Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA

Kodi Ndingatani Kuti Ndizigona Mokwanira?

Kodi Ndingatani Kuti Ndizigona Mokwanira?

Ngati masamu amakuvutani, mwina mungaganize zoti muzichita khama kuwaphunzira. Ngati simuchita bwino masewera enaake mukhozanso kuganiza zoti muziyeserera mobwerezabwereza. Komatu vuto lingakhale kuti simugona mokwanira. N’chifukwa chiyani tikutero?

 • N’chifukwa chiyani mumafunika kugona mokwanira?

 • N’chifukwa chiyani simugona mokwanira?

 • Kodi mungatani kuti muzigona mokwanira?

 • Zimene anzanu anena

N’chifukwa chiyani mumafunika kugona mokwanira?

Akatswiri amanena kuti achinyamata ambiri amafunika kugona maola 8 kapena 10 pa tsiku. N’chifukwa chiyani mumafunika kugona mokwanira?

 • Mumaganiza bwino. Anthu amanena kuti kugona kuli ngati “chakudya cha ubongo.” Kungathandize kuti zizikuyenderani bwino kusukulu, pochita masewera komanso pothana ndi mavuto.

 • Mumakhala wosangalala. Anthu ambiri amene sagona mokwanira maganizo awo sakhazikika, amakhala okhumudwa, amada nkhawa komanso amavutika kuti azigwirizana ndi anzawo.

 • Mumapewa ngozi. Pa kafukufuku amene anachitika ku United States, anthu anapeza kuti madalaivala azaka za pakati pa 16 ndi 24 “amachita ngozi kwambiri chifukwa choti amasinza” kusiyana ndi azaka za pakati pa 40 ndi 59.

 • Mumapewa matenda. Mukamagona thupi lanu limakonza maselo komanso mitsempha ya magazi. Kugona mokwanira kumathandizanso kuti mupewe kunenepa kwambiri, matenda a shuga komanso sitiroko.

Munthu akamagona mokwanira amakhala ngati foni imene yatchajidwa ndipo amatha kuchita zinthu bwinobwino

N’chifukwa chiyani simugona mokwanira?

Achinyamata ambiri sagona mokwanira ngakhale kuti kuchita zimenezi n’kothandiza kwambiri. Mwachitsanzo, mtsikana wina wazaka 16 dzina lake Elaine anati:

“Aphunzitsi athu atafunsa nthawi imene timagona, ambiri ananena kuti amagona cha m’ma 2 koloko m’mawa. Ena anati amagona 5 koloko m’mawa. Koma mmodzi yekha ananena kuti amagona 9:30 usiku.”

Kodi n’chifukwa chiyani anthu ambiri sagona mokwanira?

Kucheza. “Zimakhala zosavuta kuti ndigone mochedwa, makamaka ngati ndapita kukacheza ndi anzanga.”—Pamela.

Kutanganidwa. “Ndimafunitsitsa nditamagona mokwanira koma vuto ndi loti ndimatanganidwa kwambiri.”—Ana.

Zipangizo zamakono. “Foni ndi imene imandilepheretsa kugona mokwanira. Zimandivuta kuti ndiisiye pa nthawi imene ndikugona.”—Anisa.

Kodi mungatani kuti muzigona mokwanira?

 • Muziona nkhaniyi moyenera. Baibulo limati: “Kupuma pang’ono kuli bwino kuposa kugwira ntchito mwakhama ndi kuthamangitsa mphepo.” (Mlaliki 4:6) Kugona ndi kofunika kwambiri. Mukamapanda kugona mokwanira, mungamavutike kugwira ntchito bwino komanso chilichonse chikhoza kumangokubowani.

 • Dziwani zimene zikukulepheretsani kugona. Mwachitsanzo, kodi mumacheza ndi anzanu mpaka usiku? Kodi mumatanganidwa kwambiri ndi homuweki kapena ntchito zapakhomo? Kodi foni yanu imakupangitsani kuti muzigona mochedwa kapena kudzuka usiku?

Zoti muganizire: Pangafunike khama kuti muthane ndi vuto limene limakupangitsani kuti musamagone mokwanira koma zotsatira zake zimakhala zabwino. Lemba la Miyambo 21:5 limati: “Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulira.”

N’zoona kuti zimene zingakhale zothandiza kwa munthu wina sizingakhalenso zothandiza kwa wina. Mwachitsanzo, ena amanena kuti amagona bwino usiku ngati anagonako pang’ono masana. Pomwe ena amati akagona masana amavutika kugona usiku. Choncho muyenera kudziwa zomwe zingakuthandizeni inuyo. Taonani mfundo zotsatirazi:

 • Muzipuma bwinobwino musanakagone. Mukakhala ndi nthawi yopuma musanakagone, zingathandize kuti musavutike kupeza tulo.

  “Muzimaliza mwamsanga ntchito zapakhomo komanso zinthu zina n’cholinga choti musamakaziganizire mukapita kokagona.”Maria.

 • Muziwerengera bwino nthawi. M’malo molola kuti zochitika pa moyo wanu zizikulamulirani, muzikhala ndi ndandanda yochitira zinthu n’cholinga choti muzigona mokwanira.

  “Tsiku lililonse ndimafunika kugona maola osachepera 8. Choncho ndikadziwa kuti ndikufunika kulawirira, ndimayesetsa kukagona mwamsanga.”—Vincent.

 • Musamasinthesinthe. Thupi lanu likhoza kuzolowera nthawi yogona ndi yodzuka ngati mutaliphunzitsa. Akatswiri ena amanena kuti zimakhala bwino kumagona komanso kumadzuka nthawi yofanana tsiku lililonse. Yeserani kuchita zimenezi kwa mwezi umodzi ndipo muone mmene zingakuthandizireni.

  “Mukamagona nthawi yofanana tsiku lililonse, zimathandiza kuti muziganiza bwino. Zimenezi zingathandizenso kuti muzichita bwino zinthu.”—Jared.

 • Muzikhala ndi malire. Baibulo limanena kuti tizipewa kuchita zinthu “mopitirira malire” ndipo izi n’zofunika ngakhale pa nkhani ya zosangalatsa.—1 Timoteyo 3:2, 11.

  “Masiku ano ndimakhala ndi malire a nthawi yocheza komanso kuchita zosangalatsa madzulo. Kupanda kutero ndimavutika ndipo nthawi zambiri vuto limakhala kusagona mokwanira.”—Rebecca.

 • Muzisiya foni. Muzipewa kulowa pa intaneti kapena kulemberana mameseji ndi anzanu kutatsala ola limodzi kuti mukagone. Akatswiri ena amanena kuti kuwala kwa pa foni, tabuleti kapena TV kungachititse kuti munthu azivutika kugona.

  “Anthu amafuna kuti muzicheza nawo nthawi iliyonse ngakhale usiku. Koma kuti mugone mokwanira mumafunika kuisiya foniyo.”—Julissa.