Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA

Ndingatani Ngati Anzanga Amandiona Kuti Ndine Wotsalira?

Ndingatani Ngati Anzanga Amandiona Kuti Ndine Wotsalira?

“Ukakhala ndi anzako uzichita zimene iwowo amachita. Kupanda kutero sungapeze anzako, sungamasangalale komanso palibe chimene chingamakuyendere. Mapeto ake anzako akhoza kumakusala moti ungamasowe wocheza nawo.”—Carl.

Mwina mungaganize kuti mawu amenewa ndi ongokokomeza. Komabe, anthu ena akhoza kuchita chilichonse chomwe angathe pofuna kupewa mavuto omwe Carl watchula. Ngati nanunso mukuona kuti n’zoona, nkhaniyi ingakuthandizeni.

 N’chifukwa chiyani anthu amafuna kufanana ndi anzawo?

  • Samafuna kuti azisalidwa. “Nthawi ina, anzanga anaika zithunzi zawo pa intaneti zosonyeza akusangalala kumalo enaake. Ndinadabwa kwambiri moti sindinamvetse kuti n’chifukwa chiyani sanandiitane ndipo ndinayamba kuganiza kuti mwina ndine wosafunika.”—Natalie.

    ZOTI MUGANIZIRE: Kodi nthawi ina munasalidwapo ndi anzanu? Ndiye munachita zotani? Kodi kapena munayesa kusintha mmene mumachitira zinthu n’cholinga choti mufanane ndi anzanuwo?

  • Samafuna kuoneka osiyana ndi anzawo: “Makolo anga samafuna kuti ndikhale ndi foni. Anzanga akandipempha nambala yanga ya foni, ine n’kuwauza kuti ndilibe foni amandifunsa kuti: ‘Ulibe foni? Uli ndi zaka zingati?’ Ndikawauza kuti ndili ndi zaka 13, amandiyang’ana mondimvera chisoni.”—Mary.

    ZOTI MUGANIZIRE: Ndi malamulo ati amene makolo anu anakuikirani, omwe amakuchititsani kumva kuti ndinu osiyana ndi ena? Nanga inuyo mumakwanitsa kutsatira malamulowo?

  • Samafuna kuti anzawo aziwavutitsa: “Kusukulu ana samafuna kucheza ndi anzawo omwe amasiyana nawo zochita, zolankhula kapenanso chipembedzo. Ngati simufanana nawo pa zinthu zimenezi, angayambe kukuvutitsani.”—Olivia.

    ZOTI MUGANIZIRE: Kodi munachitiridwapo zankhanza chifukwa choti munachita zinthu mosiyana ndi anzanu? Nanga munachita zotani?

  • Samafuna kuti anzawo asiye kucheza nawo. “Ndinkayesetsa kutsatira chilichonse chomwe anzanga ankachita. Ndinkalankhula ngati mmene anzangawo ankalankhulira. Ndinkaseka nawo ngakhale pa zinthu zosaseketsa. Anzanga akamanyoza munthu wina, inenso ndinkalowerera ngakhale kuti ndinkadziwa kuti munthuyo akhumudwa.”—Rachel.

    ZOTI MUGANIZIRE: Kodi mumaona kuti chinthu chofunika kwambiri n’choti anzanu azikukondani? Kodi nthawi ina munasintha zochita zanu kuti muzichita zinthu mofanana ndi anzanuwo?

 Zimene muyenera kudziwa

  • Kumangotengera zochita za anthu ena kungakubweretsereni mavuto. Zimenezi zingachitike chifukwa anthu akhoza kuzindikirabe kuti mukungodziyerekezera ndi winawake. Brian wazaka 20 ananena kuti: “Ndinkati ndikafuna kudziyerekezera ndi anthu enaake a m’kalasi mwathu, sindinkafikapo. Ndimaona kuti ndi bwino kumangochita zinthu mmene umachitira basi chifukwa anthu amatha kuzindikira kuti ukungofuna kukhala ngati winawake.”

    ZOMWE MUNGACHITE: Muziganizira kwambiri zinthu zofunika. Baibulo limanena kuti: “Muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.” (Afilipi 1:10) Ndiye muzidzifunsa kuti, ‘Kodi chofunika kwambiri n’choti ndisamaoneke wotsalira ndikakhala ndi anthu amene amayendera mfundo zosiyana ndi zanga? Kapena ndizichita zinthu mmene ndimachitira nthawi zonse popanda kutengera ena?’

    “Ndimaona kuti n’kupanda nzeru kumangotengera zochita za anthu ena. Sizipangitsa kuti anthu azikukonda ndipo sizingakupangitse kukhala munthu wabwino.”—James.

  • Kumangotengera zochita za anthu ena kungakuchititseni kusintha makhalidwe anu. Zingakupangitseni kuti muzingoganizira zomwe mungachite kuti musangalatse anthu ena. Mnyamata wina dzina lake Jeremy ananena kuti: “Ndinkayesetsa kuchita chilichonse n’cholinga choti ndifanane ndi anzanga ngakhale zitakhala kuti zimenezo ziipitsa mbiri yanga. Zimenezi zinkandichititsa kuti ndizingokhala ngati chidole chifukwa ndinkangotsatira chilichonse chomwe anzangawo akufuna.”

    ZOMWE MUNGACHITE: Muzidziwa mfundo zomwe mumayendera ndipo muzizitsatira, m’malo momangosinthasintha ngati bilimankhwe amene amasintha maonekedwe potengera malo amene ali. Baibulo limanena kuti: “Usatsatire khamu pochita zoipa.”—Ekisodo 23:2.

    “Ndinkayesetsa kukonda chilichonse chomwe anzanga ankakonda monga nyimbo, magemu, zovala, mafilimu komanso zophodera . . . Ndinkafuna kumaoneka ngati anzangawo ndipo iwowo anazindikira kuti ndikungofuna kufanana nawo. Inenso ndinazindikira ndipo pamapeto pake zinandikhumudwitsa moti ndinkasowa wocheza naye. Ndinkangokhala ngati munthu wachabechabe basi. Ndinazindikira kuti si aliyense amene angamachite zinthu zofanana ndi iweyo kapena kukonda zimene umakonda. Koma zimenezi sizikutanthauza kuti musiye kufufuza anthu omwe angakhale anzanu. Zimangofunika kudekha komanso kudziwa kuti zimatenga nthawi kuti zimenezi zitheke.”—Melinda.

  • Kumangotengera zochita za ena kukhoza kuwononga khalidwe lanu. Mnyamata wina dzina lake Chris anafotokoza zimene zinkachitikira msuweni wake. Chris ananena kuti: “Msuweni wanga anasintha n’kuyamba kuchita zinthu zachilendo. Anayamba kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo n’cholinga choti azifanana ndi anzake. Sankatha kukhala popanda kugwiritsa ntchito mankhwalawa ndipo zimenezi zinatsala pang’ono kuwonongeratu moyo wake.”

    ZOMWE MUNGACHITE: Muzipewa anthu omwe zolankhula komanso khalidwe lawo zimasonyeza kuti satsatira mfundo za makhalidwe abwino. Baibulo limanena kuti: “Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru, koma wochita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.”—Miyambo 13:20.

    “Nthawi zina sikungakhale kulakwa kufuna kufanana ndi anzanu kuti musaoneke wotsalira. Koma zimenezi zisamakupangitseni kuchita zinthu zomwe mukudziwiratu kuti si zoyenera. Anzanu oganiza bwino angasangalale kukuonani mukuchita zinthu mmene mumachitira nthawi zonse.”—Melanie.

    Zimene zingakuthandizeni: Mukakumana ndi anthu atsopano omwe mukufuna kuti akhale anzanu, musamangoganizira za amene amakonda zinthu zofanana ndi zanu. Muziganiziranso za amene amatsatira mfundo zofanana ndi zanu pa zinthu zokhudza kutumikira Yehova komanso makhalidwe abwino.

    Si zovala zonse zomwe zingakukhaleni. Mofanana ndi zimenezi, si anthu onse omwe angagwirizane ndi mfundo zomwe mumayendera