Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Kukopana Kuli Ndi Vuto?

Kodi Kukopana Kuli Ndi Vuto?

 Kodi kukopana n’kutani?

Anthu ena amaganiza kuti kukopana ndi njira yosonyezera kuti ukufuna munthu yemwe si mwamuna kapena mkazi mnzako ndipo ungachite zimenezi poyankhula kapena kuchita zinazake. Kodi n’kulakwa kusonyeza kuti ukufuna winawake? Osati kwenikweni. Mtsikana wina dzina lake Ann anati: “Ngati munthu wafika pamsinkhu woti n’kukhala ndi chibwenzi ndipo wapeza munthu amene akukuchititsa chidwi, kodi ungadziwe bwanji ngati nayenso ali nawe chidwi?”

Komabe, mu nkhani ino tikambirana za kukopana kumene kumasonyeza ngati kuti munthu ali ndi cholinga choyamba chibwenzi ndi munthu wina, koma pamene alibe maganizo amenewa.

“Palibe vuto ngati utayamba kusonyeza munthu chidwi mwa njira yapadera ngati uli ndi maganizo ofuna kuyamba naye chibwenzi. Koma n’kulakwa kuchita zinthu zomwe zingapangitse munthu wina kuganiza kuti umamufuna koma kenako n’kusiya kumusonyeza chidwicho, chifukwa zimenezi zingamukhumudwitse kwambiri.”—Deanna.

 N’chifukwa chiyani anthu ena amakopana?

Anthu ena amachita zimenezi n’cholinga chofuna kudziwa kuti angathedi kufunsira kapena kufunsiridwa. Mtsikana wina dzina lake Hailey anati: “Ukazindikira kuti ungathe kupangitsa munthu wina kumachita nawe chidwi, umafuna kuti uzingokopabe anthu ena.”

Koma ngati munthu angamachite zinthu zosonyeza ngati ali ndi maganizo ofuna kuyamba chibwenzi ndi munthu wina pamene alibe, angasonyeze kuti ndi wankhanza ndipo sakuganizira mmene kuchita zimenezi kungakhudzire munthu winayo. Zingapangitsenso kuti anthu azikayikira ngati munthuyo amaganizadi bwino. Baibulo limati: “Munthu wopanda nzeru mumtima mwake amakondwera ndi uchitsiru.”—Miyambo 15:21.

Hailey ananenanso kuti, “Poyamba kukopana kungaoneke ngati kulibe vuto lililonse, koma nthawi zambiri sikukhala ndi zotsatirapo zabwino.”

 Kodi kukopana n’koopsa bwanji?

 • Kukopana kukhoza kuipitsa mbiri yanu.

  “Mtsikana amene amakopa ena amaoneka kuti amadzikayikira komanso ndi wachibwana. Umaona kuti ndi munthu wopanda chilungamo koma akungofuna kupeza zimene iyeyo akufuna kuchokera kwa iwe.”—Jeremy.

  Baibulo limati: “Chikondi . . . sichisamala zofuna zake zokha.”—1 Akorinto 13:4, 5.

  Zoti muganizire: Kodi ndi mawu kapena zochita zotani zimene zingakuchititseni kukhala ndi mbiri yoti mumakopa anthu?

 • Kukopana kumakhumudwitsa munthu amene mukumukopayo

  “Ndikakumana ndi mnyamata yemwe amakonda kukopa atsikana, sindifuna kumuyandikira. Zimakhala ngati akungolankhula nane chifukwa choti ndine mtsikana. Anthu amene amakopana sasamala kwenikweni za ine, koma amangofuna kudzisangalatsa okha basi.”—Jaqueline.

  Baibulo limati: “Aliyense asamangodzifunira zopindulitsa iye yekha basi, koma zopindulitsanso wina.”—1 Akorinto 10:24.

  Zoti muganizire: Kodi munayamba mwaganizapo kuti munthu wina akukufunani, koma kenako munazindikira kuti munkaganiza molakwika? Ngati ndi choncho, kodi munamva bwanji mutazindikira zimenezi? Kodi mungatani kuti mupewe kukhumudwitsa munthu wina mwa njira imeneyi?

 • Kukopana kungakuchititseni kuti mudzavutike kupeza mwamuna kapena mkazi woti mudzayambe naye chibwenzi.

  “Mnyamata yemwe amakonda kukopa atsikana sangakhale woyenera kukwatirana naye kapena kuyamba naye chibwenzi. N’zovuta kwambiri kumudziwa kapena kumukhulupirira munthu amene amangofuna kukopa anzake.”—Olivia.

  Wamasalimo Davide ananena kuti: “Sindinayanjane ndi anthu obisa umunthu wawo.”—Salimo 26:4.

  Zoti muganizire: Kodi anthu ena amamuona bwanji munthu yemwe amakonda kukopa anzake? Kodi inuyo mungakonde kusonyeza chidwi munthu wotereyu?