Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndithetse Chibwenzichi?—Gawo 2

Kodi Ndithetse Chibwenzichi?—Gawo 2

Choyamba, sankhani malo ndi nthawi yabwino kuti mukambirane zimenezi. Kodi nthawi komanso malo abwino angakhale otani?

Ganizirani zimene inuyo mungakonde kuti akuchitireni zitakhala kuti akuthetsa chibwenzi ndi mnzanuyo. (Mateyu 7:12) Kodi mungasangalale ngati atakuuzirani pagulu? Ayi ndithu.

Mungachite bwino kwambiri kuti musathetse chibwenzicho pafoni kapena pa imelo, koma muonane pamasom’pamaso. Pokhapokha ngati patakhala zifukwa zomveka zoti simungaonane pamasom’pamaso, mwina mungagwiritse ntchito foni kapena kompyuta. Choncho sankhani nthawi ndi malo abwino kuti mukumane n’kukambirana nkhaniyi.

Mukakumana, kodi munganene zotani? Mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu kuti ‘azilankhula zoona’ nthawi zonse.—Aefeso 4:25.

Choncho njira yabwino ndi yakuti muzilankhula mosamala koma motsimikiza. Fotokozani mosapita m’mbali chifukwa chimene inuyo mukuonera kuti chibwenzicho chithe.

Simukufunikira kumuyalira zolakwa zake zonse kapena kunena zinthu zambirimbiri zomunyoza. M’malo monena kuti, “Suchita zakutizakuti” kapena “Sunachitepo zakutizakuti,” zingakhale bwino kugwiritsa ntchito mawu osonyeza mmene inuyo mukuonera. Mungagwiritse ntchito mawu ngati akuti, “Ineyo ndikufuna munthu amene . . . ” kapena “Ndikuona kuti chibwenzi chithe chifukwa chakuti . . . ”

Imeneyi si nthawi yolankhula mokayikira kapena yosintha maganizo n’kulolera zimene mnzanuyo anganene kuti musathetse chibwenzicho. Kumbukirani kuti mwasankha kuthetsa chibwenzicho chifukwa chakuti pali vuto lalikulu. Choncho samalani ngati mnzanuyo akuchita zinthu kapena kulankhula mochenjera n’cholinga choti musinthe maganizo. Mtsikana wina dzina lake Lori ananena kuti: “Nditathetsa chibwenzi, mnyamatayo anayamba kuchita zinthu ngati wasokonezeka maganizo kwambiri. Ndikuganiza kuti ankachita zimenezo kuti ndimumvere chisoni. Ngakhale kuti ndinamumveradi chisoni, sindinasinthe maganizo.” Mofanana ndi Lori, tsimikizirani kuti musasinthe zimene mwasankha. Mukati ayi akhaledi ayi.Yakobo 5:12.