Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA

Ndingatani Ngati Mnzanga Atandikhumudwitsa?

Ndingatani Ngati Mnzanga Atandikhumudwitsa?

 Zimene muyenera kudziwa

  •   Tonse tikhoza kukhumudwitsa anzathu. Mnzanu wapamtima kapenanso aliyense amene mumamuona ngati mnzanu, akhoza kulankhula kapena kuchita zinthu zina zomwe zingakukhumudwitseni chifukwa ndi munthu wopanda ungwiro. Ndiye popeza inunso ndinu wopanda ungwiro, kodi munganene kuti simunayambe mwakhumudwitsapo anzanu?​—Yakobo 3:2.

  •   Zomwe zimaikidwa pa intaneti zingachititsenso kuti mukhumudwe. Mwachitsanzo mnyamata wina dzina lake David ananena kuti: “Ukatsegula intaneti n’kuona chithunzi chosonyeza kuti mnzako anali ku pate kwinakwake, umayamba kudabwa kuti n’chifukwa chiyani sanandiitane. Zikatero umakhumudwa ndipo umangoona ngati akutaya.”

  •   Mukhoza kuthana ndi vutoli.

 Zimene mungachite

 Mudzifufuze. Baibulo limati: “Usamafulumire kukwiya mumtima mwako, pakuti anthu opusa ndi amene sachedwa kupsa mtima.”​—Mlaliki 7:9.

 Alyssa ananena kuti: “Nthawi zina pakapita masiku m’pamene umaona kuti unangokhumudwa ndi zazing’ono.”

 Zoti muganizire: Kodi mumangokhumudwa zilizonse? Kodi pali zimene mungachite kuti musamakhumudwe kwambiri ndi zomwe anzanu amachita?​—Mlaliki 7:21, 22.

 Muziganizira kufunika kokhululukira ena. Baibulo limati: ‘Kunyalanyaza cholakwa kumachititsa [munthu] kukhala wokongola.’​—Miyambo 19:11.

 Mallory ananena kuti: “Ngakhale utakhumudwa pa zifukwa zomveka, ndi bwino kukhululuka ndi mtima wonse. Ukatero siufunikanso kumangokumbutsa mnzakoyo zomwe analakwitsa kuti azingokhalira kukupepesa. Ukamukhululukira, nkhaniyo izitheranso pomwepo.”

 Zoti muganizire: Kodi ndi nkhani yaikuludi? Kodi mungathe kungomukhululukira kuti mukhalenso pamtendere?​—Akolose 3:13.

Kumangokhalira kulankhula zomwe mnzanu anakulakwirani, kuli ngati kulowetsa mphepo yozizira m’nyumba moti mukutenthera.

 Muziganizira zofuna za mnzanuyo. Baibulo limati: “Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.”​—Afilipi 2:4.

 Nicole ananena kuti: “Mukamakondana komanso kulemekezana, mumayesetsa kuti mugwirizanenso mwamsanga mukasemphana zochita. Mumakhala kuti munachitira limodzi zinthu zambiri choncho simungafune kuti musiyane.”

 Zoti muganizire: Kodi mungathe kumvetsa chifukwa chimene chachititsa mnzanuyo kulankhula kapena kuchita zinthu zimenezo?​—Afilipi 2:3.

 Mfundo yofunika kwambiri: Muyenera kudziwiratu zimene mungachite anzanu akakukhumudwitsani ndipo zimenezi zidzakuthandizani mukadzakula. Yesetsani kuphunzira kuchita zimenezi panopa.