Genesis 19:1-38
19 Tsopano angelo awiri aja anafika ku Sodomu madzulo. Loti anali atakhala pachipata cha Sodomu.+ Atawaona ananyamuka kukakumana nawo, ndipo anawagwadira n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi.+
2 Ndiyeno anati: “Chonde ambuyanga, patukirani kunyumba ya kapolo wanu. Tikusambitseni mapazi ndiponso mukagone,+ kuti mawa mulawirire n’kupitiriza ulendo wanu.”+ Ndiyeno iwo anati: “Ayi, ife tigona m’bwalo la mzinda usiku wa lero.”+
3 Koma Loti anawaumiriza kwambiri+ moti mpaka iwo anapita naye kunyumba kwake. Kumeneko anawakonzera phwando,+ n’kuwaphikira mikate yopanda chofufumitsa,+ ndipo anadya.
4 Koma iwo asanagone, amuna a mumzindamo, amuna a mu Sodomu, anafika n’kuzungulira nyumbayo.+ Anafika ali chigulu, kuyambira tianyamata mpaka nkhalamba.+
5 Iwo anali kufuula kwa Loti kuti: “Kodi amuna amene abwera usiku uno aja, ali kuti? Atulutse kuti tigone nawo.”+
6 Pamenepo Loti anatuluka pakhomo kuti alankhule nawo, n’kutseka chitseko kumbuyo kwake.
7 Ndiyeno iye anati: “Chonde abale anga, musachite zoipazi.+
8 Paja ine ndili ndi ana aakazi awiri amene sanagonepo ndi mwamuna.+ Bwanji ndikutulutsireni amenewo kuti muchite nawo zimene mukufuna.+ Koma amuna okhawa musawachite chilichonse ayi,+ chifukwa abwera m’nyumba* mwanga kuti adzatetezedwe.”+
9 Pamenepo iwo anati: “Choka apa!” Ananenanso kuti: “Uyu ndi wobwera kwathu kuno, ndipo akukhala monga mlendo.+ Ndiye lero azitiuza zochita?+ Tsopano iweyo tikuchita zoopsa kuposa iwowo.” Atatero iwo anamukhamukira Lotiyo ndi kumupanikiza,+ moti anatsala pang’ono kuthyola chitseko.+
10 Pamenepo alendo aja anatulutsa manja n’kukokera Loti m’nyumbamo, n’kutseka chitseko.
11 Koma anachititsa khungu amuna amene anali pakhomo la nyumbawo,+ kuyambira wamng’ono kwambiri mpaka wamkulu koposa,+ moti anthuwo anavutika kufufuza khomo.+
12 Ndiyeno alendowo anafunsa Loti kuti: “Kodi uli ndi achibale alionse kuno? Uwatulutse mumzinda uno,+ kaya ndi akamwini ako, ana ako aamuna, ana ako aakazi, kapena alionse amene ndi abale ako.
13 Malo ano tiwawononga chifukwa kudandaula kokhumudwa ndi anthuwa kwamveka kwambiri kwa Yehova,+ moti Yehova watituma kudzawononga mzindawu.”+
14 Pamenepo Loti anatuluka n’kupita kukalankhula ndi akamwini ake omwe anali kudzakwatira ana ake. Iye anawauza mobwerezabwereza kuti: “Fulumirani! Tulukani mumzinda uno, chifukwa Yehova auwononga.”+ Koma akamwini akewo anangomuona ngati akunena zocheza.+
15 Komabe, m’kachizirezire ka m’bandakucha, angelowo anayamba kum’fulumiza Loti, kuti: “Fulumira! Tenga mkazi wako ndi ana ako aakazi awiriwa,+ kuti musawonongedwere limodzi ndi mzindawu chifukwa cha kulakwa kwake.”+
16 Pamene iye anali kuzengereza,+ alendowo, mwa chifundo cha Yehova pa iye,+ anagwira dzanja iyeyo, mkazi wake, ndi ana ake aakazi awiriwo, n’kuwatulutsa kukawasiya kunja kwa mzinda.+
17 Atafika nawo kunja kwa mzinda, mmodzi wa iwo anati: “Thawani mupulumutse moyo wanu!+ Musacheukire kumbuyo+ ndipo musaime chilili pamalo alionse m’Chigawochi.*+ Thawirani kudera la kumapiri kuti musawonongedwe!”+
18 Koma Loti anawauza kuti: “Chonde Yehova, kumeneko ayi!
19 Mwamukomera kale mtima mtumiki wanu,+ ndipo mwaonetsa kukoma mtima kwanu kosatha+ kuti mupulumutse moyo wanga.+ Koma chonde, sinditha kuthawira kudera la kumapiri chifukwa tsoka lingakandipeze kumeneko, ndipo ndingakafe ndithu.+
20 Chonde taonani pali mzinda waung’ono+ pafupipa umene ndingathawireko. Zimene ndikukupemphanizi si nkhani yaing’ono kodi? Chonde ndiloleni ndithawire kumzinda umenewo. Ndikatero, moyo wanga upulumuka.”+
21 Pamenepo iye anamuyankha Loti kuti: “Chabwino, ndavomera zimene wapempha.+ Sindiwononga mzinda umene wanenawo.+
22 Tiye, fulumira! Thawira kumeneko, ndipo sindichita kanthu mpaka utafika kumeneko.”+ N’chifukwa chake iye anatcha mzindawo dzina lakuti Zowari.*+
23 Pamene Loti ankafika ku Zowari n’kuti dzuwa litakwera.+
24 Ndiyeno Yehova anavumbitsa sulufule ndi moto kuchokera kwa Yehova kumwamba, kuvumbira pa Sodomu ndi Gomora.+
25 Iye anawononga mizindayi, ngakhale Chigawo chonsecho ndi anthu onse a m’mizindayi, kuphatikizapo zomera za panthaka.+
26 Kenako, mkazi wake amene anali kumbuyo kwake anacheukira kumbuyo, ndipo anasanduka chipilala chamchere.+
27 Tsopano Abulahamu ananyamuka m’mawa kwambiri kupita pamalo pamene anaimirira pamaso pa Yehova paja.+
28 Ndiyeno anayang’ana kumunsi ku Sodomu ndi Gomora ndi kudera lonse la Chigawocho, ndipo anaona zoopsa. Kumeneko chiutsi chinali tolo! Chinali kufuka ngati chiutsi chochokera pa uvuni wa njerwa.+
29 Choncho pamene Mulungu anawononga mizinda ya m’Chigawocho, anakumbukira Abulahamu. Anatero mwa kupulumutsa Loti ku chiwonongeko pamene ankawononga mizinda imene Loti anali kukhalako.+
30 Pambuyo pake Loti anachoka ku Zowari n’kukakhala kudera la kumapiri, iye limodzi ndi ana ake aakazi awiri aja,+ chifukwa anachita mantha kukhala ku Zowari.+ Kumeneko, iye ndi ana ake awiriwo anayamba kukhala m’phanga.
31 Ndiyeno mwana woyamba kubadwa anauza mng’ono wake kuti: “Bambo athuwa akalamba tsopano, ndipo kudziko kuno kulibe mwamuna woti angagone nafe monga mmene anthu amachitira padziko lonse lapansi.+
32 Tiye tiwapatse vinyo bambo kuti amwe,+ ndipo tigone nawo kuti tisunge mbewu kuchokera kwa iwo.”+
33 Chotero usiku umenewo iwo anakhala akupatsa vinyo bambo awo kuti azimwa.+ Kenako, mwana woyamba kubadwayo anapita n’kukagona ndi bambo akewo. Koma kuyambira pamene mwanayo anabwera kudzagona nawo mpaka pamene anachoka, bambowo sanadziwe chilichonse.
34 Ndipo tsiku lotsatira, mwana woyambayo anauza mng’ono wake kuti: “Ndagona nawo bambo usiku. Usiku wa leronso tiwapatse vinyo kuti amwe. Ndiye iwenso upite ukagone nawo, kuti tisunge mbewu kuchokera kwa iwo.”
35 Chotero, usiku uwunso anakhala akuwapatsa vinyo bambo awo kuti azimwa. Kenako, mwana wamng’ono uja anapita n’kukagona nawo. Koma kuyambira pamene mwanayo anabwera kudzagona nawo mpaka pamene anachoka, bambowo sanadziwe chilichonse.
36 Ndipo ana a Loti awiri onsewo anatenga pakati pa bambo awo.+
37 M’kupita kwa nthawi, mwana woyambayo anabereka mwana wamwamuna n’kumutcha dzina lakuti Mowabu.+ Iye ndiye tate wa Amowabu mpaka lero.+
38 Nayenso mwana wamng’onoyo anabereka mwana wamwamuna, n’kumutcha dzina lakuti Beni-ami. Iye ndiye tate wa ana a Amoni+ mpaka lero.
Mawu a M'munsi
^ Mawu ake enieni, “pansi pa mthunzi wa denga langa.”
^ Dzina lakuti “Zowari” limatanthauza “Kuchepa.”