Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndingatani Anthu Ena Akamandivutitsa?

Kodi Ndingatani Anthu Ena Akamandivutitsa?

Kuvutitsidwa ndi ena si nkhani yaing’ono. Pakafukufuku wina amene anachitika ku Britain anapeza kuti achinyamata 40 pa 100 alionse amene anadzipha ankavutitsidwa ndi anzawo.

 Kodi anthu amavutitsa anzawo m’njira ziti?

Kuwonjezera pa kumenyedwa, anthu amavutitsidwanso m’njira zosiyanasiyana monga zotsatirazi.

 • Mawu achipongwe. Mtsikana wina yemwe ali ndi zaka 20, dzina lake Celine, ananena kuti: “Sindidzaiwala mayina amene anzanga ankandipatsa komanso mawu amwano omwe ankandinena. Zomwe ankandinenazo zinkandipangitsa kudziona kuti ndine munthu wachabechabe, wosafunika komanso wopanda nzeru. Ndimaona kuti zikanakhala bwino akanamandimenya kusiyana n’kundinena mawu achipongwewo.”

 • Kukusala. Mtsikana wina wazaka 18 dzina lake Haley anati: “Anzanga akusukulu anayamba kundisala. Masana pa nthawi ya chakudya, ankayesetsa kuti ndisapeze malo patebulo limene iwowo akhala. Kwa chaka chathunthu, ndinkangokhalira kulira komanso kumadya pandekha.”

 • Kukuipitsira mbiri pogwiritsa ntchito foni kapena kompyuta. Mnyamata wina wazaka 14 dzina lake Daniel anati: “Kungodina mabatani angapo pakompyuta, ungawonongeretu mbiri ya munthu wina, ngakhale moyo wake kumene. Ena angaganize kuti ndikungokokomeza, koma zimachitika.” Anthu ena amavutitsanso anzawo pafoni kapena pakompyuta potumiza zithunzi kapena mauthenga oipa kambiri.

 N’chifukwa chiyani anthu ena amavutitsa anzawo?

Taonani zina mwa zifukwa zimene zimachititsa kuti anthu ena azivutitsa anzawo.

 • Nawonso ankavutitsidwa. Mnyamata wina dzina lake Antonio ananena moona mtima kuti: “Ndinatopa kwambiri ndi kuvutitsidwa ndi anzanga, choncho nanenso ndinayamba kuvutitsa ena n’cholinga choti anthu amene ankandivutitsa aja azindiona kuti ndine mnzawo. Patapita nthawi ndinazindikira kuti zomwe ndinkachitazo n’zolakwika kwambiri.”

 • Amatsanzira anthu olakwika. Munthu wina wolemba mabuku dzina lake Jay McGraw analemba m’buku lake lina kuti: “Nthawi zambiri achinyamata amavutitsa anzawo . . . potsanzira zimene makolo awo kapena abale awo amachita.”​—Life Strategies for Dealing With Bullies.

 • Amafuna azioneka ngati madolo koma amakhala odzikayikira. Katswiri wina wolemba mabuku dzina lake Barbara Coloroso, analemba m’buku lake lina kuti: “Ana ambiri amene amadzikayikira ndiponso amene alibe mtendere wam’maganizo amayamba kuvutitsa anzawo kuti aiwaleko mavuto awo komanso pofuna kuti azioneka ngati madolo.”​—The Bully, the Bullied, and the Bystander.

 Kodi ndi anthu otani amene amakonda kuvutitsidwa?

 • Anthu amene amangokhala okhaokha. Achinyamata ena omwe ndi amanyazi kwambiri ndipo satha kucheza ndi ena amangokhala okhaokha. Zimenezi zimachititsa kuti azipezereredwa ndi anthu ovutitsa anzawo.

 • Achinyamata amene akuoneka mosiyana ndi anzawo. Achinyamata ena amavutitsidwa ndi anzawo chifukwa choti ali ndi maonekedwe osiyana ndi anzawowo. Iwo angavutitsidwe chifukwa chosiyana nawo mtundu, chipembedzo ngakhalenso ngati ali olumala.

 • Achinyamata odzikayikira. Anthu okonda kuvutitsa ena angazindikire anthu odzikayikira. Nthawi zambiri munthu wodzikayikira amapezereredwa chifukwa sangabwezere.

 Kodi muyenera kuchita chiyani mukamavutitsidwa?

 • Musasonyeze kuti zakukhudzani. Mtsikana wina dzina lake Kylie anati: “Anthu amene amakonda kuvutitsa ena amafuna kudziwa ngati zimene akuchitazo zakukhudzani. Mukangokhala osasonyeza kuti zakukhudzani, amaona kuti sanapindule chilichonse ndipo amakusiyani.” Baibulo limati: “Wanzeru amakhala wodekha mpaka pamapeto.”​—Miyambo 29:11.

 • Musabwezere. Kubwezera sikuthandiza chilichonse koma kumangowonjezera mavuto. Baibulo limati: “Musabwezere choipa pa choipa.”​—Aroma 12:17; Miyambo 24:19.

 • Musamapite dala kumalo amene anthu ena angakuvutitseni. Muziyesetsa kupewa malo aliwonse amene mukudziwiratu kuti mungakumaneko ndi anthu omwe angakuvutitseni.​—Miyambo 22:3.

 • Chitani zosiyana ndi zimene munthu amene akukuvutitsaniyo akuyembekezera. Baibulo limati: “Kuyankha modekha kumabweza mkwiyo.”​—Miyambo 15:1.

 • Muzichita tinthabwala. Mwachitsanzo, munthu yemwe akukuvutitsani akakunyozani kuti ndinu wonenepa kwambiri, mukhoza kungovomereza moseka kenako n’kunena kuti: “Ndiyesetsa kuti ndiwondeko pang’ono.”

 • Chokanipo. Mtsikana wina wazaka 19 dzina lake Nora, anati: “Anthu ena akamakuvutitsa koma iwe n’kungochokapo osayankha chilichonse, zimasonyeza kuti ndiwe wanzeru komanso wolimba mtima kuposa anthu amene akukuvutitsawo. Zimasonyezanso kuti ndiwe wodziletsa, khalidwe lomwe anthu ovutitsa anzawo sakhala nalo.”

 • Musamachite zinthu modzikayikira. “Mukamachita zinthu modzikayikira kapena mwamantha, anthu okonda kuvutitsa anzawo angadziwe ndipo angakuonerereni n’kumakuvutitsani.”​—Anatero mtsikana wina dzina lake Rita.

 • Muziuza ena. Kafukufuku wina anapeza kuti anthu oposa hafu ya anthu onse amene amavutitsidwa pa Intaneti sauza ena poopa kuti achita manyazi (makamaka anyamata) komanso poopa kuti munthu yemwe amunenerayo akadziwa, akhoza kuwakhaulitsa kwambiri. Koma kumbukirani kuti anthu ovutitsa anzawo angakuvutitseni kwambiri akadziwa kuti palibe amene mungamuuze. Choncho kuuza ena kungathandize kuti asiye kukuvutitsani.