Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndi Mnzanga Chabe Kapena Amandifuna?​—Gawo 1: Kodi Ndikuona Zizindikiro Zotani?

Kodi Ndi Mnzanga Chabe Kapena Amandifuna?​—Gawo 1: Kodi Ndikuona Zizindikiro Zotani?

Munthuyo amakusangalatsani kwambiri ndipo mukuona kuti nayenso amasangalala nanu. Mumalemberana mameseji nthawi zonse, mumakonda kucheza awiri mukakhala pa gulu la anzanu ndipo mameseji ena amene munthuyo amakulemberani amasonyeza kuti amakufunani.

Ndiyeno mwaona kuti ndi bwino kumufunsa kuti mutsimikizire ngati amakufunanidi. Koma munthuyo akuyankha kuti, “Ndiwe mnzanga chabe.”

 Mmene mungamvere

“Ndinamukwiyira kwambiri komanso ndinadzimvera chisoni. Tinkalemberana mameseji tsiku lililonse ndipo ankaoneka kuti amandiganizira kwambiri. Kenako nanenso ndinayamba kumukonda.”​—Jasmine.

“Ine ndi mtsikana wina tinkakonda kuperekeza anthu enaake awiri amene anali pa chibwenzi. Nthawi zina zinkangokhala ngati ine ndi mtsikanayo tinalinso pa chibwenzi. Tinkacheza kwambiri ndipo tinayamba kumalemberana mameseji. Zinandivuta kuvomereza mtsikanayo atandiuza kuti amangonditenga ngati mnzake basi ndipo nthawi yonseyi n’kuti ali pa chibwenzi ndi munthu wina.”​—Richard.

“Mnyamata wina ankandilembera mameseji tsiku lililonse ndipo nthawi zina tinkalemberana zokopana. Nditamuuza kuti ndimamukonda, anayamba kuseka n’kundiuza kuti, ‘Sindikufuna kukhala pa chibwenzi ndi aliyense panopa.’ Atandiuza zimenezi ndinalira kwa nthawi yaitali.”​—Tamara.

Mfundo yofunika kwambiri: Aliyense akhoza kukhumudwa, kuchita manyazi komanso kumva kuti wapusitsidwa ngati ataona kuti akukondana ndi munthu winawake kenako n’kuzindikira kuti munthuyo sakumukonda. Mnyamata wina dzina lake Steven anati: “Ndinakhumudwa kwambiri nditazindikira kuti munthu amene ndinkamukonda, sankandikonda. Zinanditengera nthawi kuti ndiyambenso kukhulupirira munthu wina.”

 Zimene zimayambitsa

Mukamalemberana mameseji ndi munthu zimakhala zosavuta kuti muyambe kumukonda ngakhale kuti iyeyo sakukufunani. Tiyeni tione zimene achinyamata ena ananena pa nkhaniyi.

“Munthu akhoza kumakulemberani mameseji pofuna kungotayitsa nthawi koma inuyo n’kumaganiza kuti akukufunani. Ndipo ngati amakulemberani tsiku lililonse mukhoza kuyamba kuganiza kuti amakukondani kwambiri.”​—Jennifer.

“Munthu wina akhoza kukhala wokonzeka kuyamba chibwenzi pomwe winayo akungofuna munthu woti azicheza naye n’cholinga choti adziwe kuti alipo omwe angamukonde.”​—James.

“Munthu akakulembera meseji yoti ‘ugone bwino’ ukhoza kuganiza kuti amakufuna pamene iyeyo sanaganize n’komwe zimenezo potumiza mesejiyo.”​—Hailey.

“Munthu akatumiza kachithunzi ka nkhope yomwetulira akhoza kukhala kuti akungofuna kucheza nanu kapena akufuna kukukopani. Koma nthawi zina munthu wolandira mesejiyo amafulumira kuganiza kuti akumukopa.”​—Alicia.

Mfundo yofunika kwambiri: Musamafulumire kuganiza kuti munthu akamakonda kucheza nanu ndiye kuti amakufunani.

Koma kuchita zimenezi si kophweka. Baibulo limati: “Mtima ndi wonyenga kwambiri kuposa china chilichonse ndipo ungathe kuchita china chilichonse choipa.” (Yeremiya 17:9) Mtima ukhoza kukuchititsani kuganiza kuti muli pa chibwenzi ndi winawake pamene si zili choncho.

 Zimene mungachite

  • Muzionetsetsa mmene zinthu zilili. Muziganizira mofatsa mmene mumachezera ndi munthuyo n’kumadzifunsa kuti, ‘Kodi ndili ndi zifukwa zomveka zondichititsa kuganiza kuti munthuyu amandikonda kuposa anthu ena?’ Musalole kuti mutengeke kwambiri n’kumalephera kuganiza bwino.​—Aroma 12:1.

  • Muzikhala ozindikira. Mwina pali zizindikiro zina zimene zimakuchititsani kuganiza kuti mukuyamba chibwenzi. Koma m’malo momangoganizira zimenezi, muyenera kuganizira kwambiri zizindikiro zimene zimakuchititsani kukayikira zimenezo. Musamangoganiza kuti mukayamba kukonda munthu winawake ndiye kuti nayenso amakukondani.

  • Muzidekha. Musalole kuti muzimukonda kwambiri munthuyo pokhapokha atakuuzani yekha kuti akufuna kuti mukhale naye pa chibwenzi.

  • Muzilankhula moona mtima. Baibulo limanena kuti pali “nthawi yolankhula.” (Mlaliki 3:7) Ngati mukufuna kudziwa ngati munthu wina amakukondanidi, muzimufunsa maganizo ake. Mtsikana wina dzina lake Valerie ananena kuti: “Ngakhale kuti zimapweteka, ndi bwino kudziwa mwamsanga kuti munthuyo sakukufunani kusiyana ndi kupitiriza kumaganiza kuti muli naye pa chibwenzi kenako n’kudzazindikira mochedwa kuti samakufunani.”

Mfundo yofunika kwambiri: Lemba la Miyambo 4:23 limanena kuti “uteteze mtima wako.” Ndiye ngati mwayamba kukonda munthu winawake muyenera kufufuza ngati nayenso amakukondani. Mukalola kuti mupitirize kukonda munthu musanadziwe ngati nayenso amakukondani, zimakhala ngati mukubzala mbewu pamwala.

Ngati mwaona kuti munthuyo amakukondanidi ndipo ndinu okonzeka kukhala pa chibwenzi, mukhoza kusankha kukhala naye pa chibwenzi kapena ayi. Muzikumbukira kuti banja limakhala lolimba ngati mwamuna ndi mkazi amafuna kuchita zinthu zofanana potumikira Yehova komanso ngati amakambirana zinthu moona mtima. (1 Akorinto 7:39) Ndipo zinthu zimayenda bwino kwambiri ngati munthu amaona kuti mwamuna kapena mkazi wake ndi mnzake wapamtima.​—Miyambo 5:18.