Genesis 21:1-34

21  Tsopano Yehova anakumbukira Sara monga mwa mawu ake, ndipo Yehovayo anachitira Sara monga momwe ananenera.+  Choncho Sara anakhala ndi pakati+ n’kuberekera Abulahamu mwana, Abulahamuyo atakalamba. Izi zinachitika pa nthawi yoikidwiratu imene Mulungu analonjeza Abulahamu.+  Chotero Abulahamu anatcha mwana amene Sara anamuberekerayo dzina lakuti Isaki.+  Isaki atakwanitsa masiku 8, Abulahamu anamudula mwana wakeyo, monga mmene Mulungu anamulamulira.+  Abulahamu anali ndi zaka 100 pamene mwana wake Isaki anabadwa.  Ndiyeno Sara anati: “Mulungu wandipatsa chifukwa chosangalalira. Tsopano aliyense akamva zimenezi asangalala nane.”*+  Anapitiriza kunena kuti: “Akanadziwa ndani kuti Sara adzayamwitsa mwana, moti n’kumuuza Abulahamu zimenezo? Koma taonani, ndamuberekera mwana Abulahamu atakalamba.”  Tsopano mwanayo anakula n’kumusiyitsa kuyamwa.+ Pa tsiku limene anamusiyitsa kuyamwalo, Abulahamu anakonza phwando lalikulu.  Kenako Sara anakhala akuona mwana amene Hagara Mwiguputo+ anaberekera Abulahamu akuseka Isaki.+ 10  Chotero Sara anayamba kuuza Abulahamu kuti: “Thamangitsani kapolo wamkaziyu pamodzi ndi mwana wakeyu pano, chifukwa mwana wa kapolo ameneyu sadzakhala wolandira cholowa pamodzi ndi mwana wanga Isaki.”+ 11  Abulahamu anaipidwa nazo kwambiri zimenezi chifukwa cha mwana wake.+ 12  Koma Mulungu anauza Abulahamu kuti: “Usaipidwe ndi chilichonse chimene Sara wakhala akunena kwa iwe chokhudza mnyamatayo ndiponso kapolo wakoyo. Mvera mawu ake, chifukwa amene adzatchedwa mbewu yako adzachokera mwa Isaki.+ 13  Kunena za mwana wa mdzakaziyo,+ nayenso ndidzamupangitsa kukhala mtundu, chifukwa iye ndi mbewu yako.”+ 14  Choncho Abulahamu anadzuka m’mawa kwambiri n’kutenga mkate ndi thumba la madzi lachikopa, n’kuziika paphewa pa Hagara.+ Atatero anamuuza kuti azipita limodzi ndi mwana wakeyo.+ Chotero Hagarayo ananyamuka n’kumangoyendayenda m’chipululu cha Beere-seba.*+ 15  Potsirizira pake, madzi anamuthera+ m’thumba lachikopa lija, ndipo iye anangomusiya+ mwana uja pachitsamba. 16  Ndiyeno iye anapita chapatali n’kukakhala pansi payekhayekha pamtunda woti muvi woponya ndi uta ukhoza kufika. Anachita zimenezi chifukwa mumtima mwake anati: “Sindikufuna kuona mwana wanga akamafa.”+ Choncho anakakhala pansi pakatali n’kuyamba kulira mokweza.+ 17  Pamenepo Mulungu anamva mawu a mnyamatayo,+ ndipo mngelo wa Mulungu analankhula ndi Hagara kuchokera kumwamba+ kuti: “Kodi watani Hagara? Usaope, Mulungu wamva mawu a mnyamatayo pomwe wagonapo. 18  Nyamuka! Dzutsa mnyamatayo, ndipo umugwirizize ndi dzanja lako, chifukwa ndidzamupangitsa kukhala mtundu waukulu.”+ 19  Ndiyeno Mulungu anamutsegula maso Hagara, moti anaona chitsime cha madzi.+ Chotero iye anapita pachitsimecho n’kutungira madziwo m’thumba lachikopa lija, n’kumupatsa mnyamatayo kuti amwe. 20  Mulungu anakhalabe ndi Isimaeli.+ Mnyamata ameneyu anali kukhala m’chipululu, ndipo anakula n’kukhala katswiri woponya muvi ndi uta.+ 21  Iye anakhalabe m’chipululu cha Parana,+ ndipo amayi ake anakamutengera mkazi kudziko la Iguputo. 22  Ndiyeno pa nthawi imeneyo, Abimeleki limodzi ndi Fikolo mkulu wa gulu lake lankhondo anauza Abulahamu kuti: “Mulungu ali ndi iwe pa zonse zomwe ukuchita.+ 23  Chotero lumbira panopo kuti, pali Mulungu+ udzakhala wokhulupirika kwa ine, kwa ana anga ndi kwa mbadwa zanga.+ Ndiponso kuti udzatero chifukwa cha chikondi chosatha+ chimene ine ndakusonyeza. Choncho udzandichitira ine motero, pamodzi ndi dziko limene ukukhalamo monga mlendoli.”+ 24  Abulahamu anayankha kuti: “Ndikulumbira.”+ 25  Pamene Abulahamu anadzudzula kwambiri Abimeleki chifukwa cha chitsime cha madzi chimene antchito a Abimeleki analanda mwachiwawa,+ 26  Abimeleki anayankha kuti: “Sindikudziwa amene anachita zimenezi, ndipo ngakhale iwe sunandiuze. Inetu sindinamve za nkhani imeneyi, moti ndikuimvera pompano.”+ 27  Ndiyeno Abulahamu anatenga nkhosa ndi ng’ombe n’kuzipereka kwa Abimeleki.+ Kenako awiriwo anachita pangano.+ 28  Abulahamu atapatula ana a nkhosa aakazi 7 pa gululo n’kuwaika pa okha, 29  Abimeleki anafunsa Abulahamu kuti: “Kodi ana a nkhosa aakazi 7 amene wapatulawa, tanthauzo lake n’chiyani?” 30  Poyankha Abulahamu anati: “Landirani ana a nkhosa aakazi 7 amene ndikukupatsaniwa, kuti akhale umboni+ wakuti ndinakumba chitsimechi ndine.” 31  Ndiye chifukwa chake iye anatcha malowo Beere-seba,+ chifukwa chakuti onse awiri analumbirirana pamalopo. 32  Choncho iwo anachita panganolo+ pa Beere-sebapo, kenako Abimeleki limodzi ndi Fikolo mkulu wa asilikali ake, anabwerera kudziko la Afilisiti.+ 33  Zitatero, Abulahamu anabzala mtengo wa bwemba pa Beere-seba, n’kuitanirapo dzina la Yehova,+ Mulungu wanthawi zonse.+ 34  Ndipo Abulahamu anakhala masiku enanso ambiri monga mlendo m’dziko la Afilisiti.+

Mawu a M'munsi

Mawu achiheberi amene m’vesili tawamasulira kuti “chisangalalo” ndiponso kuti “asangalala,” amatanthauza “kuseka.”
Dzina lakuti “Beere-seba” limatanthauza “Chitsime cha Lumbiro” kapena, “Chitsime cha 7.”