Genesis 32:1-32

32  Nayenso Yakobo ananyamuka, koma ali m’njira, angelo a Mulungu anakumana naye.+  Yakobo atangowaona, anati: “Ilitu ndi gulu la Mulungu!”+ Chotero malowo anawatcha kuti Mahanaimu.*+  Kenako Yakobo anatsogoza amithenga+ ake powatumiza kwa Esau m’bale wake, kudziko la Seiri,+ kudera la Edomu.+  Anawalamula kuti: “Mukafika kwa mbuyanga+ Esau, mukanene kuti, ‘Kapolo wanu Yakobo wanena kuti: “Ndinali kukhala ndi Labani monga mlendo, ndipo ndakhala kumeneko nthawi yaitali mpaka leroli.+  Tsopano ndili ndi ng’ombe, abulu, nkhosa, komanso antchito aamuna ndi aakazi.+ Ndatumiza amithenga kwa mbuyanga kukupemphani kuti mundikomere mtima.”’”+  Amithengawo atabwerako, anauza Yakobo kuti: “Tinakafika kwa m’bale wanu Esau, ndipo iyenso ali m’njira kudzakumana nanu. Akubwera limodzi ndi amuna 400.”+  Atamva zimenezi, Yakobo anachita mantha ndi kuda nkhawa kwambiri.+ Chotero anagawa anthu amene anali nawo m’magulu awiri, kuphatikizapo nkhosa, mbuzi, ng’ombe ndi ngamila.+  Kenako anati: “Ngati Esau angafikire gulu limodzi kuti alithire nkhondo, gulu linalo lingathe kuthawa.”+  Atatero, Yakobo anati: “Mulungu wa kholo langa Abulahamu, Mulungu wa bambo anga Isaki,+ inu Yehova munandiuza kuti, ‘Bwerera kudziko lakwanu, kwa abale ako, ndipo ndidzakusamalira.’+ 10  Ine ndine wosayenerera kukoma mtima kosatha ndi kukhulupirika konseku, kumene mwandionetsa ine mtumiki wanu.+ Ndinawoloka Yorodano ndilibe kanthu, koma ndodo yokha, ndipo tsopano ndili ndi magulu awiriwa.+ 11  Ndapota nanu, ndipulumutseni+ ku dzanja la m’bale wanga, dzanja la Esau. Ndikuchita naye mantha kuti akafika, ndithu angavulaze ineyo,+ akaziwa pamodzi ndi anawa. 12  Inuyotu munanena kuti, ‘Mosakayikira m’pang’ono pomwe ndidzakusamalira, ndipo ndidzachulukitsa mbewu yako ngati mchenga wa kunyanja, umene suwerengeka kuchuluka kwake.’”+ 13  Tsiku limeneli Yakobo anagona pamalopo. Kenako pa chuma chake anapatulapo zinthu zoti akapatse m’bale wake Esau ngati mphatso.+ 14  Anapatula mbuzi zazikazi 200 ndi mbuzi zamphongo 20, nkhosa zazikazi 200 ndi zamphongo 20. 15  Anapatulanso ngamila zoyamwitsa 30 ndi ana ake, ng’ombe zazikazi 40 ndi nkhuzi 10, abulu aakazi 20 ndi amphongo 10.+ 16  Atatero anapatsa anyamata ake magulu a ziwetozo, gulu lililonse palokha. Kenako anawalangiza mobwerezabwereza kuti: “Tsogolani muwoloke mtsinje, ndipo muzisiya mpata pakati pa gulu lililonse la ziweto.”+ 17  Ndiyeno analangiza mnyamata woyamba kuti: “Ngati angakumane nawe Esau m’bale wanga n’kukufunsa kuti, ‘Kodi mbuyako ndani? Ndipo ukupita kuti? Nanga ziweto zimene ukukusazi n’zandani?’ 18  Ukayankhe kuti, ‘Mbuyanga ndi Yakobo kapolo wanu. Ziwetozi ndi mphatso+ imene iye watumiza kwa inu mbuyanga+ Esau. Iyeyo ali m’mbuyo mwathumu.’” 19  Analamulanso mnyamata wachiwiri ndi wachitatu, komanso ena onse amene anawagawira ziwetozo kuti atsogole nazo, kuti: “Zimene ndanenazi mukalankhule kwa Esau pokumana naye.+ 20  Mukamuuzenso kuti, ‘Ndiponso kapolo wanu Yakobo ali m’mbuyo mwathumu.’”+ Popeza mumtima mwake anati: “Mwina ndingamusangalatse potsogoza mphatsoyi,+ ndipo pambuyo pake ndingathe kuonana naye pamasom’pamaso, kuti mwina angandilandire bwino.”+ 21  Choncho mphatsoyo inatsogola ndipo anawoloka nayo. Koma usikuwo, iye anagona pamsasapo.+ 22  Usiku umenewo, iye anadzuka n’kutenga akazi ake awiri aja,+ akapolo ake awiri,+ ndi ana ake aamuna 11,+ n’kuwoloka powolokera mtsinje wa Yaboki.+ 23  Atawawolotsera kutsidya kwa chigwacho,*+ anawolotsanso zonse zimene anali nazo. 24  Potsirizira pake, Yakobo anatsala yekhayekha. Kenako, munthu winawake anayamba kulimbana naye usiku wonse mpaka m’bandakucha.+ 25  Munthuyo ataona kuti Yakobo sakugonja,+ anamugwira nsukunyu* yake, ndipo nsukunyuyo inaguluka polimbana naye.+ 26  Atatero anauza Yakobo kuti: “Ndileke ndizipita, chifukwa kukucha tsopano.” Koma Yakobo anayankha kuti: “Sindikuleka, kufikira utandidalitsa choyamba.”+ 27  Ndiyeno munthuyo anamufunsa kuti: “Dzina lako ndani?” Iye anayankha kuti, “Yakobo.” 28  Kenako munthuyo anati: “Dzina lako silikhalanso Yakobo, koma Isiraeli,*+ pakuti walimbana+ ndi Mulungu ndi anthu, ndipo potsirizira pake wapambana.” 29  Nayenso Yakobo anafunsa kuti: “Nawenso ndiuze dzina lako.” Koma iye anati: “Ukufunsiranji dzina langa?”+ Atatero, anamudalitsa pamalo amenewo. 30  Chotero Yakobo anatcha malowo Penieli,*+ chifukwa iye anati, “Ndaonana ndi Mulungu pamasom’pamaso, komabe ndapulumuka.”+ 31  Dzuwa linali litatuluka pamene Yakobo anali kuchoka pa Penueli, koma anali kuyenda chotsimphina.+ 32  Pa chifukwa chimenechi, ana a Isiraeli sadya mnyewa wa pansukunyu kufikira lero, chifukwa ndi umene munthu uja anagwira pogulula nsukunyu ya Yakobo.+

Mawu a M'munsi

Dzina lakuti “Mahanaimu” limatanthauza “Magulu Awiri.”
Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.
“Nsukunyu” ndi mfundo ya chiuno, pamene fupa la ntchafu limalumikizana ndi chiuno.
Dzina lakuti “Isiraeli” limatanthauza kuti “Mulungu Walimbana Naye,” ndiponso kuti “Walimbana ndi Mulungu.”
Dzina lakuti “Penieli” limatanthauza “Nkhope ya Mulungu.”