Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndingatani Ngati Ndikudwala Matenda Aakulu?—Gawo 2

Kodi Ndingatani Ngati Ndikudwala Matenda Aakulu?—Gawo 2

 Matenda aakulu amagwira anthu m’njira zosiyanasiyana.

  •   Matenda ena amaonetsa zizindikiro moti anthu amachita kuona kuti munthuyu akuvutika, pamene ena saonetsa zizindikiro moti wodwalayo amavutika ndi ululu popanda anthu kuzindikira.

  •   Matenda ena amavutitsa wodwala mwa apo ndi apo koma ena amavutitsa wodwala tsiku lililonse.

  •   Matenda ena amakhala ndi mankhwala moti munthu akhoza kuchira koma ena sakhala ndi mankhwala moti wodwalayo akhoza kumwalira.

 Achinyamata amatha kukhudzidwa ndi matenda m’njira zitatu zonsezi. M’nkhani ino muli zitsanzo za achinyamata amene akudwala matenda aakulu ndipo ngati inunso mukudwala matenda aakulu, mulimbikitsidwa ndi zimene anzanuwa ananena.

 GUÉNAELLE

 Zimandivuta kwambiri kuvomereza kuti sindingathe kuchita zinthu zina. Ndimafunitsitsa kuchita zinthu zambiri koma ndimalephera chifukwa cha matenda anga.

 Ndimadwala matenda enaake a muubongo amene amalepheretsa ubongo wanga kutumiza bwinobwino mauthenga ku thupi langa. Nthawi zina zimenezi zimachititsa kuti mbali zina za thupi langa, kuyambira kumutu mpaka kuphazi, zizinjenjemera kapenanso zisiyiretu kugwira ntchito. Panopa ndimavutika kuchita zinthu zing’onozing’ono monga kuyenda, kulankhula, kuwerenga, kulemba ndiponso kumvetsa zimene ena akulankhula. Ndikadwalika kwambiri, akulu a mumpingo wathu amapemphera nane ndipo zimenezi zimandithandiza kuti mtima ukhale m’malo.

 Ndimaona kuti Yehova Mulungu amandithandiza pa mayesero alionse amene ndimakumana nawo. Sindifuna kuti matenda anga azindirepheretsa kumutumikira mmene ndingathere. Moti nthawi zonse ndimayesetsa kuthandiza ena kuti aphunzire za lonjezo la m’Baibulo lakuti posachedwa Yehova Mulungu adzabweretsa paradaiso padziko lapansili ndipo pa nthawiyo sipadzakhalanso kuvutika kulikonse.—Chivumbulutso 21:1-4.

Taganizirani izi: Kodi mungatengere bwanji chitsanzo cha Guénaelle pothandiza anthu ena?—1 Akorinto 10:24.

 ZACHARY

 Ndili ndi zaka 16, anandipeza ndi matenda oopsa kwambiri a khansa ya muubongo. Madokotala anandiuza kuti ndimwalira pakatha miyezi 8. Kungoyambira nthawi imeneyi ndinakhala ndikuvutika kwambiri.

 Chifukwa chakuti khansayi inandigwira muubongo, mbali yakumanja ya thupi langa sigwira ntchito. Popeza sinditha kuyenda, nthawi zonse ndimafunika ndikhale ndi munthu kunyumba woti azindithandiza.

 Kukula kwa matendawa kwapangitsa kuti ndizivutika kulankhula bwinobwino. Ndisanayambe kudwala ndinkasangalala kuchita masewera osiyanasiyana monga kusewera m’madzi komanso kusewera mpira. Popeza ndine wa Mboni za Yehova, ndinkakondanso kulalikira. Ndikukayikira ngati anthu ambiri amamvetsa mmene munthu umamvera ukakhala kuti ukulephera kuchita zinthu zimene poyamba unkazikonda kwambiri.

 Mawu a palemba la Yesaya 57:15 amandilimbikitsa kwambiri chifukwa amanditsimikizira kuti Yehova Mulungu amathandiza anthu ‘opsinjika’ komanso kuti amandimvera chisoni. Komanso lemba la Yesaya 35:6 limanena za lonjezo la Yehova lakuti m’tsogolomu ndidzayambanso kuyenda ndiponso kumutumikira ndili ndi thanzi labwino kwambiri.

 Ngakhale nthawi zina ndimavutika kwambiri ndi matenda angawa, sindikayikira kuti Yehova amandithandiza. Ndikakhala ndi nkhawa kapena ndikamaopa kuti ndimwalira, nthawi zonse ndimauza Mulungu m’pemphero mmene ndikumvera ndipo palibe chimene chingandilekanitse ndi chikondi cha Yehova.—Aroma 8:39.

 Zachary anamwalira ali ndi zaka 18. Pa nthawiyi n’kuti patangopita miyezi iwiri kuchokera pamene anafunsidwa za matenda akewa kuti nkhaniyi ilembedwe. Chikhulupiriro chake chakuti Mulungu adzakwaniritsa lonjezo lake loukitsa anthu m’dziko lapansi la paradaiso chinakhalabe champhamvu mpaka tsiku limene anamwalira.

Taganizirani izi: Mofanana ndi Zachary, kodi pemphero lingakuthandizeni bwanji kuti mukhalebe m’chikondi cha Mulungu?

 ANAÏS

 Patangopita masiku ochepa kuchokera pamene ndinabadwa, anandipeza ndi matenda otuluka magazi muubongo. Zimenezi zinapangitsa kuti mbali zambiri za thupi langa, makamaka miyendo, zisamagwire bwino ntchito.

 Panopa ndimatha kuyenda mtunda waufupi pogwiritsa ntchito ndodo yoyendera koma nthawi zambiri ndimagwiritsa ntchito njinga ya olemala ndikafuna kupita pataliko. Komanso nthawi zina minofu yanga imakungika ndipo zimenezi zimapangitsa kuti ndizivutika kuchita zinthu zosavuta, monga kulemba.

 Kuwonjezera pa kuvutika ndi matendawa, chithandizo chakuchipatala chimene ndimalandira n’chopweteka kwambiri. Nthawi zambiri pa mlungu ndimapita kuchipatala komwe amakandichititsa mafizo othandiza kuti minofu yanga imasuke. Ndipo ndakhala ndikuchita zimenezi kwa nthawi yaitali. Ndinachitidwa maopaleshoni akuluakulu anayi, ndipo yoyamba anandichita ndili ndi zaka 5. Maopaleshoni awiri omalizira anali owawa kwambiri chifukwa ndinakhala ndili kuchipatala kwa miyezi itatu podikira kuti ndichire.

 Anthu a m’banja la kwathu amandithandiza kwambiri makamaka ndikakhala ndi nkhawa chifukwa timacheza n’kumaseka. Mayi anga komanso azichemwali anga amandithandiza kuti ndizioneka bwino chifukwa sindingathe kudzisamalira ndekha. Ndimadandaula kuti sindingathe kuvala nsapato zagogoda. Ndimakumbukira kuti ndinavalapo kamodzi ndili mwana. Ndinazivala m’manja n’kumakwawa, ndipo tonse tinaseka kwambiri.

 Ndimayesetsa kuganizira kwambiri zinthu zimene ndimakwanitsa kuchita m’malo momangoganizira zimene sindingathe. Ndimakonda kuphunzira zinenero. Ndimakondanso kuchita masewera osambira. Popeza ndine wa Mboni za Yehova, ndimakonda kupita kolalikira kuti ndikauze anthu ena zinthu zimene ndimakhulupirira. Ndimaona kuti anthu amamvetsera mwachidwi ndikamawalalikira.

 Ndili mwana makolo anga anandiphunzitsa kuti mavuto angawa adzatha. Kuyambira nthawi imeneyo, ndimakhulupirira kwambiri Yehova komanso lonjezo lake lakuti adzachotsa mavuto onse, kuphatikizapo matenda angawa. Zimenezi zimandithandiza kuti ndizipirira komanso kuti ndizilimba mtima.—Chivumbulutso 21:3, 4.

Taganizirani izi: Mofanana ndi Anaïs, kodi mungatani kuti musamangoganizira za matenda anu?

 JULIANA

 Ndimadwala matenda opweteka kwambiri amene amatha kuononga maselo a mtima, mapapo komanso magazi. Panopa anayamba kuononga maselo a impso zanga.

 Ndili ndi zaka 10, anandipeza ndi matenda enaake amene amandichititsa kuti ndizimva kupweteka komanso kutopa. Matendawa anandichititsanso kuti ndizingokwiya zilizonse. Nthawi zina ndimadziona kuti ndine munthu wosafunika.

 Tsiku lina munthu wina wa Mboni za Yehova anabwera kunyumba kwathu. Pa nthawiyi n’kuti ndili ndi zaka 13. Wa Mboniyo anandiwerengera lemba la Yesaya 41:10. Palembali Yehova Mulungu ananena kuti: “Usachite mantha, pakuti ndili nawe. . . . Ndikugwira mwamphamvu ndi dzanja langa lamanja lachilungamo.” Kungoyambira nthawi imeneyi ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova. Panopa patha zaka 8 kuchokera pamene ndinayamba kuphunzira ndipo ndikutumikira Mulungu ndi mtima wonse komanso ndimayesetsa kuti ndisamangokhalira kuganizira za matenda angawa. Ndimaona kuti Yehova wandipatsa “mphamvu yoposa yachibadwa,” kuti ndizikhala wosangalala.—2 Akorinto 4:7.

Taganizirani izi: Mofanana ndi Juliana, kodi lemba la Yesaya 41:10 lingakuthandizeni bwanji?