Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndingatani Kuti Ndizigwirizana Ndi Aphunzitsi Anga?

Kodi Ndingatani Kuti Ndizigwirizana Ndi Aphunzitsi Anga?

 Aphunzitsi ovuta

 Pafupifupi mwana wasukulu aliyense ali ndi mphunzitsi wooneka kuti ndi wokondera, wovuta kapenanso wouma mtima.

 •   Mnyamata wina wazaka 21 dzina lake Luis anati: “Mphunzitsi wanga wina ankakonda kutukwana komanso ankanyoza ana m’kalasi. Mwina ankaganiza kuti sangachotsedwe ntchito chifukwa anali atatsala pang’ono kupuma pa ntchito.”

 •   Melanie wazaka 25 amakumbukira kuti aphunzitsi ake ankakonda kumuchitira zankhanza kuposa anzake ena onse am’kalasi mwake. Iye anati: “Iwo ankalankhula modzikhululukira ponena kuti ankachita zimenezi chifukwa chakuti sindili m’chipembedzo chotchuka. Anandiuza kuti ndisamakule mopepera komanso ndizizolowera moyo wamavuto.”

 Ngati mphunzitsi wanu ndi wovuta, simufunika kusiya sukulu, m’malomwake pali mfundo zimene zingakuthandizeni kuti moyo musaumve kuwawa. Tayesani kuchita zotsatirazi.

 Zomwe zingakuthandizeni

 •   Muzikhala ololera. Aphunzitsi amasiyanasiyana pa zimene amafuna kuti ana asukulu azichita. Muzizindikira zimene aphunzitsi anu amafuna kuti muzichita ndipo muziyesetsa kuchita zimenezo.

   Mfundo ya m’Baibulo: “Munthu wanzeru amamvetsera ndi kuphunzira malangizo owonjezereka.”—Miyambo 1:5.

   “Ndinazindikira kuti ndikufunika kumachita zinthu mmene aphunzitsi anga akufunira, choncho ndinkayesetsa kuchita ntchito yomwe apereka mmene iwo akufunira. Zimenezi zinandithandiza kuti ndisamavutike kugwirizana nawo.”—Christopher.

 •   Muzichita zinthu mwaulemu. Muziyesetsa kulankhula mwaulemu ndi aphunzitsi anu. Musamalankhule mopikisana nawo ngakhale pamene mukudziwa kuti iwowo ndi amene alakwitsa. Muzikumbukira kuti iwo amakuonani monga mwana wasukulu osati mnzawo.

   Mfundo ya m’Baibulo: “Nthawi zonse mawu anu azikhala achisomo, okoma ngati kuti mwawathira mchere, kuti mudziwe mmene mungayankhire wina aliyense.”—Akolose 4:6.

   “Nthawi zambiri aphunzitsi salemekezedwa ndi ana asukulu ngati mmene zimayenera kukhalira, choncho mukamayesetsa kuwalemekeza, nawonso amakulemekezani komanso amasintha mmene amachitira nanu zinthu.”—Ciara.

 •   Muziwamvetsa. Aphunzitsi nawonso ndi anthu ngati inu nomwe. Zimenezi zikutanthauza kuti nawonso amapanikizika komanso amakhala ndi nkhawa ngati munthu wina aliyense. Choncho musamawaweruze n’kumanena kuti, ‘Aphunzitsi anga ndi ovuta’ kapenanso kuti, ‘Aphunzitsi anga amadana nane.’

   Mfundo ya m’Baibulo: “Tonsefe timapunthwa nthawi zambiri.”—Yakobo 3:2.

   “Ntchito ya uphunzitsi si yophweka. Ndikuona kuti pamakhala ntchito yaikulu kwambiri kuti athandize ana onse kuti akhale ndi makhalidwe abwino ndiponso kuwaphunzitsa. Ndimafuna kuwachepetsera ntchito kuti asamangokhalira kudandaula za ana asukulufe.”—Alexis.

 •    Muzifotokozera makolo anu. Makolo anu amakufunirani zabwino ndipo amafuna kuti muzichita bwino kusukulu. Iwo angakupatseni malangizo omwe angakuthandizeni kudziwa zoyenera kuchita ngati mphunzitsi wanu ndi wovuta.

   Mfundo ya m’Baibulo: “Zolingalira sizikwaniritsidwa ngati anthu sakambirana moona mtima.”—Miyambo 15:22.

   “Makolo amadziwa bwino kwambiri mmene angathetsere mavuto kusiyana ndi achinyamata. Choncho muzimvera malangizo amene amakupatsani ndipo zinthu zizikuyenderani bwino kwambiri.”—Olivia.

 Mmene mungalankhulire ndi aphunzitsi anu

 Nthawi zina mungafunike kukambirana ndi aphunzitsi anu n’kuwafotokozera zimene mukuwadandaula. Musamachite mantha kuwafotokozera poopa kuti nkhaniyo ingathere mu mkangano. Mungadabwe kuona kuti mwakambirana nkhaniyo bwinobwino popanda kukangana.

 Mfundo ya m’Baibulo: “Titsatire zinthu zobweretsa mtendere ndiponso zolimbikitsana.”—Aroma 14:19.

 “Ngati mukuona kuti mphunzitsi wanu ndi wovuta kwa inu nokha basi, mufunseni kuti mudziwe ngati munamuchitira zinthu zomwe zinamukhumudwitsa. Zimene angakuuzeni zingakuthandizeni kudziwa zimene mukufunika kusintha.”—Juliana.

 “Mungachite bwino kufotokozera mphunzitsi wanu mmene mukumvera zokhudza nkhaniyo koma modekha. Muyenera kuchita zimenezi muli pa awiri, musanalowe m’kalasi kapena mutaweruka. Iye akhoza kukumvetsani komanso angayambe kukulemekezani chifukwa cha mmene mwachitira zinthu.”—Benjamin.

 NKHANI YOMWE INACHITIKADI

 “Ndinkalephera kwambiri kusukulu komanso aphunzitsi anga sankandithandiza n’komwe. Ndinkafuna kusiya sukulu chifukwa sindinkasangalala.

 Ndinakafunsa malangizo kwa mphunzitsi wina. Iye anandiuza kuti: ‘Simudziwana bwino ndi mphunzitsiyo. Ukufunika kumuuza vuto limene ukukumana nalo. Zimenezi zingathandize ophunzira ena omwe amachita mantha kuti azimasuka naye.’

 Sindinkafuna kukalankhula naye. Koma ndinaganizira zomwe mphunzitsiyo ankanena ndipo ndinaona kuti zinali zoona. Ndinkafunika kuchitapo kanthu kuti zinthu zisinthe.

 Choncho tsiku lina, ndinakumana ndi mphunzitsiyo ndipo ndinakambirana naye mwaulemu kuti ndimayamikira kwambiri akamatiphunzitsa ndipo ndimafuna ndizikhoza bwino m’kalasi. Komabe, zinthu zinkandivuta komanso sindinkadziwa zoyenera kuchita. Kenako anadzipereka kuti andithandiza tikangoweruka kapena angondilembera imelo.

 Zimenezi zinandidabwitsa. Titangokambirana, ndinayamba kugwirizana kwambiri ndi mphunzitsiyo moti ndinayambiranso kusangalala ndi sukulu.”—Maria.

 Zimene zingakuthandizeni: Ngati simugwirizana ndi mphunzitsi wanu, muziona kuti umenewu ndi mwayi wanu woti muphunzire zinazake zomwe zidzakuthandizeni mukadzakula. Katie wazaka 22, anati: “Mukadzamaliza sukulu, mudzakumanabe ndi anthu ena amaudindo omwe ndi ovuta kuchita nawo zinthu. Ngati mungamagwirizanebe ndi mphunzitsi wovuta, mudzakwanitsa kugwirizananso ndi anthu ena ovuta amene mungadzakumane nawo m’tsogolo.”