Genesis 42:1-38

42  Tsopano Yakobo anamva kuti ku Iguputo kuli tirigu,+ ndipo anafunsa ana ake kuti: “Kodi muzingoyang’anana?”  Anapitiriza kuti: “Ine ndamva kuti ku Iguputo kuli tirigu.+ Pitani kumeneko mukatigulire tirigu kuti tikhalebe ndi moyo, tingafe ndi njala.”  Choncho abale ake a Yosefe 10+ ananyamuka kuti akagule tirigu ku Iguputo.  Koma Yakobo sanalole kuti Benjamini,+ m’bale wake wa Yosefe, apite limodzi ndi abale akewo, chifukwa anati: “Mwina angakumane ndi tsoka n’kufa.”+  Ndiyeno ana a Isiraeliyo anafika ku Iguputo limodzi ndi anthu ena okagula tirigu, chifukwa m’dziko la Kanani munali njala.+  Tsopano Yosefe ndiye anali wolamulira m’dzikomo.+ Iye ndiye anali kugulitsa tirigu kwa anthu onse ochokera kumayiko ena onse.+ Choncho abale a Yosefe anafika kwa iye. Anamugwadira n’kumuweramira mpaka nkhope zawo pansi.+  Yosefe atawaona abale akewo, anawazindikira nthawi yomweyo, koma anadzisintha kuti asam’dziwe.+ Chotero analankhula nawo mwaukali n’kuwafunsa kuti: “Mwachokera kuti?” Iwo anayankha kuti: “Tachokera kudziko la Kanani, ndipo tabwera kuno kudzagula chakudya.”+  Ngakhale kuti Yosefe anawazindikira abale akewo, iwo sanam’zindikire.  Nthawi yomweyo Yosefe anakumbukira maloto ake aja onena za abale akewo.+ Pamenepo anawauza kuti: “Inu ndinu akazitape! Ndithu mwabwera kuno kudzafufuza malo amene dziko lathu lili lofooka!”+ 10  Koma iwo anakana kuti: “Ayi mbuyathu,+ akapolo anufe+ tabwera kudzagula chakudya. 11  Tonsefe ndife ana a munthu mmodzi, ndipo ndife anthu achilungamo. Akapolo anufe sitichita zaukazitape ayi.”+ 12  Koma iye anawauza kuti: “Mukunama! Mwabwera kuno kudzafufuza malo ofooka a dziko lathu.”+ 13  Pamenepo iwo anati: “Akapolo anufe tilipo 12 pa ubale wathu.+ Ndife ana a munthu mmodzi amene akukhala ku Kanani.+ Wamng’ono kwambiri watsala ndi bambo athu,+ koma winayo kulibenso.”+ 14  Komabe Yosefe anawauza kuti: “Pajatu ndanena kale kuti, ‘Anthu inu ndinu akazitape!’ 15  Chabwino, ndikuyesani motere kuti ndione ngati mukunena zoona: Simuchoka kuno mpaka mng’ono wanuyo atabwera,+ ndithu pali Farao wamoyo! 16  Tumani mmodzi pakati panu apite akatenge mng’ono wanuyo. Enanu ndikutsekerani m’ndende. Ndikufuna ndione ngati zimene mukunena zili zoona.+ Ndipo ngati si zoona, pali Farao wamoyo, ndiye kuti ndinu akazitape basi.” 17  Atatero, anawatsekera pamodzi m’ndende masiku atatu. 18  Pa tsiku lachitatu, Yosefe anawauza kuti: “Popeza ine ndimaopa+ Mulungu woona, chitani izi kuti mukhale ndi moyo: 19  Ngati mulidi achilungamo, mmodzi wa inu atsale m’ndendemu.+ Ena nonsenu pitani, mukapereke tirigu kunyumba zanu chifukwa kuli njala.+ 20  Ndiyeno mukabweretse mng’ono wanuyo kwa ine. Mukatero, ndidzatsimikiza kuti mukunena zoona, ndipo simudzaphedwa.”+ Iwo anavomereza kuchita zimenezo. 21  Kenako iwo anayamba kulankhulana kuti: “Ndithudi, izi zikuchitika chifukwa cha zimene tinachitira m’bale wathu uja.+ Pajatu tinaona kusautsika kwake pamene anatichonderera kuti timumvere chisoni, koma ife sitinalabadire. N’chifukwa chake tsokali latigwera.”+ 22  Ndiyeno Rubeni anayankhira kuti: “Kodi ine sindinanene kuti, ‘Mwanayu musam’chite choipa’? Koma inu simunamve.+ Si izi nanga, magazi ake akufunidwatu kwa ife.”+ 23  Iwo sanadziwe kuti Yosefe anali kumva zimene amanena, chifukwa anali kulankhula nawo kudzera mwa womasulira. 24  Ndiyeno Yosefe anapita payekha kukalira.+ Kenako anabwerako n’kuyambiranso kulankhula nawo, ndipo anatenga Simiyoni+ n’kumumanga iwo akuona.+ 25  Yosefe atatero, analamula anyamata ake kuti awadzazire tirigu m’matumba awo. Anawalamulanso kuti aliyense am’bwezere ndalama zake pomuikira m’thumba lake.+ Anatinso awapatse kamba wa pa ulendo wawo.+ Anyamatawo anawachitiradi zimenezo. 26  Chotero, iwo anasenzetsa abulu awo tiriguyo n’kuyamba ulendo wawo. 27  Atafika pamalo ogona, mmodzi wa iwo anamasula thumba lake kuti atengemo chakudya chopatsa bulu wake.+ Atamasula, anangoona kuti ndalama zake zili pakamwa pa thumbalo.+ 28  Ameneyo anauza abale ake kuti: “Taonani! Ndalama zanga andibwezera, izi zili m’thumbazi!” Pamenepo mitima yawo inangoti myuu! ndipo anayamba kunthunthumira+ n’kuyamba kufunsana kuti: “Kodi Mulungu akutichita chiyani ife?”+ 29  Potsirizira pake, anafika kwa bambo awo Yakobo kudziko la Kanani. Iwo anafotokozera bambo awo zonse zimene zinawagwera kuti: 30  “Nduna yaikulu ya dzikolo inalankhula nafe mwaukali,+ chifukwa inatiyesa akazitape okafufuza dzikolo.+ 31  Koma tinaiuza kuti, ‘Ndife anthu achilungamo,+ sitichita zaukazitape ayi. 32  Ndife ana a bambo mmodzi,+ ndipo tilipo 12 pa ubale wathu.+ Mmodzi kulibenso,+ koma wamng’ono ali ndi bambo athu kudziko la Kanani.’+ 33  Koma munthuyo, yemwe ndi nduna yaikulu ya dzikolo, anatiuza kuti,+ ‘Ngati mulidi achilungamo+ muchite izi: Mmodzi wa inu atsale ndi ine kuno.+ Koma enanu tengani chakudya, mupite nacho kunyumba zanu chifukwa kuli njala.+ 34  Mukabweretse m’bale wanu wamng’onoyo kwa ine kuti ndidzatsimikize kuti si inu akazitape koma anthu achilungamo. Mukadzatero, ndidzakubwezerani m’bale wanuyu, ndipo mudzatha kuchita malonda m’dziko lino.’”+ 35  Tsopano pamene anali kukhuthula matumba awo, aliyense anapeza mpukutu wa ndalama zake m’thumba lake. Ataziona ndalamazo limodzi ndi bambo awo, onse anachita mantha. 36  Pamenepo Yakobo bambo wawo anadandaula kuti: “Inetu mwandisandutsa namfedwa!+ Yosefe anapita, Simiyoni kulibenso.+ Tsopano mukufuna kutenga Benjamini! Masoka onsewa akugwera ine!” 37  Koma Rubeni anauza bambo ake kuti: “Ndikapanda kudzam’bwezera kwa inu Benjamini, mudzaphe ana anga awiri.+ Mum’pereke m’manja mwanga, ndipo ineyo ndi amene ndidzam’bwezere kwa inu.”+ 38  Komabe bambo awo anati: “Zoti mwana wanga apite nanu, izo ndakana, chifukwa m’bale wake anafa, ndipo iye anatsala yekha.+ Ngati angakumane ndi tsoka n’kufa panjira, ndithu mudzatsitsira ku Manda+ imvi zanga ndi chisoni.”

Mawu a M'munsi