Genesis 46:1-34

46  Choncho Isiraeli ndi onse a m’nyumba yake ananyamuka kupita ku Beere-seba.+ Kumeneko iye anapereka nsembe kwa Mulungu wa bambo ake Isaki.+  Ndiyeno Mulungu analankhula ndi Isiraeli m’masomphenya usiku,+ kuti: “Yakobo, Yakobo!” Ndipo Yakobo anayankha kuti: “Ine pano!”+  Mulungu anapitiriza kuti: “Ine ndine Mulungu woona,+ Mulungu wa bambo ako.+ Usaope kupita ku Iguputo, chifukwa kumeneko ndidzakukuza kukhala mtundu waukulu.+  Ineyo ndipita nawe ku Iguputo, ndiponso ine ndi amene ndidzabwere nawe kuchokera kumeneko.+ Ndipo Yosefe ndi amene adzakutseke maso pa imfa yako.”+  Kenako, Yakobo ananyamuka ku Beere-sebako. Ana a Isiraeliwo anatenga bambo awo, Yakobo, limodzi ndi ana awo aang’ono, ndi akazi awo. Anawatengera m’ngolo zimene Farao anatumiza.+  Anatenganso ziweto zawo zonse ndi katundu wawo yense amene anapeza m’dziko la Kanani.+ Potsirizira pake, Yakobo ndi ana ake onse anafika ku Iguputo.  Anafika limodzi ndi ana ake aamuna ndi aakazi, limodzinso ndi adzukulu ake aamuna ndi aakazi obadwa kwa ana ake aamuna, mbadwa zake zonse.+  Tsopano nawa mayina a ana a Isiraeli, kapena kuti ana a Yakobo, omwe anabwera nawo ku Iguputo:+ Mwana woyamba wa Yakobo anali Rubeni.+  Ndipo ana a Rubeni anali Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karami.+ 10  Ana a Simiyoni+ anali Yemueli, Yamini, Ohadi, Yakini,+ Zohari ndi Shauli+ mwana wa mkazi wachikanani. 11  Ana a Levi+ anali Gerisoni,+ Kohati+ ndi Merari.+ 12  Ana a Yuda+ anali Ere,+ Onani,+ Shela,+ Perezi,+ ndi Zera.+ Komabe, Ere ndi Onani anafera kudziko la Kanani.+ Ana a Perezi anali Hezironi+ ndi Hamuli.+ 13  Ana a Isakara+ anali Tola,+ Puva,+ Yabi ndi Simironi.+ 14  Ana a Zebuloni+ anali Seredi, Eloni ndi Yahaleeli.+ 15  Amenewa ndiwo anali ana a Leya,+ amene anaberekera Yakobo ku Padana-ramu, kuphatikizapo Dina+ mwana wamkazi wa Yakobo. Ana ake onse aamuna ndi aakazi ndi adzukulu ake analipo 33. 16  Ana a Gadi+ anali Zifioni, Hagi, Suni, Eziboni, Eri, Arodi ndi Areli.+ 17  Ana a Aseri+ anali Imuna, Isiva, Isivi ndi Beriya.+ Panalinso mlongo wawo Sera. Ana a Beriya anali Hiberi ndi Malikieli.+ 18  Amenewa ndiwo anali ana a Zilipa,+ yemwe Labani anam’pereka kwa mwana wake wamkazi Leya. Ndiwo ana amene Zilipa anaberekera Yakobo m’kupita kwa nthawi. Onse pamodzi analipo 16. 19  Ana a Rakele,+ mkazi wa Yakobo, anali Yosefe+ ndi Benjamini.+ 20  Yosefe anabereka Manase+ ndi Efuraimu*+ ku Iguputo. Anabereka anawa kwa mkazi wake Asenati+ mwana wa Potifera, yemwe anali wansembe wa mzinda wa Oni. 21  Ana a Benjamini anali Bela,+ Bekeri,+ Asibeli, Gera,+ Namani,+ Ehi, Rosi, Mupimu,+ Hupimu+ ndi Aridi. 22  Amenewa ndiwo ana amene Rakele anaberekera Yakobo. Onse pamodzi analipo 14. 23  Ana a Dani+ anali Husimu.*+ 24  Ana a Nafitali+ anali Yahazeeli, Guni,+ Yezera ndi Silemu.+ 25  Amenewa ndiwo anali ana a Biliha,+ yemwe Labani anam’pereka kwa mwana wake wamkazi Rakele. Awa ndiwo ana amene Biliha anaberekera Yakobo m’kupita kwa nthawi. Onse pamodzi analipo 7. 26  Ana onse a Yakobo otuluka m’chiuno mwake,+ amene anali nawo ku Iguputo, analipo 66 onse pamodzi, osawerengera akazi a ana ake. 27  Ana amene Yosefe anabereka ku Iguputo analipo awiri. Onse a m’nyumba ya Yakobo amene anali nawo ku Iguputo analipo 70.+ 28  Yakobo anatumiza Yuda+ kuti atsogole kupita kwa Yosefe kukam’dziwitsa za kubwera kwa bambo ake ku Goseni. Pambuyo pake iwo anafika ku Goseni.+ 29  Pamenepo Yosefe anakonza galeta lake n’kunyamuka kupita kukakumana ndi Isiraeli bambo ake ku Goseni.+ Atangofika kwa bambo akewo, nthawi yomweyo anawakumbatira n’kulira ndi kugwetsa misozi. Anachita zimenezi mobwerezabwereza.+ 30  Pamapeto pake Isiraeli anauza Yosefe kuti: “Ndingathe kufa+ tsopano chifukwa ndaona nkhope yako, popeza ukadali ndi moyo.” 31  Ndiyeno Yosefe anauza abale ake ndi a m’nyumba ya bambo ake kuti: “Ndipite kwa Farao ndikam’dziwitse.+ Ndikanene kuti, ‘Abale anga ndi a m’nyumba ya bambo anga, amene anali m’dziko la Kanani, abwera kuno kwa ine.+ 32  Anthuwa ndi abusa,+ pakuti amaweta ziweto.+ Abwera ndi nkhosa zawo, ng’ombe, ndi zinthu zawo zonse.’+ 33  Farao akakuitanani n’kukufunsani kuti, ‘Kodi mumagwira ntchito yanji?’ 34  Inu mukayankhe kuti: ‘Akapolo anufe takhala tikuweta ziweto kuyambira tili ana kufikira lero, ifeyo ndi makolo athu omwe.’+ Mukayankhe choncho kuti mukhale ku Goseni,+ chifukwa aliyense woweta nkhosa Aiguputo amanyansidwa naye.”+

Mawu a M'munsi

Pambuyo potchula “Efuraimu,” Baibulo la Septuagint limawonjezera mayina ena asanu, pamene limati: “Koma Manase anali ndi ana ndipo wina anali Makiri, amene mdzakazi wake wa ku Siriya anam’berekera. Ndipo Makiri anabereka Galaadi. Koma ana a Efuraimu, m’bale wake wa Manase, anali Sutalaamu ndi Taamu. Sutalaamu anali ndi ana ndipo wina anali Edemu.” Ichi chingakhale chifukwa chake Baibulo la Septuagint limatchula anthu 75 m’malo mwa 70 pa Ge 46:27 ndi pa Eks 1:5, komanso Sitefano anatchula zomwezi pa Mac 7:14.
Mwina mayina a ana ena sanatchulidwe.