Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndimangokhalira Kuganizira za Maonekedwe Anga?

Kodi Ndimangokhalira Kuganizira za Maonekedwe Anga?

 Mafunso amene angakuthandizeni

 1.   Kodi ndi chiganizo chiti chimene chikugwirizana ndi mmene mumadzionera?

  •  Sindimasangalala ndi mmene ndimaonekera.

  •  Nthawi zina ndimasangalala ndi mmene ndimaonekera.

  •  Nthawi zonse ndimasangalala ndi mmene ndimaonekera.

 2.   Kodi n’chiyani chimene mungafunitsitse mutasintha pa thupi lanu?

  •  Kutalika

  •  Kunenepa

  •  Mmene thupi lanu linaumbidwira

  •  Tsitsi

  •  Kaonekedwe ka khungu

  •  Kukula kwa masozi

  •  Zina

 3.   Malizitsani kulemba chiganizo chotsatirachi.

   Sindimasangalala ndi mmene ndimaonekera . . .

  •  Ndikakwera pasikelo.

  •  Ndikayang’ana pagalasi.

  •  Ndikadziyerekezera ndi anthu ena (anzanga, anthu oonetsedwa pamafashoni, anthu a m’mafilimu).

 4.   Malizitsani kulemba chiganizo chotsatirachi.

   Ndimakwera pasikelo . . .

  •  Tsiku lililonse.

  •  Mlungu uliwonse.

  •  Pakapita nthawi.

 5.   Kodi ndi mawu ati amene akugwirizana ndi mmene mumamvera?

  •  Sindisangalala ndi mmene ndimaonekera. (Mwachitsanzo, mtsikana wina dzina lake Serena ananena kuti: “Nthawi iliyonse ndikadziyang’anira pagalasi, ndimaona kuti ndine chimunthu chonenepa kwambiri komanso chosaoneka bwino. Moti nthawi zina ndimadzizunza ndi njala kuti ndichepeko thupi.”)

  •  Sindikhumudwa ndi mmene ndimaonekera. (Mwachitsanzo, mtsikana wina dzina lake Natanya ananena kuti: “N’zoona kuti pamakhala zinthu zina zokhudza maonekedwe athu zimene sizitisangalatsa koma timangofunika kuvomereza kuti ndi mmene tinabadwira. Kungakhale kupanda nzeru kumadandaula ndi zinthu zimene sitingathe kuzisintha.”)

 Baibulo limatiuza kuti tisamadziganizire kuposa ‘mmene tiyenera kudziganizira.’ (Aroma 12:3) N’zoona kuti sikulakwa ndipo ndi zofunika kumaganizira mmene timaonekera. N’chifukwa chake timachita zinthu zodzisamalira monga kutsuka m’kamwa komanso kukhala aukhondo.

 Komabe sibwino kumaganizira monyanyira za maonekedwe athu.Komano kodi mungatani ngati nthawi zambiri simusangalala ndi mmene mumaonekera? Mwina munadzifunsapo funso lakuti. . .

 ‘N’chifukwa chiyani sindisangalala ndi mmene ndimaonekera?’

 Pakhoza kukhala zifukwa zambiri. Zina mwa zifukwazo zikhoza kukhala:

 •  Mauthenga a pa TV ndi malo ena. “Mauthenga ambiri a pa TV kapena pa zipangizo zina amasonyeza kuti wachinyamata ayenera kukhala wochepa thupi kwambiri komanso nthawi zonse azioneka wokopa. Ndiye ukakhala kuti ndiwe wonenepa komanso suoneka mokopa zimapangitsa kuti usamasangalale ndi mmene umaonekera.”—Kellie.

 •  Makolo. “Ndinaona kuti ngati mayi amangokhalira kuganizira za maonekedwe awo ananso amachita chimodzimodzi. Izi zimachitikanso ngati bambo amangokhalira kuganizira za maonekedwe awo. Nawonso ana aamuna amachita chimodzimodzi.”—Rita.

 •  Kudzikayikira. “Anthu amene amangokhalira kuganizira mmene amaonekera amafuna kuti nthawi zonse anthu aziwauza kuti akuoneka bwino kapena atchena. Zimakhala zotopetsa kukhala ndi anthu otere.”—Jeanne.

 Mosasamala kanthu za chifukwa chimene chimapangitsa kuti musamasangalale ndi mmene mumaonekera, mwina mukhoza kumadzifunsabe kuti . . .

 ‘Kodi ndisinthe mmene ndimaonekera?’

 Taonani zimene achinyamata anzanu ananena.

 “Sungathe kusintha zinthu zonse zimene sizikusangalatsa zokhudza mmene umaonekera. Choncho ndi bwino kungovomereza kuti ndi mmene unabadwira. Ndipo ukavomereza mmene umaonekera, anthunso amangokuona mmene ulili basi.”—Rori.

 “Ndi bwino kuchita zonse zimene ungathe kuti ukhale ndi thanzi labwino. Ukakhala ndi thanzi labwino umaoneka mmene unafunikira kuonekera. Ndipo ngati munthu wina sangamasangalale ndi khalidwe lako labwino koma kumafuna kuti uzioneka mmene iyeyo akufunira, ameneyo si mnzako wabwino.”—Olivia.

 Mfundo yofunika kuikumbukira: Muzichita zonse zimene mungathe kuti muzioneka bwino. Koma musamadandaule ndi zinthu zimene simungathe kuzisintha. Kudera nkhawa kwambiri ndi mmene mumaonekera kungakubweretsereni mavuto aakulu. (Onani mutu wakuti “ Zimene Julia Ananena.”)

 Kuganizira moyenerera mmene mumaonekera kungakuthandizeni kuti muzisangalala ndi mmene mumaonekera. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zimene zinachitikira mtsikana wina dzina lake Erin. Iye ananena kuti: “N’zoona kuti pali zinthu zina zokhudza mmene ndimaonekera zimene sindisangalala nazo. Koma ndikuona kuti ndimakhumudwa kwambiri ndikamaganizira kwambiri zinthu zimene sizindisangalatsa. Panopa ndimaonetsetsa kuti ndikuchita masewera olimbitsa thupi nthawi ndi nthawi komanso ndikudya moyenerera. Kuchita zimenezi kumandithandiza kuti ndizisangalala ndi mmene ndimaonekera.”

 Malangizo amene angakuthandizeni

 Mukamaganizira moyenera mmene mumaonekera mumasangalala komanso mumaoneka bwino. Baibulo lingakuthandizeni pa nkhani imeneyi ndipo likukulimbikitsani kuchita zinthu zotsatirazi:

 •  Kukhala wokhutira. “Kuona ndi maso kuli bwino kuposa kulakalaka ndi mtima. Izinso n’zachabechabe ndipo zili ngati kuthamangitsa mphepo.”—Mlaliki 6:9.

 •  Kuchita masewera olimbitsa thupi moyenera. “Kuchita masewera olimbitsa thupi n’kopindulitsa pang’ono.”—1 Timoteyo 4:8.

 •  Kukhala ndi Khalidwe labwino. “Munthu amaona zooneka ndi maso, koma Yehova amaona mmene mtima ulili.”—1 Samueli 16:7.

 “Mmene nkhope yathu imaonekera zimasonyeza mmene timamvera muntima. Ngati munthu amasangalala ndi mmene amaonekera, anthu ena amazindikira zimenezo ndipo amasangalala kucheza naye.”—Sarah.

 “N’zoona kuti anthu akhoza kutengeka nawe mwansanga chifukwa cha maonekedwe ako. Koma anthu amakukumbukira kwambiri chifukwa cha umunthu wako komanso khalidwe lako labwino.”—Phylicia.

 Onaninso Miyambo 11:22; Akolose 3:10, 12; 1 Petulo 3:3, 4.