Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA

Ndingatani Kuti Ndichepetse Thupi?

Ndingatani Kuti Ndichepetse Thupi?

 Kodi ndikufunika kuchepetsadi thupi?

Achinyamata ambiri amanena kuti akufuna kuchepetsa thupi lawo. Koma zoona zake n’zakuti . . .

 • Ambiri amadera nkhawa za mmene akuonekera osati thanzi lawo. Achinyamata ena amasala zakudya kapenanso kumwa mankhwala pofuna kuchepetsa thupi lawo mofulumira. Koma zimenezi n’zosathandiza ndipo nthawi zina zimaika moyo wawo pangozi.

  “Atsikana ena amadzilanga ndi njala n’cholinga choti achepetse thupi lawo mofulumira. Koma zimenezi zimangowabweretsera mavuto ndipo pamatenga nthawi kuti thupi lawo libwererenso mmene linalili.”—Hailey.

 • Ambiri amene amafuna atachepetsa thupi lawo sikuti amakhaladi onenepa. Achinyamata oterewa amadziona kuti ndi onenepa akamadziyerekezera ndi achinyamata anzawo kapena potengera zimene otsatsa malonda amanena.

  “Ndili ndi zaka 13 ndinkadziyerekezera ndi anzanga. Ndinkaganiza kuti anzangawo akhoza kumandikonda kwambiri ndikamaoneka ngati iwowo. Zimenezi zikanachititsa kuti ndionde mpaka kumaoneka ngati kamtengo.”—Paola.

Komabe, pali achinyamata ena omwe amafunikiradi kuchepetsa thupi. Mwachitsanzo, lipoti la Bungwe Loona za Umoyo Padziko Lonse limasonyeza kuti . . .

 • Padziko lonse, achinyamata pafupifupi 340 miliyoni azaka zapakati pa 5 ndi 19 ndi onenepa kwambiri.

 • Mu 1975, anthu 4 okha pa anthu 100 alionse azaka zapakati pa 5 ndi 19, ndi omwe anali onenepa kwambiri. Koma pofika mu 2016 chiwerengerochi chinakwera kufika pa anthu 18 pa 100 alionse.

 • M’mayiko ambiri, anthu onenepa kwambiri amakhala ochuluka tikayerekezera ndi anthu oonda.

 • Anthu onenepa kwambiri amapezekanso m’mayiko osauka, ngakhale m’mabanja omwe sakwanitsa kugula zakudya zopatsa thanzi.

 Kodi njira yabwino yochepetsera thupi ndi iti?

Inuyo mungasankhe njira iti?

 1. Kudzimana zakudya.

 2. Kuchita masewera olimbitsa thupi komanso kudya zakudya zamagulu onse.

 3. Kumwa mankhwala ochepetsa thupi.

Yankho lolondola: Njira ya nambala 2: Kuchita masewera olimbitsa thupi komanso kudya zakudya zamagulu onse.

N’zoona kuti kusala zakudya kapena kusiya kudya zakudya zina kungasinthe zinthu mwachangu. Koma kuchita zimenezi kungawononge thanzi lanu ndipo ngati nthawi ina mutadzayambiranso kudya ngati poyamba, mukhoza kudzanenepa kwambiri.

Komabe, ngati mutakhala ndi cholinga choti mukhale wathanzi, mukhoza kumaoneka bwino komanso kumasangalala. Dr. Michael Bradley ananena kuti: “Ngati mukufuna kukhala ndi thanzi labwino komanso kuti zinthu zizikuyenderani bwino . . . muzisintha zina ndi zina pa moyo wanu ndipo muzichita zomwe mungazikwanitse kwa moyo wanu wonse.” * Apa mfundo ndi yakuti, mukafuna kuchepetsa thupi musamaganize zosiya kudya zakudya zina koma muzisintha mmene mumachitira zinthu pa moyo wanu.

 Zimene mungachite

Baibulo limatiuza kuti tizichita zinthu “mosapitirira malire” ndipo zimenezi zikuphatikizapo kudya. (1 Timoteyo 3:11) Ndipo limanenanso mosapita m’mbali kuti tiyenera kupewa kudya kwambiri. (Miyambo 23:20; Luka 21:34) Poganizira mfundo zimenezi, tayesani kuchita zinthu zotsatirazi kuti mukhale ndi moyo wathanzi:

 • Muzidziwa zomwe zimafunika kuti chakudya chikhale chopatsa thanzi.

  Simuyenera kumangokakamira zakudya zomwe mumakonda. Koma muzidziwanso zinthu zina zokhudza zakudya ndipo izi zingakuthandizeni kuti muzidya zakudya zopatsa thanzi. Ndipotu njira ina yabwino yochepetsera thupi, ndi kudya zakudya zamagulu onse.

 • Muzichita masewera olimbitsa thupi nthawi zonse.

  Ganizirani zomwe mungamachite tsiku lililonse kuti mukhalebe athanzi. Mwachitsanzo, m’malo mokwera chikepi, muzikwera masitepe. Ndipo m’malo moti muzisewera magemu pafoni kapena pakompyuta kwa 30 minitsi, muzikawongolako miyendo.

 • Muzidya zakudya zopatsa thanzi m’malo mwa zakudya zosafunika.

  Mtsikana wina dzina lake Sophia ananena kuti: “Ndimayesetsa kusunga zakudya zina zopatsa thanzi monga zipatso komanso zakudya zamasamba. Zimenezi zimandithandiza kuti ndizidya zakudya zopatsa thanzi nthawi zonse.”

 • Muzidya pang’onopang’ono.

  Anthu ena amadya mofulumira kwambiri moti amalephera kumva kuti akhuta. Choncho muzidya pang’onopang’ono. Ndipo muzipuma kaye musanakatenge chakudya china chowonjezera. Mukhoza kuzindikira kuti mulibenso njala ngati mmene mumaganizira.

 • Muzidziwa kuchuluka kwa zinthu zonenepetsa zomwe zimapezeka mu zakudya.

  Muziwerenga malangizo osonyeza kuchuluka kwa zinthu zonenepetsa zomwe zili mu zakudya zomwe mwagula. Mwachitsanzo: Zakumwa zoziziritsa kukhosi, zakudya zokhala ndi mafuta ambiri komanso zakudya zina zotsekemera, zingakuchititseni kuti munenepe kwambiri.

 • Muzikhala ndi malire.

  Sara yemwe ndi wazaka 16 ananena kuti: “Nthawi ina ndinkangokhalira kuganizira kuchuluka kwa zinthu zonenepetsa zomwe zili m’chakudya changa.” Koma simuyenera kufulumira kuda nkhawa. Nthawi zina mukhoza kudya zakudya zokhala ndi tinthu tonenepetsa, koma chisamakhale chizolowezi.

Zimene zingakuthandizeni: Auzeni adokotala kuti mukufuna kuchepetsa thupi. Ndipo adokotalawo akhoza kukuthandizani kudziwa ndandanda yabwino yomwe mungatsatire kuti zomwe mukufunazo zitheke.

^ ndime 25 Kuchokera m’buku lakuti When Things Get Crazy With Your Teen.