Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA

Kodi Baibulo Lingandithandize Bwanji?​—Gawo 2: Zimene Mungachite Kuti Kuwerenga Baibulo Kuzikusangalatsani

Kodi Baibulo Lingandithandize Bwanji?​—Gawo 2: Zimene Mungachite Kuti Kuwerenga Baibulo Kuzikusangalatsani

 Mnyamata wina dzina lake Will ananena kuti: “Ndimaona kuti kuwerenga Baibulo kukhoza kukhala kosasangalatsa ngati sukudziwa njira yabwino yoti utsatire poliwerenga.”

 Kodi mungakonde kudziwa zimene mungachite kuti kuwerenga Baibulo kuzikusangalatsani? Nkhaniyi ingakuthandizeni.

 Muziyerekezera kuti mukuona zomwe zikuchitika m’nkhaniyo

 Mukamawerenga nkhani inayake, muzikhala ngati kuti inuyo munali pompo. Tayesani kuchita izi:

  1.   Sankhani nkhani ya m’Baibulo imene mukufuna muiphunzire. Mungasankhe nkhani ina yake yomwe inachitika kaya yopezeka m’mauthenga abwino kapenanso nkhani ya m’Baibulo yowerengedwa mwasewero pa jw.org.

  2.   Werengani nkhaniyo. Mukhoza kuwerenga nkhaniyo panokha, mungaiwerengenso mokweza mawu limodzi ndi anzanu kapena anthu a m’banja lanu. Wina akhoza kutenga mbali ya wofotokozera, pamene enawo akhoza kutenga mbali za anthu otchulidwa m’nkhaniyo.

  3.   Mungatsatire njira imodzi kapena zingapo pa njira zotsatirazi:

    •   Jambulani zithunzi zofotokozera zomwe zikuchitika m’nkhaniyo komanso zosonyeza zinthu zomwe zinachitika pa nthawi ina yake. Mukhozanso kulemba mawu osonyeza zomwe zikuchitika pa chigawo chilichonse cha nkhaniyo.

    •   Jambulani chithunzi cha munthu wotchulidwa m’Baibulo ndipo lembaninso makhalidwe abwino omwe anali nawo komanso zomwe anachita. Muthanso kulemba madalitso amene analandira.

    •   Konzani nkhani yofotokoza zomwe zinachitikazo. Pofotokoza nkhaniyo, mukhozanso kukhala ndi mbali yofunsa mafunso anthu otchulidwa m’nkhaniyo komanso ena omwe anaona zinthuzo zikuchitika.

    •   Ngati mmodzi wa anthu a mu nkhaniyo anasankha zinthu molakwika, yesani kuganizira zinthu zina zomwe akanachita kuti zimuyendere bwino. Mwachitsanzo, ganizirani mmene zinakhalira kuti Petulo akane Yesu. (Maliko 14:66-72) Ndiye kodi akanatani kuti achite zinthu mwanzeru?

    •   Ngati muli ndi luso lopeka nkhani, lembani sewero lanu potengera nkhani yomwe mwawerenga m’Baibulo. Mungawonjezeremonso zimene tikuphunzirapo mu nkhaniyo.​—Aroma 15:4.

      Mukamawerenga Baibulo muziyerekezera kuti mukuona zomwe zikuchitika m’nkhaniyo

 Fufuzani mokwanira

 Mukamafufuza mokwanira zimene mukuwerenga, mukhoza kupeza mfundo zina zobisika. Mwachitsanzo, nthawi zina mungapeze mawu amodzi kapena awiri m’Baibulo koma omwe angakuthandizeni kumvetsa mfundo zambiri za nkhaniyo.

 Yerekezerani zomwe zili pa Mateyu 28:7 ndi zomwe zili pa Maliko 16:7.

  •    N’chifukwa chiyani Maliko pofotokoza kuti Yesu akaonekera kwa ophunzira ake, anawonjezera mawu oti akaonekeranso kwa “Petulo”?

  •  Zokuthandizani: Maliko sanaone nawo zochitikazi chifukwa pa nthawiyi iyeyo panalibe, koma zikuoneka kuti anazimva kuchokera kwa Petulo.

  •  Mfundo yobisika: N’chifukwa chiyani tinganene kuti Petulo analimbikitsidwa atamva zoti Yesu akufuna kuonana naye limodzi ndi ophunzira enawo? (Maliko 14:66-72) Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti analidi mnzake wapamtima wa Petulo? Nanga inuyo mungasonyeze bwanji kuti ndinu bwenzi lenileni potsanzira zimene Yesu anachita?

 Mukamayerekezera kuti mukuona zomwe zikuchitika m’nkhani yomwe mukuwerengayo komanso mukamafufuza mokwanira, mukhoza kuona kuti kuwerenga Baibulo n’kosangalatsa kwambiri.