ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA
Kodi Ndi Bwino Kumachita Zinthu Zingapo Nthawi Imodzi?
Kodi mumatha kuchita zinthu zingapo nthawi imodzi?
Kodi mumatha kuchita zinthu zingapo nthawi imodzi? Ambiri amaganiza kuti anthu amene akula akugwiritsa ntchito zipangizo zamakono sangavutike kuchita zinthu zingapo nthawi imodzi, kusiyana ndi anthu omwe zipangizo zamakono azidziwira ku ukulu. Koma kodi zimenezi ndi zoona?
ZOONA kapena ZABODZA?
Kuchita zinthu zingapo nthawi imodzi kumathandiza kuti munthu azichita zinthu mofulumira.
Ukamachita zinthu zingapo nthawi imodzi umazolowera moti sikhalanso nkhani.
Achinyamata savutika kuchita zinthu zingapo nthawi imodzi kusiyana ndi achikulire.
Ngati mwayankha kuti “inde” pa funso linalake pamwambapa, dziwani kuti nanunso muli ndi maganizo olakwika oti mukhoza kuchita zinthu zingapo nthawi imodzi.
Maganizo olakwika amene anthu amakhala nawo
Kodi mumaona kuti mukhoza kuchita zinthu ziwiri nthawi imodzi? Zikhoza kuthekadi kumachita zinthu zina nthawi imodzi popanda kusokonezeka. Mwachitsanzo, n’zotheka kumamvetsera nyimbo kwinaku mukukonza kuchipinda kwanu ntchitoyo n’kuyenda bwinobwino.
Koma ngati mukuchita zinthu ziwiri zomwe zimafuna kuganiza, zinthu ziwiri zonsezo zikhoza osayenda bwino. Mwina n’chifukwa chake mtsikana wina dzina lake Katherine ananena kuti kuchita zinthu zingapo nthawi imodzi “kumachititsa kuti munthu achite zinthu zosalongosoka.”
“Tsiku lina ndinkalankhula ndi munthu ndipo ndinalandira meseji yomwe ndinkafunika kuyankha nthawi yomweyo. Ndinkaganiza kuti ndikhoza kuchita ziwiri zonsezi nthawi imodzi. Koma zotsatira zake ndi zoti zambiri zimene munthuyo ananena zinandidutsa ndipo pafupifupi mawu onse omwe ndinalemba pamesejiyo anali olakwika.”—Caleb.
Katswiri woona za zipangizo zamakono, dzina lake Sherry Turkle analemba kuti: “Tikamachita zinthu zingapo nthawi imodzi, . . . maganizo athu amagawanika moti zonse zimene tikuchita siziyenda bwino. Zili choncho chifukwa ubongo wathu umakhala pa chintchito chachikulu moti tikamaganiza kuti zinthu zikuyenda bwino m’pamene timakhala tikuwononga zinthu.” a
“Nthawi zina ndimaganiza kuti ndikhoza kumalemba meseji kwinaku ndikulankhula ndi munthu. Koma mapeto ake zimapezeka kuti ndayamba kulankhula zimene ndimafunika kulemba pameseji, n’kumalemba zimene ndimafuna kulankhula.”—Tamara.
Anthu amene amachita zinthu zingapo nthawi imodzi amakhala ngati akuwazira nkhuni nkhwangwa yobuntha. Mwachitsanzo, zimawatengera nthawi yayitali kwambiri kuti amalize kulemba homuweki yawo. Kapena amazindikira kuti homuwekiyo sinalongosoke moti amafunika kuyambiranso kawiri. Mwachidule tingoti, anthu oterewa sakhala ndi nthawi yochita zimene akufuna chifukwa nthawi yawo imangothera kuchita chinthu chimodzimodzi.
Chimenechi n’chifukwa chake katswiri wina woona za maganizo, yemwenso amalangiza ana asukulu dzina lake Thomas Kersting, ananena kuti: “Ngati titayerekezera kuti ubongo wa munthu ndi kabati yosungira mabuku ofunika, ubongo wa munthu amene amachita zinthu zingapo nthawi imodzi ungakhale wofanana ndi kabati yomwe mabuku ake angoti balala.” b
“Munthu akamachita zinthu zambirimbiri nthawi imodzi, amazichita mongowaula. Mapeto ake amapezeka kuti akungodziwonjezera chintchito ndipo amawononga nthawi imene amaganiza kuti akuipulumutsa.”—Teresa.
Njira yomwe ingathandize
Mudziphunzitse kumachita chinthu chimodzi pa nthawi imodzi. Zimenezi zingakhale zovutirapo makamaka ngati munazolowera kuchita zinthu zingapo nthawi imodzi, mwachitsanzo kutumiza mameseji kwa anzanu kwinaku mukulemba homuweki. Baibulo limanena kuti, “muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.” (Afilipi 1:10) Si zinthu zonse zomwe timachita zomwe zili zofunika kwambiri. Choncho muzisankha ntchito yofunika kwambiri ndipo muzionetsetsa kuti maganizo anu onse ali pa zimene mukuchita mpaka mutamaliza.
“Nthawi zina ubongo wathu umangokhala ngati mwana wamng’ono. Tikamachita zinazake timafunika kumachita kudziletsa kuti tisayambe kuganizira zinthu zina.”—Maria.
Muzichotsa zinthu zomwe zingakusokonezeni. Kodi mukayamba kuwerenga mumalephera kupirira kuti musagwire foni yanu? Ngati ndi choncho, muziisiya pamalo oti isakusokonezeni. Muzithimitsanso TV ndipo musamaganizire zokhudza malo ochezera a pa intaneti. Baibulo limati: “Muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu.”—Akolose 4:5.
“Ndimaona kuti zinthu zimayenda bwino ndikamachita chinthu chimodzi pa nthawi imodzi. Ndimamva bwino kwambiri ndikapita pamene ndinalemba ntchito zoti ndigwire n’kuikhwatchapo kuti ndiyambe ntchito yotsatira. Ndikamachita zimenezi kumtima kwanga kumangoti mbee.”—Onya.
Muzikhala tcheru mukamalankhula ndi munthu. Kuyang’ana pafoni yanu kwinaku mukulankhula ndi munthu kungakusokonezeni ndiponso kungasonyeze kuti ndinu wopanda ulemu. Baibulo limanena kuti zinthu zimene tikufuna kuti ena atichitire, ifenso tiziwachitira zomwezo.—Mateyu 7:12.
“Nthawi zina ndikamalankhula ndi mchemwali wanga amandimvetsera akulemba mameseji kapena kuchita zinthu zina pafoni yake. Ndisanameyi, zimenezi zimandinyansa kwambiri. Koma ndinene zoona, nthawi zina nanenso ndimachita zomwezo.”—David.