Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA

Mungatani Kuti Musamachite Manyazi Kwambiri?

Mungatani Kuti Musamachite Manyazi Kwambiri?

Vuto lake: Manyazi angakumanitseni zinthu zina ndipo simungapeze anzanu abwino.

Ubwino wake: Manyazi si oipa nthawi zonse. Amathandiza kuti munthu uziganiza usanalankhule, uziona zinthu moyenerera komanso uzimvetsera ena akamalankhula.

Mfundo yolimbikitsa: Pali zomwe mungachite kuti musakhale amanyazi kwambiri ndipo tikambirana zinthu zimenezi munkhaniyi.

 Kodi ndi zinthu ziti zimene mumaopa?

Munthu wamanyazi amaopa kulankhula ndi anthu pamasom’pamaso. Izi zingachititse kuti musapeze anzanu ambiri n’kumangokhala ngati muli m’chipinda chanokha chamdima. Zimenezi n’zoopsa kwambiri. Koma mukaganizira zimene mumaopa mutha kupeza kuti palibe chifukwa choopera. Taonani zinthu zitatu zimene ena amaopa.

 • Choyamba: “Ndimasowa nkhani zoti ndizikamba.”

  Zoona zake: Anthu sakumbukira kwambiri zimene mumalankhula koma mmene amamvera akakhala ndi inuyo. Mungachepetse mantha anu ngati mutakulitsa luso lanu lomvetsera, muzichita chidwi ndi zimene anthu ena amalankhula.

  Ganizirani izi: Kodi mumakonda munthu wotani, wolongolola amene sasowa chonena pa nkhani iliyonse kapena amene amamvetsera bwino wina akamalankhula?

 • Chachiwiri: “Anthu akhoza kuona kuti ndine wobowa.”

  Zoona Zake: Anthu amanenabe za munthu kaya ndi wamanyazi kapena ayi. Mukhoza kusiya kuopa zimenezi ndipo n’zotheka kuchititsa anthu kuti azinena zabwino za inuyo. Chongofunika ndi kuwapatsa mpata woti akudziweni bwino.

  Ganizirani izi: Mukamakhala ndi maganizo akuti anthu sakunena zabwino za inuyo, nthawi zina zimakhala kuti inuyo ndi amene mukuwaganizira zolakwika.

 • Chachitatu: “Ndikhoza kuchita manyazi kwambiri ngati nditanena zolakwika.”

  Zoona zake: Zimenezi zikhoza kuchitikira aliyense. Mukhoza kusiya kuopa zimenezi. Chongofunika ndi kuphunzira kudziseka nokha ngati mwalakwitsa zinazake.

  Ganizirani izi: Ngakhale inuyo, kodi simusangalala kukhala ndi anthu amene amavomereza kuti amalakwitsa zinthu zina?

Kodi mukudziwa? Anthu ena amaganiza kuti si amanyazi chifukwa choti amalemba kwambiri mameseji. Koma kuti munthu akhale mnzako weniweni pamafunika kukumana naye pamasom’pamaso. Wasayansi wina dzina lake Sherry Turkle analemba kuti: “Umunthu weniweni umaonekera tikakumana n’kumalankhulana uku tikuonana.” a

Mukasiya kuchita mantha, mudzayamba kuona kuti kucheza ndi anthu pamasom’pamaso sikukukuvutaninso ngati kale.

 Zimene Mungachite

 • Musamadziyerekezere ndi anthu ena. Musamafune kufanana ndi anthu ochangamuka kwambiri. Muzingoonetsetsa kuti simukuchita manyazi kwambiri n’cholinga choti zinazake zisakupiteni komanso muyambe kugwirizana ndi anthu.

  “Sikuti mufunika kukamba nkhani zambirimbiri kapena kukhala ngati muli kupate nthawi zonse. Umangofunika kuuza munthu wachilendo dzina lako, kenako n’kumufunsa mafunso angapo osavuta basi.”—Alicia.

  Mfundo ya m’Baibulo: “Koma aliyense payekha ayese ntchito yake kuti aone kuti ndi yotani. Akatero adzakhala ndi chifukwa chosangalalira ndi ntchito yake osati modziyerekezera ndi munthu wina.”—Agalatiya 6:4.

 • Muzikhala tcheru. Muziona zimene anthu ochezeka amachita akamalankhula ndi anthu. Kodi ndi zinthu ziti zimene zimawathandiza? Nanga ndi zinthu ziti zimene zimawavuta nthawi zina? Nanga ndi maluso ati amene ali nawo omwe mungafune kutengera?

  “Muziona zimene anthu amene savutika kupeza anzawo amachita. Muziona zimene amachita komanso zimene amalankhula akakumana ndi munthu koyamba.”—Aaron.

  Mfundo ya m’Baibulo: “Chitsulo chimanola chitsulo chinzake. Momwemonso munthu amanola munthu mnzake.”—Miyambo 27:17.

 • Muzifunsa mafunso. Anthu amakonda kufotokoza maganizo awo pa nkhani zosiyanasiyana choncho kufunsa mafunso kumathandiza kuti muyambe kucheza. Kumathandizanso kuti anthu asiye kuganizira kwambiri za inuyo.

  “Kukonzekereratu kungakuthandizeni kuti musamaope kwambiri. Mukhoza kuganizira nkhani zingapo zimene mungakambirane ndi anthu musanapite kokacheza, n’cholinga choti musakapanikizike mukakakumana ndi anthu achilendo.”—Alana.

  Mfundo ya m’Baibulo: “Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena”—Afilipi 2:4.

a Zachokera m’buku lakuti Reclaiming Conversation.