+ 16  Kenako Abimeleki anauza Sara kuti: “Ndalama zasiliva 1,000 izi ndikuzipereka kwa mlongo wakoyu.+ Zikhale umboni wotsimikizira+ kwa onse amene muli nawo, ndi kwa wina aliyense, kuti sunaipitsidwe.” 17  Kenako Abulahamu anayamba kum’pempherera iye kwa Mulungu woona.+ Chotero Mulungu anachiritsa Abimeleki ndi mkazi wake, ndi akapolo ake aakazi, moti iwo anayamba kubereka ana. 18  Zinatero pakuti Yehova anachititsa kuti akazi onse a m’nyumba ya Abimeleki asabereke, chifukwa cha Sara mkazi wa Abulahamu.+

Mawu a M'munsi

Mwina limeneli linali dzina laudindo.