Pitani ku nkhani yake

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Zinthu Zinachita Kulengedwa?—Gawo 3: N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kukhulupirira Kuti Zinthu Zinachita Kulengedwa?

Kodi Zinthu Zinachita Kulengedwa?—Gawo 3: N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kukhulupirira Kuti Zinthu Zinachita Kulengedwa?

“Ukamakhulupirira zoti zinthu zinachita kulengedwa, anthu angaganize zoti ndiwe wosachangamuka. Angamaone kuti ukungokakamira zimene makolo ako anakuphunzitsa uli mwana, kapena ukungokhulupirira zinthu zopanda umboni zimene zipembedzo zimaphunzitsa.”​—Jeanette.

 Kodi mukugwirizana ndi maganizo a Jeanette? Ngati ndi choncho, mwina mungayambe kukayikira zimene mumakhulupirira zoti zinthu zinachita kulengedwa. Ndipotu palibe munthu amene amafuna kuti azioneka ngati mbuli. Ndiyeno mungatani kuti muthane ndi maganizo amenewa?

 N’chifukwa chiyani ena amaopa kuvomereza zoti zinthu zinachita kulengedwa?

 1. Ngati ukukhulupirira zoti zinthu zinachita kulengedwa, anthu ena angaganize kuti ukutsutsana ndi sayansi.

 “Aphunzitsi athu ananena zoti anthu omwe amakhulupirira zoti zinthu zinachita kulengedwa ndi opanda nzeru. Anthuwo amangokhulupirira kuti zinthu zinachita kulengedwa chifukwa sangathe kufotokoza mmene zinthu m’dzikoli zinayambira komanso mmene zimayendera.”​—Maria.

 Zimene muyenera kudziwa: Anthu ena amanena zimenezi chifukwa choti sadziwa zoti akatswiri ena asayansi otchuka kwambiri, monga Galileo ndi Isaac Newton, ankakhulupirira zoti kuli Mlengi. Ndipotu zimene akatswiriwa ankakhulupirira sikuti ndi zotsutsana ndi sayansi. Masiku anonso, asayansi ena amakhulupirira zoti zinthu zinachita kulengedwa ndipo amaona kuti zimenezi sizikutsutsana ndi sayansi.

 Tayesani izi: Lembani mawu akuti (limodzi ndi mitengero) “akufotokoza za chikhulupiriro chake” m’kabokosi kofufuzira pa LAIBULALE YA PA INTANETI ya Watchtower kuti muone zitsanzo za anthu ena amene ndi madokotala kapena asayansi omwe amakhulupirira zoti zinthu zinachita kulengedwa. Onani chimene chinawathandiza kuti ayambe kukhulupirira zimenezi.

 Mfundo yofunika kwambiri: Kukhulupirira zoti zinthu zinachita kulengedwa sikuchititsa munthu kuti azidana ndi sayansi. Ndipotu ngati munthu ataphunzira zinthu zambiri zachilengedwe m’dzikoli angayambe kukhulupirira kwambiri zoti zinthuzo zinachita kulengedwa.​—Aroma 1:20.

2. Ngati ungamakhulupirire zimene Baibulo limanena zoti zinthu zinachita kulengedwa, anthu ena angaganize kuti umangokakamira zimene zipembedzo zimaphunzitsa.

 “Anthu ambiri amakhulupirira zoti zinthu zinangokhalako zokha, osati zinachita kulengedwa. Iwo amaona kuti nkhani ya m’buku la Genesis ndi yongopeka.”​—Jasmine.

 Zimene muyenera kudziwa: Kawirikawiri anthu amakhulupirira zinthu zosiyanasiyana koma zolakwika zokhudza nkhani ya m’Baibulo yonena za kulengedwa kwa zinthu. Mwachitsanzo, anthu ena amanena zoti dzikoli linalengedwa chaposachedwapa, komanso kwa masiku 6 enieni okhala ndi maola 24 tsiku lililonse. Koma m’Baibulo mulibe mfundo zimenezi.

 •   Lemba la Genesis 1:1 linanena momveka bwino kuti: “Pa chiyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.” Izi sizikutsutsana ndi umboni umene asayansi apeza, wakuti dziko lapansili lakhalapo kwa zaka mabiliyoni ambirimbiri.

 •   Mawu akuti “tsiku” amene agwiritsidwa ntchito m’buku la Genesis angatanthauze nthawi yaitali. Mwachitsanzo, pa Genesis 2:4, mawu akuti “tsiku” agwiritsidwa ntchito ponena za masiku onse 6 amene zinthu zinalengedwa.

 Mfundo yofunika kwambiri: Nkhani ya m’Baibulo yonena za kulengedwa kwa zinthu ndi yogwirizana ndi mfundo zolondola zokhudza sayansi.

 Ganizirani zimene mumakhulupirira

 Sikuti munthu angafunike kumangokhulupirira zoti zinthu zinachita kulengedwa popanda umboni. Koma munthuyo angafunike kuganizira mwakuya umboni wamphamvu umene ulipo. Taganizirani izi:

 Chinthu chilichonse chogometsa chimene mungaone pamoyo wanu chimakhala choti chinapangidwa ndi winawake. Mwachitsanzo, mukaona zinthu ngati kamera, ndege, kapena nyumba, mumadziwa kuti zinthuzo si zinangokhalapo zokha koma zinachita kupangidwa. Bwanji osagwiritsanso ntchito mfundo yomweyi mukaona zinthu zogometsa monga diso la munthu, mbalame yomwe ikuuluka, kapena dziko lathu lapansili?

 Zoti muganizire: Nthawi zambiri akatswiri opanga zinthu amapanga zinthuzo potsanzira zinthu zachilengedwe zimene aona, ndipo amafuna anthu ena adziwe zinthu zimene apangazo komanso aziwapatsa ulemu. Ngati anthu amene apanga zinthu pokopera zachilengedwe amapatsidwa ulemu, kodi mukuona kuti zingakhale zomveka kuti anthu asamavomereze zoti zinthu zogometsa za m’chilengedwechi zinachita kulengedwa, komanso asamapereke ulemu kwa Mlengi wa zinthu zonsezi?

Kodi n’chinthu chanzeru kumakhulupirira zoti ndege inachita kupangidwa ndi winawake, koma mbalame inangokhalako yokha?

 Zimene Zingakuthandizeni kudziwa kuti zinthu zinachita kulengedwa

 Kuunika mozama umboni umene uli m’zinthu zachilengedwe kungakuthandizeni kuti muzikhulupirira kwambiri zoti zinthu zinachita kulengedwa.

 Tayesani izi: Lembani mawu akuti (osaiwala mikutira mawuyo) “kodi zinangochitika zokha” m’kabokosi kofufuzira pa LAIBULALE YA PA INTANETI ya Watchtower. Mukatero muona mitu yambirimbiri ya nkhani zakuti, “Kodi Zinangochitika Zokha?” zimene zinatuluka mu Galamukani! ndipo sankhani nkhani imene yakusangalatsani. Pa nkhani iliyonse, pezani mbali yochititsa chidwi kwambiri ya chinthu chachilengedwe chimene akuchifotokozacho. Kodi zimenezo zikukuthandizani bwanji kukhulupirira zoti zinthu zinachita kulengedwa ndi Mlengi wanzeru?

 Fufuzani mozama: Gwiritsani ntchito nkhani zotsatirazi zochokera m’magazini a Galamukani! kuti mufufuze umboni wamphamvu wotsimikizira kuti zinthu zinachita kulengedwa.

 Galamukani! February 2009

 •   Dziko lili pamalo abwino kwambiri ndipo lili ndi zonse zofunikira kuti zinthu zamoyo zizikhalapo.​—Onani tsamba 3.

   Galamukani! September 2006

  •   Zinthu zachilengedwe zimasonyeza kuti zinachita kupangidwa mwaluso.​—Onani tsamba 24 mpaka 25.

  •   Nkhani ya m’buku la m’Baibulo la Genesis, yonena za kulengedwa kwa zinthu ndi yogwirizana ndi sayansi.​—Onani tsamba 18 mpaka 20.

  •   Zinthu zamoyo ndi zogometsa kwambiri, moti n’zosamveka kunena kuti zinangokhalako zokha.​—Onani tsamba 4 mpaka 7.

 •   Zinthu zonse zamoyo sizinachite kusintha kuchokera ku chinthu chimodzi chamoyo. Zinthu zakufa zakale zikusonyeza kuti mitundu yonse ikuluikulu ya zinyama inakhalapo mwadzidzidzi, osati inachita kusintha mwa pang’onopang’ono.​—Onani tsamba 13 mpaka 17.

  •  Galamukani! February 2010

  •   Sizikanatheka kuti zinthu zopanda moyo zisinthe mwadzidzidzi n’kupanga zinthu zamoyo.​—Onani tsamba 23.

  •  Galamukani! November 2011

  •   DNA imasunga zinthu zochuluka zedi kuposa zimene zingasungidwe m’makompyuta apamwamba kwambiri.​—Onani tsamba 4 mpaka 6.

“Zinthu zachilengedwe, monga zinyama komanso zinthu zakuthambo, zimandithandiza kukhulupirira zoti kuli Mulungu. Zinyama zimachita zinthu mwadongosolo. Nazonso zinthu zakuthambo zinaikidwa m’malo awo mwadongosolo kwambiri.”​—Thomas.