Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndiyenera Kuganizira Mfundo Ziti pa Nkhani ya Masewera?

Kodi Ndiyenera Kuganizira Mfundo Ziti pa Nkhani ya Masewera?

 Masewera akhoza kukhala abwino kapena oipa. Zimangodalira masewera amene mumachita, zimene mumachita posewerapo komanso kuchuluka kwa nthawi imene mumachita masewerawo.

 Ubwino wake

 Masewera angathandize munthu kuti akhale wathanzi. Baibulo limanena kuti: “Kuchita masewera olimbitsa thupi n’kopindulitsa.” (1 Timoteyo 4:8) Mnyamata wina dzina lake Ryan anati: “Kuchita masewera olimbitsa thupi kumathandiza kwambiri munthu kusiyana ndi kungokhala m’nyumba n’kumasewera magemu apakompyuta.”

 Masewera angathandize munthu kukhala wodziletsa komanso kugwirizana ndi anthu ena. Baibulo limagwiritsa ntchito fanizo lokhudza masewera pophunzitsa mfundo inayake yofunika. Limati: “Ochita mpikisano wa liwiro amathamanga onse, koma mmodzi yekha ndiye amalandira mphoto.” Limanenanso kuti: “Munthu aliyense wochita nawo mpikisano amakhala wodziletsa pa zinthu zonse.” (1 Akorinto 9:24, 25) Kodi tikuphunzirapo chiyani palembali? Munthu akamachita masewera amafunika kukhala wodziletsa komanso kugwirizana ndi anzake kuti azichita zinthu motsatira malamulo a masewerawo. Mtsikana wina dzina lake Abigail amagwirizana ndi mfundoyi ndipo anati: “Kuchita masewera kwandithandiza kuti ndizigwirizana ndi anthu ena ndiponso kuti ndizilankhulana nawo bwino.”

 Masewera angathandize kuti munthu apeze anzake apamtima. Masewera amachititsa kuti anthu azigwirizana. Mnyamata wina dzina lake Jordan anati: “N’zoona kuti masewera ambiri angachititse kuti anthu azipikisana. Komabe ngati cholinga cha munthu ndi kungosangalala ndi masewerawo, akhoza kupeza anzake ambiri.”

 Mavuto ake

 Masewera amene mumachita. Baibulo limanena kuti: “Yehova amasanthula anthu olungama ndi oipa omwe, ndipo Mulungu amadana kwambiri ndi aliyense wokonda chiwawa.”—Salimo 11:5.

 Masewera ena amachita kuonekeratu kuti ndi achiwawa. Mwachitsanzo, mtsikana wina dzina lake Lauren ananena kuti: “Munthu akamasewera nkhonya, cholinga chake chimangokhala kuvulaza mnzakeyo. Popeza kuti Akhristufe timapewa kumenyana ndi anthu ena, kodi tingasangalale kuonerera anthu ena akumenyedwa?”

 Zoti muganizire: Kodi inuyo munaonerapo kapena kuchita masewera enaake achiwawa n’kumaganiza kuti sizingakuchititseni kuti nanunso muchite zachiwawazo? Ngati zili choncho, musaiwale kuti lemba la Salimo 11:5 limasonyeza kuti Yehova samangodana ndi munthu wochita chiwawa koma amadananso ndi munthu “wokonda chiwawa.”

 Zimene mumachita posewera. Baibulo limati: “Musachite chilichonse ndi mtima wokonda mikangano kapena wodzikuza, koma modzichepetsa, ndi kuona ena kukhala okuposani.”—Afilipi 2:3.

 N’zoona kuti pa masewera alionse amene ali ndi magulu awiri pamakhala kupikisana kuti adziwike amene wawina. Koma munthu akamafuna kuti azingowina nthawi zonse sasangalala ndi masewerawo. Mnyamata wina dzina lake Brian anati: “Kupanda kusamala, munthu akhoza kuyamba mosavuta mtima wampikisano. Munthu akakhala ndi luso pa masewera enaake, ayenera kuchita khama kwambiri kuti akhale wodzichepetsa.”

 Zoti muganizire: Mnyamata wina dzina lake Chris anati: “Timasewera mpira mlungu uliwonse koma sipalephera kupezeka anthu ovulala.” Ndiye dzifunseni kuti, ‘Ndi zinthu ziti zimene zingachititse kuti anthu azivulala? Nanga kodi ineyo ndingathandize bwanji kuti asamavulale?’

 Kuchuluka kwa nthawi imene mumachita masewerawo. Baibulo limati: “Muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.”—Afilipi 1:10.

 Muyenera kuika zinthu zokhudza kutumikira Yehova pamalo oyamba. Masewera ambiri amatenga nthawi yayitali kuti athe. Choncho mungawononge nthawi yanu, kaya mukusewera nawo kapena mukungoonera. Mtsikana wina dzina lake Daria ananena kuti: “Ndinkakangana ndi mayi anga chifukwa chakuti ndinkawononga nthawi yanga yambiri kuonera masewera pa TV m’malo mochita zinthu zina zofunika.”

Kuchita kapena kuonera masewera kwambiri kumakhala ngati kuthira mchere wambiri m’chakudya

 Zoti muganizire: Makolo akakupatsani malangizo okhudza mmene mukugwiritsira ntchito nthawi yanu, kodi mumawamvera? Mtsikana wina dzina lake Trina anati: “Ndinkati ndikakhala ndi abale anga n’kumaonera masewera m’malo mogwira ntchito zina zofunika, mayi ankatiuza kuti anthu ochita masewerawo amalandirabe malipiro, kaya mukuonera masewerawo kapena ayi. Kenako ankatifunsa kuti, ‘Nanga inuyo akupatseni malipiro ndi ndani?’ Mayi ankatanthauza kuti: Anthu amene akusewerawo ali pa ntchito yawo. Koma tikapanda kulemba homuweki komanso kugwira ntchito zina zofunika, m’tsogolo tidzavutika kuti tipeze ntchito. Ankafuna kuti tizindikire zoti si bwino kuika kuchita kapena kuonera masewera pamalo oyamba.”