Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA

Kodi Ndafika Poti Nditha Kuchoka Pakhomo pa Makolo Anga?

Kodi Ndafika Poti Nditha Kuchoka Pakhomo pa Makolo Anga?

 

Kuchoka pakhomo pa makolo kumamveka kosangalatsa koma kumadetsanso nkhawa. Koma ungadziwe bwanji ngati wafika poti ungathe kukakhaladi pawekha?

N’chifukwa chiyani mukufuna kuchoka?

Mukhoza kukhala ndi zifukwa zambiri zoti muchokere pakhomo pa makolo anu. Zifukwa zina sizingakhale zomveka kwenikweni. Mwachitsanzo, mnyamata wina dzina lake Mario ananena kuti, “Ndinaganiza zosamuka pofuna kuthawa ntchito zapakhomo.”

Komatu zoona zake n’zakuti mukachoka pakhomo pa makolo anu m’pamene mumakhala opanikizika. Mtsikana wina wazaka 18 dzina lake Onya ananena kuti, “Ukasamuka, umakhala ndi udindo wosamalira nyumba yomwe ukukhalayo, kugula chakudya komanso kulipira mabilu. Ndipo zikatero sungauzenso makolo ako kuti akuthandize.”

 Mfundo yofunika kwambiri: Mukapeza chifukwa chimene mukufuna kuchokera pakhomopo, zingakuthandizeni kudziwa ngati mwakonzekadi kukakhala panokha.

Dziwiranitu ngati mungakwanitsedi

Yesu ananena kuti: “Ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja sayamba wakhala pansi ndi kuwerengera ndalama zimene adzawononge, kuti aone ngati ali ndi ndalama zokwanira kumalizira nsanjayo?” (Luka 14:28) Ndiye mogwirizana ndi lembali, mungadziwe bwanji ngati mungakwanitsedi kukhala panokha? Mfundo zili m’munsizi zingakuthandizeni.

KODI MUMAGWIRITSA NTCHITO NDALAMA MWANZERU?

Baibulo limati: “Ndalama zimatetezera.”​—Mlaliki 7:12.

  • Kodi zimakuvutani kusunga ndalama?

  • Kodi mumangogula zinthu mwachisawawa?

  • Kodi mumangokhalira kubwereka ndalama kwa anzanu?

Ngati mwayankha kuti inde kaya pa funso limodzi mwa mafunso amenewa, ndiye kuti simungakwanitse kukhala panokha.

Danielle ananena kuti: “Mchimwene wanga anachoka pakhomo ali ndi zaka 19. Koma chaka chisanathe n’komwe anali atapseratu. Analandidwa galimoto chifukwa cholephera kumalizitsa ndalama, anamutsekera khadi yogulira zinthu pangongole moti anayamba kuchonderera makolo kuti abwererenso kunyumba.”

Zimene mungachite panopa: Funsani makolo anu kuti akuuzeni kuchuluka kwa ndalama zomwe amawononga pamwezi. Amafunika kulipira zinthu ziti ndipo amapanga bwanji bajeti kuchokera pa ndalama zomwe amapeza? Nanga amakwanitsa bwanji kuti azitha kusungako ndalama zina?

Mfundo yofunika kwambiri: Mukadziwa kugwiritsa ntchito ndalama mosamala panopa, zidzakuthandizani mukadzakhala panokha.

KODI PANOKHA MUMATHA KUDZIWA ZOYENERA KUCHITA?

Baibulo limati: “Aliyense ayenera kunyamula katundu wake.”​—Agalatiya 6:5.

  • Kodi mumazengereza pochita zinthu?

  • Kodi mumachita kukumbutsidwa ndi makolo anu kuti mugwire ntchito zapakhomo?

  • Kodi nthawi zonse mumafika pakhomo mochedwa?

Ngati mwayankha kuti inde kaya pa funso limodzi mwa mafunso amenewa, ndiye kuti zingakuvuteni kwambiri ngati mutakhala panokha.

Jessica ananena kuti: “Ukayamba kukhala pawekha, pali zinthu zina zomwe sizikusangalatsa koma umangofunika kuti uzipangebe basi. Uyenera kuphunzira kuchita zinthu pawekha ndi kuzolowera.”

Zimene mungachite panopa: Yesani kugwira pafupifupi ntchito zonse za pakhomopo kwa mwezi wathunthu. Mwachitsanzo, mungamasese ndi kukolopa m’nyumba, kuchapa zovala zanu, kugula zinthu zina zofunika pakhomo, kuphika chakudya chamadzulo aliwonse komanso kutsukiratu mbale mukangomaliza kudya. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuti mudziwiretu zomwe muzidzachita mukasamuka.

Mfundo yofunika kwambiri: Mukaphunzira kuchita zinthu zofunika popanda kuuzidwa ndi winawake, simungadzavutike kukhala panokha.

Kuchoka pakhomo pa makolo usanakonzekere kuli ngati kujowa m’ndege usanaphunzire kugwiritsa ntchito palashuti

KODI MUMATHA KUUGWIRA MTIMA?

Baibulo limati: “Zonsezo muzitaye kutali ndi inu. Mutaye mkwiyo, kupsa mtima, kuipa, ndi mawu achipongwe.”​—Akolose 3:8.

  • Kodi zimakuvutani kuti muzigwirizana ndi anzanu?

  • Kodi simuchedwa kupsa mtima?

  • Kodi nthawi zonse mumangofuna kuti zinthu zichitike mmene inuyo mukufunira?

Ngati mwayankha kuti inde kaya pa funso limodzi mwa mafunso amenewa, ndiye kuti zingadzakuvuteni kukhala ndi munthu wina. Mwinanso mukadzakhala pabanja, muzidzalimbana ndi mwamuna kapena mkazi wanu.

Helena ananena kuti: “Nditayamba kukhala ndi anzanga m’pamene ndinadziwa kuti munthune ndili ndi vuto. Anzangawo ankalephera kuti azigwirizana nane chifukwa nthawi zina ndinkangopezeka kuti ndakwiya pazifukwa zosadziwika bwino. Ndinkafunika kuugwira mtima kuti ndizigwirizana nawo.”

Zimene mungachite panopa: Muziyesetsa kugwirizana ndi makolo komanso azibale anu. Zimene mumachita ndi anthu omwe mukukhala nawo pakhomo panopa, zingasonyeze zomwe muzidzachitanso ndi anthu omwe mudzakhale nawo mukadzachoka pakhomo pa makolo anu.

 Mfundo yofunika kwambiri: Zimafunika kukonzekera mokwanira kuti mudziimire panokha. Choncho musamaganize zochoka pakhomo la makolo anu ngati njira yothawira ntchito zapakhomo. Mungachite bwino kufunsa anzanu omwe akukhala pawokha panopa. Afunseni kuti mudziwe kuti ndi zinthu ziti zomwe amalakalaka akanapangiratu asanachoke pakhomo la makolo awo. Kufufuza zinthu mwa njira imeneyi n’kothandiza kwambiri musanasankhe zochita pa nkhani zikuluzikulu.