Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Kukhala ndi Ulemu N’kofunikadi?

Kodi Kukhala ndi Ulemu N’kofunikadi?

‘Palibe amene amanditsegulira chitseko, ndiye palibe chifukwa choti ineyo ndizitsegulira chitseko anthu ena.’

‘Pali zinthu zofunika kwambiri zoti ndiziganizira, osati mawu osafunika kwenikweni ngati akuti “chonde,” “zikomo” kapena “pepani.”’

‘Palibe chifukwa chosonyezera ulemu kwa abale anga. Ndife a pachibale basi.’

Kodi inuyo mukugwirizana ndi mfundo, ngakhale imodzi, pa mfundo zimene zili pamwambazi? Ngati zili choncho, ndiye kuti mwina simukudziwa zonse zokhudza kufunika kokhala ndi ulemu.

 Zimene muyenera kudziwa zokhudza kukhala ndi ulemu

 Kukhala ndi ulemu kungakuthandizeni pa mbali zitatu zotsatirazi:

 1.   Mbiri yanu. Anthu angakuoneni kuti ndinu munthu wabwino kapena ayi, potengera zimene mumachitira anthu ena. Ngati muli ndi ulemu, anthu angakuoneni kuti ndinu wokhwima nzeru, ndipo angamakusonyezeni ulemu. Koma ngati muli wamwano, anthu angaone kuti mumangoganizira zanu zokha. Zimenezi zingachititse kuti muvutike kupeza ntchito ndiponso musapeze mwayi wochita zinthu zina zimene zingakuthandizeni. Baibulo limati: “Munthu wankhanza amachititsa kuti thupi lake linyanyalidwe.”—Miyambo 11:17.

 2.   Ubwenzi wanu ndi ena. Baibulo limati: “Valani chikondi, pakuti chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu kwambiri kuposa chinthu china chilichonse.” (Akolose 3:14) Zimenezi ndi zoona, makamaka pa nkhani yokhudza ubwenzi ndi anthu ena. Anthu amakonda kucheza ndi munthu waulemu komanso wakhalidwe labwino. Koma palibe amene angafune kumacheza ndi munthu wamwano komanso wakhalidwe loipa.

 3.   Mmene anthu angamachitire nanu zinthu. Mtsikana wina dzina lake Jennifer anati: “Nthawi zonse ukamachita zinthu mwaulemu, m’kupita kwa nthawi, ngakhale anthu amwano kwambiri akhoza kusintha n’kuyamba kukulemekeza.” Koma zimenezi sizingachitike ngati inunso mumachita zinthu mopanda ulemu. Baibulo limati: “Muyezo umene mukuyezera ena, iwonso adzakuyezerani womwewo.”—Mateyu 7:2.

 Mfundo yofunika kwambiri: Tsiku ndi tsiku timafunika kulankhula kapena kuchita zinthu ndi anthu ena. Mmene mumachitira zinthu pa mbali imeneyi zingachititse kuti anthu azikulemekezani kapena ayi. Choncho kunena mwatchutchutchu, kukhala ndi ulemu n’kofunika kwambiri.

 Zimene mungachite kuti musinthe

 1.   Dzifufuzeni kuti mudziwe ngati mumasonyeza ulemu kwa ena. Dzifunseni mafunso ngati awa: ‘Kodi anthu akuluakulu ndimalankhula nawo mwaulemu? Kodi ndimalankhula kawirikawiri mawu ngati “chonde,” “zikomo” komanso “pepani”? Ndikamalankhula ndi ena, kodi ndimachitanso zinthu zina, monga muwerenga kapena kulemba mameseji? Kodi ndimasonyeza ulemu kwa makolo ndiponso abale anga, kapena ndimaona kuti ndi osafunika kuwasonyeza ulemu chifukwa ndi “abale anga”?’

   Baibulo limati: “Posonyezana ulemu, khalani patsogolo.”—Aroma 12:10.

 2.   Zimene mukufuna kuchita. Lembani zinthu zitatu zimene mukuona kuti mukufunikira kusintha. Mwachitsanzo, mtsikana wina wazaka 15, dzina lake Allison, anati: “Ndikufunika kumamvetsera kwambiri m’malo molankhula kwambiri.” David, wazaka 19, ananena kuti akufunika kupewa kuwerenga ndi kulemba mameseji akakhala ndi achibale ake kapena anzake. Iye anati: “Kuchita zimenezi n’kupanda ulemu. Zimakhala ngati ukuuza anthu amene uli nawowo kuti, sindikufuna kucheza ndi inuyo. Kuli bwino ndizicheza ndi amene ndikulemberana naye mamesejiwa.” Nayenso Edward, mnyamata wazaka 17, ananena kuti akufunika kusiya kudula mawu anthu ena akamalankhula. Ndipo Jennifer amene tamutchula poyamba uja ananena kuti akufunika kuyesetsa kumasonyeza ulemu kwa anthu akuluakulu. Iye anati: “Poyamba, ndinkangopereka moni mwachidule kenako n’kupitiriza kucheza ndi achinyamata anzanga. Koma panopa ndikuyesetsa kucheza ndi anthu achikulire kuti ndiwadziwe bwino. Zimenezi zandithandiza kwambiri kuti ndizichita zinthu mwaulemu.”

   Baibulo limati: “Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.”—Afilipi 2:4.

 3.   Muziona ngati pali kusintha. Kwa mwezi wathunthu, muziona ngati mukusintha pa nkhani ya malankhulidwe ndi zochita zanu. Mweziwo ukatha, dzifunseni kuti: ‘Kodi kukhala ndi ulemu kwathandiza kuti ndikhale munthu wabwinopo? Nanga ndi zinthu ziti zimene ndikufunikirabe kusintha?’ Mukatero, onani zimene mungachite kuti musinthe.

   Baibulo limati: “Zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muwachitire zomwezo.”—Luka 6:31.