Genesis 12:1-20

12  Tsopano Yehova anauza Abulamu kuti: “Tuluka m’dziko lako, pakati pa abale ako, ndi kusiya nyumba ya bambo ako. Upite kudziko limene ndidzakusonyeza.+  Ine ndidzatulutsa mtundu waukulu mwa iwe. Ndidzakudalitsa ndi kukuza dzina lako, ndipo iwe ukhale dalitso+ kwa ena.  Odalitsa iwe ndidzawadalitsa, ndipo otemberera iwe ndidzawatemberera.+ Mabanja onse a padziko lapansi adzapeza madalitso* chifukwa cha iwe.”+  Pamenepo, Abulamu ananyamuka malinga ndi mmene Yehova anamuuzira, ndipo Loti ananyamuka naye limodzi. Pochoka ku Harana,+ Abulamu anali ndi zaka 75.  Iye anatenga mkazi wake Sarai,+ Loti mwana wa m’bale wake,+ ndi chuma chawo chonse,+ komanso akapolo awo onse amene anapeza kudziko la Harana. Iwo ananyamuka ulendo wopita kudziko la Kanani.+ Potsirizira pake anafika ku Kanani.  Tsopano Abulamu anayenda m’dzikomo mpaka kukafika ku Sekemu,+ pafupi ndi mitengo ikuluikulu ya More.+ Pa nthawiyo n’kuti m’dzikomo muli Akanani.  Ndiyeno Yehova anaonekera kwa Abulamu n’kumuuza kuti: “Ndidzapereka dziko ili+ kwa mbewu yako.”+ Pambuyo pake, iye anamanga pamalopo guwa lansembe la Yehova, yemwe anaonekera kwa iye.  M’kupita kwa nthawi, anasamuka pamalopo n’kupita kudera lamapiri, kum’mawa kwa Beteli.+ Kumeneko iye anamanga hema wake. Beteli anali kumadzulo kwake ndipo Ai+ anali kum’mawa kwake. Kenako anamangira Yehova guwa lansembe,+ n’kuyamba kuitana pa dzina la Yehova.+  Pambuyo pake, Abulamu anasamutsa hema wake kumeneko. Kuyambira pa nthawi imeneyi, iye ankangokhalira kumanga ndi kusamutsa msasa, kulowera ku Negebu.+ 10  Tsopano m’dzikomo munagwa njala, ndipo Abulamu ananyamuka kulowera ku Iguputo kukakhala kumeneko monga mlendo.+ Anatero chifukwa njalayo inafika poipa kwambiri m’dzikomo.+ 11  Ali pafupi kulowa mu Iguputo, anauza mkazi wake Sarai kuti: “Ndikudziwa ndithu kuti ndiwe mkazi wokongola m’maonekedwe ako.+ 12  Aiguputo akakuona, mosakayikira anena kuti, ‘Ameneyu ndi mkazi wake.’ Ndipo andipha ndithu, koma iweyo akusiya wamoyo. 13  Ndiye chonde, unene kuti ndiwe mlongo wanga+ kuti zindiyendere bwino. Ukatero upulumutsa moyo wanga.”+ 14  Choncho zinachitikadi kuti, Abulamu atangolowa mu Iguputo, Aiguputo anaona kuti mkaziyo anali wokongola kwambiri. 15  Nawonso akalonga a Farao anamuona, ndipo anayamba kum’tamanda kwa Farao, moti anatenga mkaziyo n’kupita naye kunyumba kwa Farao. 16  Farao anamusamalira bwino Abulamu chifukwa cha mkazi wake, moti anamupatsa nkhosa, ng’ombe ndi abulu. Anamupatsanso antchito aamuna ndi aakazi, komanso abulu aakazi ndi ngamila.+ 17  Ndiyeno, Yehova anagwetsera Farao ndi banja lake miliri yoopsa+ chifukwa cha Sarai, mkazi wa Abulamu.+ 18  Farao ataona zimenezi anaitana Abulamu, n’kumufunsa kuti: “N’chiyani wandichitachi? N’chifukwa chiyani sunandiuze kuti ndi mkazi wako?+ 19  N’chifukwa chiyani unanena kuti, ‘Ndi mlongo wanga,’+ moti ndinatsala pang’ono kumutenga kukhala mkazi wanga? Nayu tsopano mkazi wako. Mutenge uzipita!” 20  Pamenepo Farao analamula anyamata ake kuti aperekeze Abulamu ndi mkazi wake, limodzi ndi zonse zimene anali nazo.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “adzadzidalitsa okha,” kusonyeza kuti akufunika kuchitapo kanthu kuti apeze madalitsowo.