Genesis 14:1-24
14 Tsopano m’masiku a Amarafele mfumu ya ku Sinara,+ Arioki mfumu ya ku Elasara, Kedorelaomere+ mfumu ya ku Elamu,+ ndi Tidala mfumu ya ku Goimu,+
2 mafumuwa anachita nkhondo ndi mafumu otsatirawa: Bera mfumu ya ku Sodomu,+ Birisa mfumu ya ku Gomora,+ Sinabi mfumu ya ku Adima,+ Semebere mfumu ya ku Zeboyimu,+ ndi mfumu ya ku Bela (kapena kuti ku Zowari).+
3 Onsewa anagwirizana+ ndi kutsetserekera limodzi kuchigwa cha Sidimu,+ ku Nyanja Yamchere.+
4 Iwowa, anatumikira Kedorelaomere kwa zaka 12, koma m’chaka cha 13 anamupandukira.
5 M’chaka cha 14, Kedorelaomere anabwera limodzi ndi mafumu omwe anali naye. Iwo anagonjetsa Arefai ku Asiteroti-karanaimu,+ Azuzi ku Hamu, Aemi+ ku Save-kiriyataimu,
6 ndi Ahori+ kuphiri lawo la Seiri,+ mpaka kukafika ku Eli-parana,+ kuchipululu.
7 Kenako anatembenuka n’kulowera ku Eni-misipati, kumene ndi ku Kadesi,+ ndipo anagonjetsa dera lonse la Aamaleki,+ ndiponso Aamori+ omwe anali kukhala ku Hazazoni-tamara.+
8 Pa nthawi imeneyi, mfumu ya ku Sodomu, mfumu ya ku Gomora, mfumu ya ku Adima, mfumu ya ku Zeboyimu, ndi mfumu ya ku Bela (kapena kuti ku Zowari), ananyamuka n’kutsetserekera kuchigwa cha Sidimu.+ Kumeneko, iwo anafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo kuti amenyane ndi
9 Kedorelaomere mfumu ya ku Elamu, Tidala mfumu ya ku Goimu, Amarafele mfumu ya ku Sinara, ndi Arioki mfumu ya ku Elasara.+ Panali mafumu anayi amene analimbana ndi mafumu asanu.
10 Kenako, mafumu a Sodomu ndi Gomora+ anayamba kuthawa. Koma chigwa cha Sidimu+ chinali ndi maenje aphula+ ambirimbiri, choncho iwo pothawa anali kugwera m’maenje amenewo. Amene anatsala anathawira kudera lamapiri.+
11 Ndiyeno, ogonjetsawo anafunkha katundu yense wa ku Sodomu ndi Gomora, limodzi ndi chakudya chonse, n’kumapita.+
12 Anatenganso Loti mwana wa m’bale wake wa Abulamu, ndi katundu wake, n’kupitiriza ulendo wawo. Pa nthawiyo n’kuti Loti akukhala ku Sodomu.+
13 Pambuyo pake, munthu wina amene anathawa anafika kwa Abulamu Mheberi.+ Pa nthawiyo n’kuti Abulamu akukhala m’hema wake pakati pa mitengo ikuluikulu. Mitengoyo mwiniwake anali Mamure, yemwe anali Muamori.+ Ameneyu anali m’bale wake wa Esikolo, ndipo analinso m’bale wake wa Aneri.+ Iwowa anapanga ubale ndi Abulamu.
14 Chotero Abulamu anamva kuti m’bale wake wagwidwa+ ndipo akupita naye kudziko lina. Atamva zimenezo iye anasonkhanitsa anyamata ake odziwa kumenya nkhondo.+ Anali akapolo ake okwanira 318, obadwira m’nyumba yake.+ Iwo analondola oukirawo mpaka ku Dani.+
15 Usiku iye anagawa m’magulu asilikali akewo,+ omwe anali akapolo ake, kuti amenyane ndi adaniwo. Ndipo anawagonjetsa, moti anawapitikitsa mpaka ku Hoba, kumpoto kwa Damasiko.
16 Atatero anapulumutsa katundu wawo yense.+ Anapulumutsanso Loti m’bale wake, katundu wake, akazi, ndi anthu ena.+
17 Ndiyeno, mfumu ya ku Sodomu inapita kuchigwa cha Save, kapena kuti chigwa cha mfumu.+ Inapita kukakumana ndi Abulamu, pamene anali kubwera kuchokera kumene anakagonjetsa Kedorelaomere, limodzi ndi mafumu amene anali naye.
18 Ndipo Melekizedeki,+ mfumu ya ku Salemu,+ anabweretsa mkate ndi vinyo.+ Iyeyu anali wansembe wa Mulungu Wam’mwambamwamba.+
19 Kenako anadalitsa Abulamu kuti:
“Mulungu Wam’mwambamwamba adalitse Abulamu,+Iye amene anapanga kumwamba ndi dziko lapansi.+
20 Ndipo adalitsike Mulungu Wam’mwambamwamba,+Amene wapereka okupondereza m’manja mwako!”+
Pamenepo, Abulamu anamupatsa iye chakhumi cha zilizonse.+
21 Kenako mfumu ya ku Sodomu inauza Abulamu kuti: “Mungondipatsako anthu okhawo,+ koma katunduyo mutenge.”
22 Koma Abulamu anauza mfumu ya ku Sodomuyo kuti: “Ndikukweza manja anga kulumbira+ kwa Yehova Mulungu Wam’mwambamwamba, Amene anapanga kumwamba ndi dziko lapansi.
23 Ndikulumbira kuti pa zinthu zako sinditengapo kanthu n’kamodzi komwe,+ kaya kakhale kaulusi kapena kachingwe komangira nsapato. Ayi sinditero, kuti usadzati, ‘Ndine ndinamulemeretsa Abulamu.’
24 Ineyo sinditengapo chilichonse ayi,+ koma zokhazo zimene anyamata anadya, komanso zogawira anyamata amene anapita nane. Amenewo ndi Aneri, Esikolo ndi Mamure.+ Aliyense atenge gawo lake.”+