Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Zomwe Ndiyenera Kudziwa pa Nkhani Yosuta Kapena Kuvepa

Zomwe Ndiyenera Kudziwa pa Nkhani Yosuta Kapena Kuvepa

 “M’dera lomwe ndimakhala, sizachilendo kupeza munthu yemwe sanakwanitse zaka 25 akusuta kapena kuvepa.”—Julia.

Zimene zili munkhaniyi

 Zimene muyenera kudziwa

 •   Fodya amapha ndithu. Fodya amakhala ndi nikotini yemwe ndi mankhwala oopsa kwambiri ndipo amachititsa kuti munthu azikhala ndi chibaba champhamvu. Malinga ndi bungwe la U.S. Centers for Disease Control and Prevention, “kusuta fodya kumachititsa kuti anthu ambiri azidwala matenda osiyanasiyana kapenanso kufa asanadyerere, zomwe ndi zopeweka.”

   “Ndimagwira ntchito monga dokotala wochita sikani ndipo ndimaona zithunzi za odwala omwe ziwalo zawo zina zinawonongeka chifukwa chosuta. Zimakhala zomvetsa chisoni kuona kuti mitsempha ya anthu omwe anasiya kusuta inafuchirira. Ndimalemekeza kwambiri thupi langa moti sindingayerekeze n’komwe kusuta.”—Theresa.

   Kodi mukudziwa? Ndudu za fodya zimakhala ndi mankhwala pafupifupi 7,000 ndipo ambiri mwa mankhwalawa amakhala oopsa kwambiri. Anthu mamiliyoni ambiri amamwalira chaka chilichonse chifukwa cha matenda obwera chifukwa chosuta.

 •   Anthu amene amavepa amakhala akulowetsa mankhwala oopsa m’thupi lawo. Anthu amene amavepa, kusuta ndudu zoyendera magetsi kapena batire amawononga mapapo awo kapenanso kumwalira kumene. Zili choncho chifukwa chakuti zovepera zambiri zimakhala ndi nikotini mofanana ndi ndudu za fodya. Buku lina lofotokoza zokhudza kuvepa linanena kuti popeza kuti nikotini amayambitsa chibaba champhamvu, “angachititse kuti achinyamata azingokhala ndi chibaba cha mankhwala ena osokoneza bongo.”

   “Fodya wina amene anthu amavepa amakoma ngati masiwiti kapenanso zipatso zina zimene ana ndi achinyamata amakonda. Choncho iwo amangotsatira kukomako m’malo moganizira mavuto ake.”—Miranda.

   Kodi mukudziwa? Nthunzi yomwe imatuluka anthu akamavepa simakhala ndi madzi okha koma mumakhalanso mankhwala ena oopsa kwambiri omwe nthawi zambiri amawononga mapapo.

 Mavuto amene amabwera chifukwa cha kusuta kapena kuvepa

 1.  (1) Anthu amene ubongo wawo sunakhwime amakhala ndi mavuto monga kulephera kuzindikira zinthu, kuvutika kuika maganizo pachinthu chimodzi komanso amangosinthasintha, pena asangalale pena akhumudwe

 2.  (2) Nkhama zimadyeka komanso mano amawola

 3.  (3) Chiwindi chimadyeka komanso amadwala matenda a mtima

   Matenda a asima ovuta kuchiritsika

   Kuvutika m’mimba komanso mseru

 Zimene mungachite

 •   Dziwani zoona zake. Musamangokhulupirira zilizonse zimene anthu akunena. Mwachitsanzo, ena anganene kuti kuvepa sikoopsa kwenikweni kapenanso kuti kuvepa kumathandiza kuti munthu achepetse nkhawa. Muzifufuza panokha n’kusankha zoyenera kuchita.

   Mfundo ya m’Baibulo: “Munthu amene sadziwa zambiri amakhulupirira mawu alionse, Koma wochenjera amaganizira zotsatira za zimene akufuna kuchita.”—Miyambo 14:15.

   “Ukamaganizira mavuto amene amabwera chifukwa chosuta kapenanso kuvepa, umazindikira kuti zinthu zimene anthu otchuka kapena anzako amaziona ngati ‘zosangalatsa’ sizikhala zosangalatsa kwenikweni koma amakhala akudziputira mavuto aakulu.”—Evan.

   Zoti muganizire: Kodi achinyamata amene amasuta kapenanso kuvepa, amakhaladi osangalala? Kodi ndi okonzeka kupirira mavuto amene angakumane nawo panopa kapenanso m’tsogolo? Kapena amangokhala akufesa mbewu za mavuto omwe angadzakolole kutsogolo?

 •    Muzipeza njira zabwino zothetsera nkhawa zanu. Njira zabwino kwambiri zochepetsera nkhawa ndi kuchita zinthu monga masewera olimbitsa thupi ndiponso kuwerenga kapena kucheza ndi anzanu abwino omwe angakulimbikitseni. Mukakhala ndi zinthu zabwino zambiri zoti muchite, simungaganizirenso zofuna kusuta.

   Mfundo ya m’Baibulo: “Nkhawa mumtima mwa munthu ndi imene imauweramitsa, koma mawu abwino ndi amene amausangalatsa.”—Miyambo 12:25.

   “Anthu amaganiza kuti kusuta komanso kuvepa kumathandiza kuti athetse nkhawa. Koma zoona zake n’zoti munthu amangopepukidwako kwa kanthawi kochepa chabe koma mavuto amene amakhalapo ndi amoyo wonse. Njira zabwino zochepetsera nkhawa zilipo zambiri.”—Angela.

   Zoti muganizire: “Kodi ndi zinthu zinanso ziti zimene zingakuthandizeni kuchepetsa nkhawa? Onani “Zimene Achinyamata Amadzifunsa” nkhani yakuti “N’chiyani Chingandithandize Ndikakhala Ndi Nkhawa?

Kudalira kusuta kapena kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo n’cholinga chofuna kuthana ndi nkhawa kumangowonjezera mavuto chifukwa kuli ngati kudumphira m’nyanja pofuna kuusa mvula.

 •    Khalani okonzeka kukana kukakamazidwa ndi anzanu. Mungakakamizike ndi anzanu akusukulu kapenanso chifukwa cha zosangalatsa zomwe mumakonda. Mafilimu, mapologalamu a pa TV kapenanso zimene anthu amaposita pamalo ochezera a pa intaneti zimachititsa kuti anthu aziona ngati kusuta ndi kuvepa n’kosangalatsa ndipo kulibe vuto lililonse.

   Mfundo ya m’Baibulo: “Anthu aakulu mwauzimu . . . amatha kusiyanitsa zoyenera ndi zosayenera chifukwa choti amagwiritsa ntchito luso lawo la kuganiza.”—Aheberi 5:14.

   “Pa nthawi imene ndinali kusukulu, anzanga ambiri ankandilemekeza chifukwa choti sindinkasuta komanso kuvepa. Nditawauza momveka bwino kuti sindingasute kapenanso kuvepa anzangawo ankanditeteza. Choncho ngakhale kuti zingaoneke zochititsa mantha, koma kufotokozeratu maganizo anu kungakutetezeni kwambiri.”—Anna.

   Zoti muganizire: Kodi mungakwanitse kukana kutengera zochita za anzanu? Kodi mukukumbukira nthawi imene munakana kuchita nawo zimenezo? Ngati mukufuna thandizo pa nkhani imeneyi onani gawo lakuti “Mmene Mungakonzekerere” mu buku la Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa buku Lachiwiri, mutu 15.

 •   Muzisankha mosamala anthu oti muzicheza nawo. Ngati anzanu amaona kuti kusuta kapena kuvepa n’koipa inunso simungavute kupewa kuchita zimenezi.

   Mfundo ya m’Baibulo: “Uzicheza ndi anthu anzeru, ndipo iwenso udzakhala wanzeru. Sankha kumacheza ndi zitsiru ndipo udzakumana ndi mavuto.”—Miyambo 13:20, Easy-to-Read Version.

   “Kukhala ndi anzako omwe ali ndi makhalidwe monga kudziletsa komanso kukhulupirika n’kothandiza kwambiri. Ukamaona kuti zinthu zikuwayendera bwino, nawenso umafunitsitsa kukhala ngati iwowo.”—Calvin.

   Zoti muganizire: Kodi anzanu apamtima amagwirizana ndi zimene munasankha kuti simukufuna kusuta komanso mukufuna kumakhala moyo wabwino kapena amakufooketsani?

 Kodi kusuta chamba n’kulakwa?

 Anthu ambiri amanena kuti chamba si choopsa. Koma limeneli ndi bodza lamkunkhunidza.

 •   Achinyamata amene amasuta chamba amakhala pangozi yokhala ndi chibaba champhamvu. Kafukufuku akusonyeza kuti chamba chimatha kuwonongeratu ubongo zomwe zingachititse kuti nzeru zichepe.

 •   Bungwe lina loona za mankhwala osokoneza ubongo ku United States linanena kuti “kafukufuku akusonyeza kuti anthu amene amasuta chamba amakhala ndi mavuto m’banja, amalephera kusukulu, amavutika kupeza ntchito yabwino komanso sakhutira ndi moyo wawo.”—U.S. Substance Abuse and Mental Health Services Administration.

   “Ndinkafuna kusuta chamba poganiza kuti chindithandiza kuchepetsa nkhawa. Koma nditaganizira mavuto amene ndingakumane nawo monga kukhala ndi chibaba champhamvu, kuchuluka kwa ndalama zomwe ndingawononge, komanso mmene zingakhudzire thanzi langa, ndinazindikira kuti kusuta chamba kutha kungondiwonjezera nkhawa.”—Judah.