Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamachite Zinthu Mozengereza?

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamachite Zinthu Mozengereza?

Kodi mwatopa n’kumaliza ntchito zanu kapena homuweki yanu mochedwa nthawi zonse? Ngati zili choncho, mukufunika kuchitapo kanthu. Nkhani ino ikuthandizani kuti musiye kuchita zinthu mozengereza, ngakhale pamene

Mukamaliza kuwerenga nkhaniyi,  muyankhe mafunso okhudza kuchita zinthu mozengereza.

 Baibulo limafotokoza kuti kuchita zinthu mozengereza kuli ndi zotsatirapo zoipa. Limati: “Woyang’ana mphepo sadzabzala mbewu, ndipo woyang’ana mitambo sadzakolola.”​—Mlaliki 11:4.

 Taonani zinthu zina zimene zingachititse vutoli komanso zimene mungachite kuti musamazengereze mukafuna kuchita zinthu.

 Ntchitoyo ikuoneka kuti ndi yovuta.

 Kunena zoona, ntchito zina n’zovuta kwambiri moti nthawi zina zingaoneke kuti ndi bwino kungozisiya. Koma taonani mfundo zotsatirazi zomwe zingakuthandizeni.

  •   Muzigawa ntchitoyo m’magawo ang’onoang’ono. Mtsikana wina dzina lake Melissa anati: “Ngakhale ndikadziwa kuti ndachedwa kwambiri kumaliza ntchito inayake, ndimayesetsa kuchita chinthu chimodzi pa nthawi imodzi.”

  •   Muziyamba nthawi yomweyo. Mtsikana wina dzina lake Vera anati: “Mukangodziwa kuti mukufunika kugwira ntchito inayake, muziyamba nthawi yomweyo. Ngati muli kale ndi ntchito zina zambiri zoti muchite, muzilemba ntchitoyo pagulu la ntchito zimene mukufunika kugwira. Mungalembenso zimene mungachite kuti mumalize msanga ntchitoyo.”

  •   Muzipempha nzeru. N’kutheka kuti makolo anu komanso aphunzitsi anu anakumanapo ndi zimene mukukumana nazo, choncho mungachite bwino kuwapempha nzeru. Angakuthandizeni kuti mukonze bwino zinthu pa moyo wanu komanso angakuuzeni nzeru zimene zingakuthandizeni.

 Zimene zingakuthandizeni. Mtsikana wina dzina lake Abbey anati: “Muzilemba zimene mukufunika kuchita. N’zoona kuti pamafunika khama komanso kuchita zinthu mwadongosolo kuti muzitsatira zimene mwalembazo. Koma zimathandiza ndipo zinthu zimayenda bwino kwambiri chifukwa mumachita chilichonse pa nthawi yake.”

 Ntchitoyo ikuoneka kuti ndi yosasangalatsa.

 Nthawi zambiri ntchito imene mukufunika kugwira imaoneka kuti ndi yosasangalatsa. Zikatere, n’chiyani chingakuthandizeni kuti mugwirebe ntchitoyo? Tayesani kutsatira mfundo zotsatirazi.

  •   Muziganizira ubwino womaliza ntchitoyo mwachangu. Mwachitsanzo, mungaganizire mmene mungasangalalire mukamaliza ntchitoyo. Pa nkhaniyi, mtsikana wina wazaka 13 dzina lake Amy anati: “Ndimasangalala kwambiri ndikamaliza kugwira ntchito inayake pa nthawi yake kapena ndikamaliza msanga. Ndimakhala ndi mpata wopuma.”

  •   Muziganizira za kuipa kochita zinthu mozengereza. Mukamachita zinthu mochedwa, mumangodziwonjezera ntchito ndiponso mavuto ndipo zinthu sizingakuyendereni bwino. Baibulo limati: “Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.”—Agalatiya 6:​7.

  •   M’maganizo mwanu, muziona kuti tsiku limene mukufunika kumaliza ntchitoyo layandikira. “Zimandiyendera bwino ndikakonza zoti ndimalize ntchitoyo kutatsala tsiku limodzi kapena awiri kuchokera pa tsiku lenileni loyenera kumaliza ntchitoyo. Zimenezi zimandipatsa mpata woonanso bwinobwino ntchito imene ndagwirayo n’kukonza poyenera kukonza.”​—Anatero mtsikana wina dzina lake Alicia.

 Zimene zingakuthandizeni. “Zimangodalira mmene mukuganizira. Mumangofunika kudziuza kuti mukuyenera kumaliza ntchitoyo ndipo simulola kuti chilichonse chikulepheretseni. Ineyo ndikadziuza zimenezi, zinthu zimandiyendera bwino.”​—Anatero Alexis.

 Mwatanganidwa kwambiri ndi zinthu zina.

 Mnyamata wina wazaka 20 dzina lake Nathan, anati: “Nthawi zambiri anthu amandinena kuti ndimachita zinthu mozengereza, ndipo sizimandisangalatsa. Sadziwa kuti ndine munthu wotanganidwa kwambiri.” Ngati zimene Nathan wafotokozazi zimakuchitikirani, tayesani kutsatira mfundo izi.

  •   Muziyamba ndi ntchito zosavuta. Mtsikana wina dzina lake Amber anati: “Munthu wina anandiuzapo kuti ngati ntchito inayake ingatenge m’mphindi 5 kuti ithe, ndi bwino kuigwira nthawi yomweyo. Zimenezi ndi ntchito monga kusesa ndi kukolopa, kuyanika zovala, kutsuka mbale ndiponso kuimba foni.”

  •   Muziyamba kuchita zofunika kwambiri. Baibulo limati: “Muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.” (Afilipi 1:10) Kodi mfundo imeneyi mungaigwiritse ntchito bwanji pa moyo wanu? Mtsikana wina dzina lake Anna anati: “Ndimalemba zinthu zonse zimene ndikufunika kuchita komanso nthawi imene ndikufunika kumaliza. Koma chofunika kwambiri n’choti ndimalembanso nthawi imene ndikufunika kugwira ntchito iliyonse komanso nthawi imene ndikufunika kuimaliza.”

 Kodi zimenezi zikuoneka ngati zovuta kuchita? Zingaoneke choncho, koma si zovuta. Mfundo ndi yakuti mukalemba zimene mukufuna kuchita, mumagwiritsa ntchito nthawi mwanzeru m’malo mongochita zinthu mwachisawawa nthawi n’kukutherani. Zimenezi zimathandiza kuti musamapanikizike kwambiri. Mtsikana wina dzina lake Kelly anati: “Kulemba zimene ndikufunika kuchita kumandithandiza kuti ndizichita zinthu mtima uli m’malo.”

  •   Muzipewa zinthu zimene zingakudodometseni. “Ndisanayambe kugwira ntchito kapena kuchita zinthu zina, ndimauziratu aliyense kwathu kuti asandisokoneze. Ngati pali chinachake chimene abale anga akufuna kuti ndichite, ndimawapempha kuti andiuziretu ndisanayambe. Ndimathimitsanso foni yanga komanso chipangizo changa chilichonse chimene chingandisokoneze.”​—Anatero Jennifer.

 Zimene zingakuthandizeni. “Ntchito singathe yokha popanda kuigwira. Choncho ngati mukufunika kugwira ntchito inayake, igwireni ndipo musasiye mpaka mutaimaliza. Kuchita zimenezi kumathandiza chifukwa mumakhala ndi mpata wopuma mukamaliza ntchitoyo.”​—Anatero Jordan.