Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndimafuna Kuti Ndisamalakwitse Chilichonse?

Kodi Ndimafuna Kuti Ndisamalakwitse Chilichonse?

Ngati

  • mumayembekezera kuti kusukulu muzingokhala nambala 1

  • mumaopa kukumana ndi mavuto poopa kuti mulephera kuwathetsa

  • mumaona kuti nthawi zonse anthu akakupatsani malangizo ndiye kuti akulimbana nanu

 . . , ndiye kuti yankho la funso lili pamwambalo ndi Inde. Koma kodi m’pofunikadi kusamala?

  • Kodi pamakhala mavuto otani ngati munthu safuna kulakwitsa chilichonse?

  • Kodi n’chiyani chingakuthandizeni?

  • Zimene achinyamata anzanu amanena

Kodi pamakhala mavuto otani ngati munthu safuna kulakwitsa chilichonse?

Sikulakwa kuyesetsa kuchita zinthu bwino. Buku lina linanena kuti, “pali kusiyana pakati pa kuyesetsa kuchita zinthu zabwino ndi kuvutika ndi mtima wofuna kuchita zinthu zomwe n’zosatheka. Kufuna kuchita chilichonse popanda kulakwitsa ndi kudzivutitsa chabe chifukwa pajatu tonse timalakwitsa zinthu zina.”​—Perfectionism​—What’s Bad About Being Too Good?

Pa nkhaniyi Baibulo limanenanso kuti: “Palibe munthu wolungama padziko lapansi amene amachita zabwino zokhazokha osachimwa.” (Mlaliki 7:20) Chifukwa chakuti nanunso ndinu ochimwa, nthawi zina mungalephere kuchita zinthu mmene munkafunira.

Kodi mumavutika kuvomereza mfundo imeneyi? Ngati mwayankha kuti inde, taganizirani mavuto anayi amene amakhalapo munthu akakhala ndi mtima wosafuna kulakwitsa chilichonse. Ndipo onani mmene inunso angakukhudzireni.

  1. Mmene Mumadzionera. Anthu osafuna kulakwitsa chilichonse amafuna kuti azichita bwino china chilichonse koma pamapeto pake amakhumudwa. Mtsikana wina dzina lake Alicia anati: “Kunena zoona sitingathe kumachita bwino pachilichonse, ndipo tikamangodziona ngati olephera nthawi zonse, mapeto ake timangokulitsa mtima wodzikayikira. Zimenezi zimangokusowetsa mtendere.”

  2. Mmene Mumaonera Malangizo Omwe Angakuthandizeni. Anthu amene safuna kumalakwitsa zinthu amakonda kuganiza kuti munthu akawalangiza ndiye kuti akufuna kuwaipitsira mbiri. Mnyamata wina dzina lake Jeremy anati: “Sindimasangalala munthu akandilangiza. Kukhala ndi maganizo osafuna kulakwitsa zinthu kumachititsa kuti munthu azivutika kuvomereza kuti pali zinthu zina zimene zimamuvuta komanso savomereza malangizo oti amuthandiza.”

  3. Mmene Mumaonera Anthu Ena. Anthu osafuna kulakwitsa chilichonse nthawi zambiri amakonda kupezera zifukwa pa zimene ena achita chifukwa amafuna kuti anthuwo asamalakwitse chilichonse. Mtsikana wina wazaka 18 dzina lake Anna ananena kuti: “Ngati uli ndi mtima wosafuna kulakwitsa chilichonse, umafunanso kuti anthu ena azichita zomwezo. Ndiye ukaona kuti anzako sakuchita zomwe ukuyembekezera umakhumudwa nawo.”

  4. Mmene Ena Amakuonerani. Ngati mumafuna kuti anzanu asamalakwitse chilichonse, musamadabwe mukaona kuti anthu akukuthawani. Mtsikana wina dzina lake Beth anati: “Kuyesetsa kusangalatsa munthu wotereyu n’kotopetsa kwambiri. Palibe amene angakonde kumacheza naye.”

Kodi n’chiyani chingakuthandizeni?

Baibulo limati: “Anthu onse adziwe kuti ndinu ololera.” (Afilipi 4:5) Anthu ololera samayembekezera kuti azichita zinthu zonse bwinobwino popanda kulakwitsa chilichonse, ndipo sayembekezeranso kuti ena azichita zinthu mosalakwitsa chilichonse.

M’dzikoli muli kale mavuto ambirimbiri. Ndiye munthu uzidzivutitsiranji n’kumaganiza kuti sungalakwitse chilichonse? Zimenezitu n’zosatheka!”​—Nyla

Baibulo limati: “Uziyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.” (Mika 6:8) Anthu odzichepetsa amazindikira kuti pali zinthu zina zimene sangakwanitse kuchita. Choncho, sachita zinthu zimene sangakwanitse kapenanso kuthera nthawi pochita zinthu zimene mapeto ake ziwakanika.

Ndimangogwira ntchito imene ndikudziwa kuti ndiikwanitsa. Ndipo pamapeto pake ndimasangalala ndi zimene ndachitazo. Sindifuna kuchita zomwe sindingathe.”​—Hailey.

Baibulo limati: “Chilichonse chimene dzanja lako lapeza kuti lichite, uchichite ndi mphamvu zako zonse.” (Mlaliki 9:10) Apatu tawona kuti munthu angathetse vuto lofuna kumangochita chilichonse mosalakwitsa akamagwira ntchito mwakhama osati mwaulesi. Koma amafunikanso kukhala ndi makhalidwe amene afotokozedwa m’nkhaniyi, omwe ndi kukhala wololera ndiponso wodzichepetsa.

“Ndimayesetsa kugwira ntchito ndi mtima wonse. Ndimazindikira kuti sindingathe kuchita zinthu mosalakwitsa chilichonse, komabe ndimasangalala ndikayesetsa kuchita zomwe ndingathe.”​—Joshua.