Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Munthu Ameneyu Ndi Woyenera Kuti Ndimange Naye Banja?

Kodi Munthu Ameneyu Ndi Woyenera Kuti Ndimange Naye Banja?

 Kodi mwapeza mnzanu amene mukuganiza kuti mungamange naye banja? Ngati zili choncho, kodi mungadziwe bwanji ngati munthuyo ali woyenereradi?

 Ndi bwino kuti musatengeke ndi zinthu ngati maonekedwe kapena kutchuka kwa munthuyo. Mwachitsanzo, mtsikana amene mukumuona kuti ndi chiphadzuwa akhoza kukhala wosakhulupirika, kapena mnyamata wotchuka kwambiri angathe kukhala wakhalidwe loipa. Koma inuyo mungafune munthu yemwe mungadzakhale naye momasuka, munthu wogwirizana ndi khalidwe lanu komanso zolinga zanu.​—Genesis 2:18; Mateyu 19:​4-6.

Onani Zinthu Zofunika Kwambiri

 Kuti mudziwe ngati mnzanuyo ndi wokuyenererani, ganizirani za moyo wake mofatsa. M’pofunika kusamala chifukwa mungathe kukopeka naye n’kumanyalanyaza kuona zinthu zofunika kwambiri. Musapupulume, yesetsani kuona khalidwe lake lenileni.

 Anthu ambiri akakhala pa chibwenzi, safufuza mokwanira za mnzawoyo. M’malomwake amangotengeka ndi zinthu zimene onse awiri amakonda. Mwina anganene kuti: “Timakonda nyimbo zofanana.” “Timakonda kuchita zinthu zofanana.” “Timagwirizana pa chilichonse.” Komatu mungafunike kuona bwinobwino zinthu zofunika kwambiri. Mungafunike kuona “munthu wobisika wamumtima.” (1 Petulo 3:4; Aefeso 3:16) M’malo mongoona kuti mumagwirizana pa zinthu zambiri, mungachite bwino kuti muziona zimene zimachitika mukasemphana maganizo.

 Mwachitsanzo, taganizirani mfundo zotsatirazi:

  •   Kodi munthu ameneyu amatani tikasemphana maganizo? Kodi amangoumirira maganizo ake, mwina mpaka kufika ‘popsa mtima’ kapenanso kulankhula “mawu achipongwe”? (Agalatiya 5:​19, 20; Akolose 3:8) Kapena amasonyeza kuti ndi woganiza bwino moti amalolera maganizo a ena ngati sakutsutsana ndi mfundo za m’Baibulo?​​—Yakobo 3:17.

  •   Kodi mnzanuyo ndi wofuna zake zokha, wokonda kulamula kapenanso wansanje? Kodi amafuna kuti muzimuuza chilichonse chimene mukuchita kapena kulikonse kumene mukupita? Mtsikana wina dzina lake Nicole anati: “Ndamvapo anthu apachibwenzi akukangana chifukwa wina sanauze mnzake kumene akupita. Ndikuganiza kuti zikamatere, ndiye kuti pali vuto lalikulu.”​​—1 Akorinto 13:4.

  •   Kodi anthu ena amamuona bwanji? Mungachite bwino kufunsa anthu odalirika, amene akhala akumudziwa bwino munthuyo kwa nthawi yaitali, monga amumpingo mwake. Anthuwo adzakuthandizani kudziwa ngati mnzanuyo ali ndi mbiri yabwino.​​—Machitidwe 16:​1, 2.