ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA
Kodi Ndingatani Kuti Ndizigwirizana ndi Makolo Anga?
Yankhani mafunso otsatirawa
Kodi mumakonda kukangana ndi ndani?
Bambo
Mayi
Kodi mumakangana nawo kangati?
Patalipatali
Mwa apo ndi apo
Kawirikawiri
Kodi mkanganowo umatha bwanji?
Timauthetsa mwamsanga komanso mwamtendere.
Timauthetsa pambuyo pokangana kwambiri.
Sutha ngakhale titakangana kwambiri.
Zikamakuvutani kugwirizana ndi makolo anu, mukhoza kuganiza kuti iwowo ndi amene ayenera kuyamba kuchita zinthu zoti muzigwirizana. Koma m’nkhaniyi, tiona zinthu zina zimene inuyo mungachite kuti musamakangane nawo. Choyamba, ganizirani izi:
Chifukwa chake mumakangana
Kaganizidwe kanu. Mukamakula mumayamba kuganiza kwambiri kusiyana ndi nthawi imene munali mwana. Mumayamba kukhala ndi maganizo anuanu amene akhoza kusiyana ndi a makolo anu. Komabe Baibulo limati: “Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako.”—Ekisodo 20:12.
Dziwani izi: Pamafunika nzeru ndiponso luso kuti munthu asakangane ndi mnzake amene wasiyana naye maganizo.
Kuchita Zinthu Panokha. Makolo amayamba kukupatsani ufulu wambiri mukamakula. Koma vuto ndi lakuti mwina sangakupatseni msanga ufulu wina uliwonse umene mukufuna. Ndiyeno izi zingachititse kuti muzikangana. Komabe Baibulo limati: “Muzimvera makolo anu.”—Aefeso 6:1.
Dziwani izi: Nthawi zambiri makolo amakupatsani ufulu wina ngati aona kuti mukugwiritsa ntchito bwino ufulu umene muli nawo kale.
Zimene mungachite
Muziganizira zimene inuyo mungachite. M’malo momangoimba mlandu makolo anu, muziganizira zimene inuyo mungachite kuti musamakangane nawo. Mnyamata wina dzina lake Jeffrey ananena kuti: “Sikuti nthawi zonse zimene makolo amanena ndi zomwe zimayambitsa mkangano, koma mmene timawayankhira. Choncho, kuwayankha modekha kungathandize kuti tisamakangane nawo.”
Baibulo limati: “Ngati ndi kotheka, khalani mwamtendere.”—Aroma 12:18.
Muziwamvetsera. Mtsikana wina wazaka 17 dzina lake Samantha anati: “Ndimaona kuti kumvetsera makolo si nkhani yapafupi. Koma makolo akaona kuti ukumvetsera zimene akunena, nawonso amakumvetsera.”
Baibulo limati: “Aliyense akhale wofulumira kumva, wodekha polankhula.”—Yakobo 1:19.
Mikangano imakhala ngati moto chifukwa ngati sitiithetsa msanga imangokulirakulira
Muziwaona kuti ndi anzanu. Mukasemphana maganizo ndi makolo anu, muzikumbukira kuti zili ngati nonse mukusewera m’timu imodzi yampira. Tikutero chifukwa choti nonsenu mukufuna zofanana. Mnyamata wina dzina lake Adam anati: “Mukasemphana maganizo ndi makolo anu, makolowo amaona kuti zimene akunena n’zokuthandizani inuyo ndipo nanunso mumaona kuti zimene mukufunazo n’zokuthandizani. Choncho tinganene kuti aliyense amakhala ndi cholinga chofanana.”
Baibulo limati: “Titsatire zinthu zobweretsa mtendere.”—Aroma 14:19.
Muziwamvetsa. Mtsikana wina dzina lake Sarah anati: “Ndimayesetsa kukumbukira kuti makolo nawonso akulimbana ndi mavuto.” Mtsikana winanso dzina lake Carla anati: “Ndimadzifunsa kuti, ‘Ineyo ndikanakhala kuti ndikulera mwana ndipo ndikukumana ndi zimene makolo anga akukumana nazo, kodi ndikanatani? Kodi ndikanachita zotani pofuna kuthandiza mwana wangayo?’”
Baibulo limati: “Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.”—Afilipi 2:4.
Muzimvera. Baibulo limanena kuti muyenera kumvera makolo anu. (Akolose 3:20) Zinthu zikhoza kukuyenderani bwino mukamachita zimenezi. Mtsikana wina dzina lake Karen anati: “Ndikachita zimene makolo anga amandipempha kuchita, ndimasangalala. Iwo anandichitira zinthu zambiri zabwino, choncho ndikawamvera ndimasonyeza kuti ndikuwathokoza.” Kuti tisamakangane, mankhwala ake ndi kumvera basi.
Baibulo limati: “Popanda nkhuni moto umazima.”—Miyambo 26:20.
Zimene zingakuthandizeni. Ngati mukuona kuti simungathe kulankhula ndi makolo anu za vuto linalake, muzilemba kakalata kapena meseji pafoni. Mtsikana wina dzina lake Alyssa anati: “Ndimachita zimenezi ndikaona kuti zindivuta kulankhula. Kulemba mmene ndikumvera kumandithandiza kuti ndisalankhule zinthu zimene ndikhoza kunong’oneza nazo bondo.”