Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kukhala Mwamtendere ndi Abale Anga?

N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kukhala Mwamtendere ndi Abale Anga?

 “Mumawakonda kwambiri koma nthawi zina amakukhumudwitsani”

Anthu amanena kuti “anthu apachibale amakondana kwambiri, komanso sachedwa kukhumudwitsana.” Pachibale anthu mumakondana kwambiri koma nthawi zina mumapezeka kuti mwasemphana maganizo. Mtsikana wina wazaka 18 dzina lake Helena ananena kuti: “Mchimwene wanga amakonda kundiputa. Iye amachitira dala zinthu zomwe akudziwa kuti ndikwiya nazo.”

Nthawi zina anthu apachibale angathetse mkangano pokambirana mwaulemu. Mwachitsanzo:

 • Munthu ndi mchimwene wake omwe amagona chipinda chimodzi angasemphane maganizo pa nkhani yopatsana mpata woti wina achite zinazake. Kodi angathetse bwanji vutoli? Angayesetse kuphunzira kukhala wololera ndi kumapatsana mpata. Angachitenso bwino kutsatira mfundo ya pa Luka 6:31.

 • Mtsikana wina amangotenga zovala za mchemwali wake asanapemphe n’kumavala. Kodi angathetse bwanji vutoli? Angakambirane nkhaniyo n’kuuzana zomwe aliyense amafuna mnzake atamachita. Angachitenso bwino kutsatira mfundo ya pa 2 Timoteyo 2:24.

Nthawi zina mikangano ya anthu apachibale imatha kukula kwambiri mpaka kuyambitsa mavuto aakulu. Taganizirani zitsanzo ziwiri za m’Baibulo izi:

 • Miriamu ndi Aroni ankachitira nsanje mchimwene wawo Mose ndipo zimenezi zinabweretsa mavuto aakulu. Werengani nkhaniyi pa Numeri 12:1-15. Kenako dzifunseni kuti: ‘Ndingatani kuti ndisiye kuchitira nsanje m’bale wanga?’

 • Kaini anakwiya kwambiri mpaka anapha m’bale wake Abele. Werengani nkhaniyi pa Genesis 4:1-12. Kenako dzifunseni kuti: ‘Ndingatani kuti ndisamapse mtima kwambiri mchimwene kapena mchemwali wanga akandilakwira?’

 Zifukwa ziwiri zokuthandizani kuti muzikhala mwamtendere

Ngakhale kuti kukhala mwamtendere ndi abale anu sikophweka, pali zifukwa ziwiri zomwe zikusonyeza kuti kuchita zimenezi n’kofunika kwambiri.

 1. Zimasonyeza kuti mukukula. Mnyamata wina dzina lake Alex anati: “Azichemwali anga awiri akalakwitsa chinachake, sindinkachedwa kuwakwiyira. Koma panopa ndimayesetsa kuchita nawo zinthu moleza mtima komanso modekha. Nanunso mutha kuona kuti ndakuladi.”

  Baibulo limati: “Wosafulumira kukwiya n’ngozindikira zinthu kwambiri, koma wokwiya msanga amalimbikitsa uchitsiru.”—Miyambo 14:29.

 2. Zimakuthandizani kuti mukonzekere zam’tsogolo. Ngati panopa mumalephera kukhala bwino ndi achibale anu, mungadzakwanitse bwanji kukhala bwino ndi mwamuna kapena mkazi wanu, mnzanu wa kuntchito, bwana wanu kapenanso munthu wina aliyense?

  Dziwani izi: Kuti musadzavutike kukhala bwino ndi anthu ena mtsogolo mumafunika kuyambiratu panopa kuphunzira kuyankhulana bwino ndi anthu a m’banja lanu.

  Baibulo limati: “Ngati ndi kotheka, khalani mwamtendere ndi anthu onse, monga mmene mungathere.”—Aroma 12:18.

Kodi mukufuna kudziwa mmene mungamathetsere mikangano ndi wachibale wanu? Werengani bokosi lakuti “Zimene achinyamata anzanu amanena” m’munsimu kenako onani zoti muchite pa mutu wakuti, “Zimene Mungachite Mukasemphana Maganizo ndi Abale Anu.”