ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA
Kodi Ndingatani Ngati Chibwenzi Chatha?
Mnyamata wina dzina lake Steven anati, “Chibwenzi chathu chitatha, ndinakhumudwa kwambiri. Zinandiwawa kwambiri ndipo ndinamva ululu wamumtima woti sindinaumvepo moyo wanga wonse.”
Kodi zimenezi zinakuchitikiranipo? Ngati ndi choncho, nkhaniyi ingakuthandizeni.
Mmene munthu amamvera
Chibwenzi chikatha, zimakhala zopweteka kwa onse awiri.
Ngati inuyo ndi amene munathetsa chibwenzi mwina mungavomereze zimene ananena mtsikana wina dzina lake Jasmine yemwe anati, “Ndinavutika kwambiri mumtima chifukwa choti ndinakhumudwitsa munthu yemwe ndinkamukonda ndipo sindikufuna kudzachitanso zimenezi.”
Ngati chibwenzicho simunathetse ndinu mwina mungagwirizane ndi zimene anthu ena amanena kuti umakhala ngati waferedwa. Mtsikana wina dzina lake Janet anati, “Ndinkachita zimene munthu amachita akaferedwa monga kulephera kuvomereza, kukwiya ndiponso kuvutika maganizo, koma patadutsa pafupifupi chaka chimodzi ndinangovomereza.”
Zoona Zake N’zakuti: Munthu amakhumudwa kwambiri chibwenzi chikatha. Ndipo wolemba Baibulo wina ananena kuti: “Mtima wosweka umaumitsa mafupa.”—Miyambo 17:22.
Zimene Mungachite
Uzani mnzanu yemwe ndi wodalirika. Baibulo limati: “Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo bwenzilo ndi m’bale amene anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.” (Miyambo 17:17) Kuuza kholo lanu kapena mnzanu wina yemwe mumamudalira kungakuthandizeni kuti muyambe kuona nkhaniyo moyenera.
“Kwa miyezi ingapo ndinkangochita zinthu ndekhandekha ndipo sindinkafuna kuuza aliyense mmene ndinkamvera. Koma kufotokozera anzako mmene ukumvera n’kothandiza ndipo ndinayamba kumva bwino nditachita zimenezi.”—Janet.
Phunzirani pa zomwe zachitikazo. Mwambi wina wa m’Baibulo umati: “Upeze nzeru, upezenso luso lomvetsa zinthu.” (Miyambo. 4:5) Mavuto amene takumana nawo angatiphunzitse zambiri zokhudza ifeyo komanso zimene tingachite munthu wina akatikhumudwitsa.
“Chibwenzi chathu chitatha, mnzanga wina anandifunsa kuti, ‘Kodi waphunzira chiyani panthawi imene unali pachibwenzi, ndipo ungadzagwiritse bwanji ntchito zimene waphunzirazo ngati utadzakhalanso pachibwenzi?’.”—Steven.
Muzipemphera. Baibulo limati: “Umutulire Yehova nkhawa zako, Ndipo iye adzakuchirikiza.” (Salimo 55:22) Pemphero lingakuthandizeni pa nthawi imene chibwenzi chanu chatha ndipo mukhoza kuyamba kuona nkhaniyo moyenera.
“Muzipemphera nthawi zonse. Yehova amamvetsa ululu womwe mukumva ndipo amadziwa bwino zimene zikukuchitikirani kuposanso eniakenu.”—Marcia.
Muzithandiza anthu ena. Baibulo limati: “Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.” (Afilipi 2:4) Mukamakonda kuthandiza anthu ena sizingakuvuteni kuyamba kuona zinthu moyenera.
“Chibwenzi chikatha umangoona ngati palibenso chabwino ndipo ululu wake umaposa wina uliwonse. Koma ine ndaona kuti pakapita nthawi umadzaiwala ndipo zinthu zimayambiranso kuyenda bwino.”—Evelyn.