Genesis 17:1-27

17  Pamene Abulamu anali ndi zaka 99, Yehova anaonekera kwa iye n’kumuuza kuti:+ “Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse.+ Yenda pamaso panga ndipo ukhale wolungama.+  Ndidzakhazikitsa pangano langa pakati pa ine ndi iwe,+ pangano lakuti ndidzachulukitsa kwambiri mbadwa zako.”+  Abulamu atamva zimenezi anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi.+ Kenako Mulungu anapitiriza kulankhula naye kuti:  “Ine ndinachita pangano ndi iwe,+ ndipo iwe udzakhaladi tate wa mitundu yambiri.+  Tsopano dzina lako silikhalanso Abulamu, m’malo mwake likhala Abulahamu, chifukwa ndidzakupangitsa kukhala tate wa mitundu yambiri.  Ndidzakupatsa ana ambiri zedi, ndipo mwa iwe mudzatuluka mitundu ndi mafumu.+  “Ndidzakwaniritsa pangano langa la pakati pa ine ndi iwe,+ ndi mbewu yako yobwera pambuyo pa iwe ku mibadwomibadwo. Lidzakhala pangano mpaka kalekale,+ kusonyeza kuti ndine Mulungu wako ndi wa mbewu yako yobwera pambuyo pa iwe.+  Dziko limene ukukhalamo ngati mlendoli,+ ndidzalipereka kwa iwe ndi mbewu yako yobwera pambuyo pako. Dziko lonse la Kanani lidzakhala lawo mpaka kalekale, ndipo ine ndidzakhala Mulungu wawo.”+  Mulungu anapitiriza kumuuza Abulahamu kuti: “Koma iwe usunge pangano langa, iwe ndi mbewu yobwera pambuyo pako ku mibadwo yawo yonse.+ 10  Ili ndi pangano limene anthu inu muyenera kulisunga, la pakati pa ine ndi inu, ngakhalenso mbewu yobwera pambuyo pa inu.+ Mwamuna aliyense pakati pa inu azidulidwa.+ 11  Muzichita mdulidwe kuti ukhale chizindikiro cha pangano la pakati pa ine ndi inu.+ 12  Mwana aliyense wamwamuna amene wakwanitsa masiku 8 azidulidwa+ m’mibadwo yanu yonse. Aliyense wobadwira m’nyumba yanu ndi aliyense wosakhala mbewu yanu koma wogulidwa ndi ndalama kwa mlendo azidulidwa. 13  Mwana aliyense wobadwa m’nyumba mwanu, ndi mwamuna aliyense amene mwamugula ndi ndalama zanu azidulidwa ndithu,+ ndipo pangano langa pathupi panu lidzakhala pangano mpaka kalekale.+ 14  Mwamuna aliyense wosadulidwa amene sadzadulidwa, ameneyo aphedwe kuti asakhalenso pakati pa anthu ake.+ Waphwanya pangano langa.” 15  Ndiyeno Mulungu anauza Abulahamu kuti: “Sarai mkazi wako usamutchulenso kuti Sarai, chifukwa tsopano dzina lake ndi Sara.+ 16  Iye ndidzamudalitsa ndipo iwe ndidzakupatsa mwana wamwamuna wochokera mwa iye.+ Ndidzamudalitsa ndipo adzakhala mayi wa mitundu yambiri ya anthu+ ndi wa mafumu a mitundu yambiri ya anthu.”+ 17  Abulahamu atamva zimenezi anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi, n’kuyamba kuseka mumtima mwake+ kuti: “Kodi mwamuna wa zaka 100 angabereke mwana zoona? Komanso Sara mkazi wa zaka 90, zoona angakhale ndi mwana?”+ 18  Kenako Abulahamu anapempha Mulungu woona kuti: “Mbuyanga! Isimaeli akhale ndi moyo pamaso panu.”+ 19  Pamenepo Mulungu anati: “Ndithu Sara mkazi wako adzakuberekera mwana wamwamuna ndipo dzina lake udzamutche Isaki.+ Ndidzakhazikitsa pangano ndi iye, limene lidzakhala mpaka kalekale kwa mbewu yake yobwera pambuyo pa iye.+ 20  Koma za Isimaeli ndamva pempho lako. Iye ndidzamudalitsa ndipo ndidzamupatsa ana ambiri, komanso ndidzachulukitsa kwambiri mbadwa zake.+ Atsogoleri 12 a mafuko adzatuluka mwa iye, ndipo ndidzamupangitsa kukhala mtundu waukulu.+ 21  Koma ndidzakhazikitsa pangano langa ndi Isaki,+ amene Sara adzakuberekera iwe nthawi ngati yomwe ino chaka chamawa.”+ 22  Ndi mawu amenewa, Mulungu anamaliza kulankhula ndi Abulahamu, n’kuchoka.+ 23  Ndiyeno Abulahamu anatenga mwana wake Isimaeli ndi amuna onse obadwira m’nyumba yake, ndi aliyense amene anamugula ndi ndalama zake, komanso mwamuna aliyense wa m’nyumba ya Abulahamu. Anawadula khungu lawo la kunsonga tsiku lomwelo, monga mmene Mulungu anamuuzira.+ 24  Abulahamu anadulidwa khungu lake la kunsonga ali ndi zaka 99.+ 25  Ndipo Isimaeli anadulidwa khungu lake la kunsonga ali ndi zaka 13.+ 26  Choncho, Abulahamu ndi mwana wake Isimaeli anadulidwa tsiku lomwelo.+ 27  Komanso amuna onse a m’nyumba yake, aliyense wobadwira m’nyumba yake ndi aliyense wogulidwa ndi ndalama zake kwa mlendo anadulidwa limodzi naye.+

Mawu a M'munsi