Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA

Kodi Kuchita Zamatsenga Kuli ndi Vuto Lililonse?

Kodi Kuchita Zamatsenga Kuli ndi Vuto Lililonse?

Kodi inuyo mukuganiza bwanji?

  • Kodi pali vuto lililonse ngati munthu atachita zamatsenga kuti adziwe zinthu zam’tsogolo kapena zinthu zina?

  • Kodi nkhani zamizimu zimangokhala nthano chabe kapena ndi zenizeni komanso zoopsa?

Munkhaniyi tiona chifukwa chake anthu amachita chidwi ndi zamizimu komanso chifukwa chake tiyenera kusamala nazo.

 N’chifukwa chiyani anthu amachita nazo chidwi?

Masiku ano zamatsenga zimapezeka kwambiri m’mafilimu, m’mapulogalamu a pa TV, m’masewera apakompyuta komanso m’mabuku. Zimenezi zachititsa kuti achinyamata azichita chidwi ndi zinthu monga ziwanda, mavampaya ndi ufiti. N’chifukwa chiyani zili choncho? Zina mwa zifukwa zake ndi izi:

  • Chidwi: Amafuna kudziwa ngati mizimu ilikodi

  • Nkhawa: Amafuna kudziwa zimene zidzachitike m’tsogolo

  • Kuferedwa: Amafuna kulankhulana ndi anzawo kapena abale awo amene anamwalira

Zinthu zimene tatchulazi pazokha zilibe vuto. Anthufe mwachibadwa timafuna kudziwa zam’tsogolo ndipo mnzathu akamwalira timamusowa. Koma pali zinthu zina zimene tiyenera kusamala nazo.

 N’chifukwa chiyani muyenera kusamala?

Baibulo limapereka malangizo osapita m’mbali okhudza zamatsenga. Mwachitsanzo, limanena kuti:

“Pakati panu pasapezeke munthu . . . wolosera, wochita zamatsenga, woombeza, wanyanga, kapena wolodza ena, aliyense wofunsira kwa wolankhula ndi mizimu, wolosera zam’tsogolo kapena aliyense wofunsira kwa akufa. Pakuti aliyense wochita zimenezi ndi wonyansa kwa Yehova.”—Deuteronomo 18:10-12.

N’chifukwa chiyani Baibulo limaletsa kuchita zamizimu?

  • Zinthu zamizimu zimachititsa kuti munthu azigwirizana ndi ziwanda. Baibulo limanena kuti angelo ena anaukira Mulungu n’kukhala adani ake. (Genesis 6:2; Yuda 6) Angelo oipawa amatchedwa ziwanda ndipo amapusitsa anthu pogwiritsa ntchito anthu olosera kapena oombeza. Koma tikamachita zimenezi timakhala kuti tikugwirizana ndi adani a Mulungu.

  • Kukhulupirira mizimu kumachititsa anthu kuganiza kuti anthu ena angathe kudziwa zam’tsogolo. Koma Mulungu yekha ndi amene anganene kuti: “Ine ndi amene ndimanena za mapeto kuyambira pa chiyambi. Kuyambira kalekale, ndimanena za zinthu zimene sizinachitike.”—Yesaya 46:10; Yakobo 4:13, 14.

  • Kukhulupirira mizimu kumachititsa anthu kuganiza kuti akhoza kulankhulana ndi anthu amene anamwalira. Koma Baibulo limanena kuti: “Akufa sadziwa chilichonse . . . Kulibe kugwira ntchito, kuganiza zochita, kudziwa zinthu, kapena nzeru, ku Manda.”—Mlaliki 9:5, 10.

Pa zifukwa zimenezi, a Mboni za Yehova amapewa chilichonse chokhudzana ndi zamizimu. Amapewanso zosangalatsa zokhala ndi mavampaya, mizukwa komanso zamatsenga. Mtsikana wina dzina lake Maria ananena kuti: “Ngati mufilimu muli zinthu zamatsenga, sindiyenera kuonera.” a

Mofanana ndi munthu wachiwembu amene amadzibisa kuti musamuzindikire, ziwanda zimanamizira kukhala anzanu kapena achibale anu amene anamwalira

 Zimene mungachite

  • Muziyesetsa kupewa zosangalatsa zilizonse zokhudza matsenga n’cholinga choti ‘musapalamule kwa Mulungu.’—Machitidwe 24:16.

  • Muzitaya chilichonse chokhudza matsenga chimene muli nacho. Werengani Machitidwe 19:19, 20, kuti muone zimene Akhristu oyambirira anachita pa nkhaniyi.

Kumbukirani kuti: Mukamapewa zamatsenga mumasonyeza kuti muli kumbali ya Yehova ndipo iye amasangalala kwambiri.—Miyambo 27:11.

a Koma apa sitikutanthauza kuti mafilimu onse osonyeza zinthu zodabwitsa ndi amatsenga. Akhristu amatsatira chikumbumtima chawo chophunzitsidwa Baibulo kuti apewe chilichonse chokhudzana ndi zamizimu.—2 Akorinto 6:17; Aheberi 5:14.