Pitani ku nkhani yake

Kodi Ndingatani Ngati Sukulu Yanditopetsa?

Kodi Ndingatani Ngati Sukulu Yanditopetsa?

Zimene zingakuthandizeni

Khalani ndi maganizo oyenerera. Muziganizira ubwino wa sukulu. N’zoona kuti si zonse zimene mumaphunzira kusukulu zimene zingaoneke kuti n’zaphindu panopa. Komabe, kuphunzira maphunziro osiyanasiyana kusukulu kungakuthandizeni kuti muzimvetsa bwino zinthu m’dzikoli. Komanso zingakuthandizeni kuti mukhale “zinthu zonse kwa anthu osiyanasiyana,” ndipo mungakwanitse kumalankhula ndi anthu azikhalidwe komanso maphunziro osiyanasiyana. (1 Akorinto 9:22) Mfundo ina yofunika kwambiri ndi yakuti sukulu ingakuthandizeni kukhala ndi luso lotha kuganiza bwino. Ndipotu luso limeneli lingadzakuthandizeni kwambiri m’tsogolo muno.

Nthawi yomwe muli kusukulu ili ngati kudula mitengo m’nkhalango yowirira kuti mupeze njira, ndipo zonsezi zingatheke ngati mukugwiritsa ntchito zipangizo zoyenerera

Muziona aphunzitsi anu moyenerera. Ngati mukuona kuti aphunzitsi anu amakutopetsani, muziganizira kwambiri zimene mukuphunzira, osati aphunzitsiwo. Muzikumbukiranso kuti aphunzitsi anuwo mwina akhala akuphunzitsa zimenezo kwa zaka zambiri komanso kwa ana ambirimbiri. Choncho, zingakhale zovuta kuti aphunzitsiwo akhalebe ndi chidwi kwambiri mofanana ndi mmene ankachitira atangoyamba kumene kugwira ntchito yophunzitsa.

Yesani izi: Muzilemba notsi, muzifunsa mwaulemu kuti mudziwe zambiri komanso muzimvetsera mwachidwi. Ngati inuyo mungayambe kumvetsera mwachidwi, anzanu angayambenso kumvetsera mwachidwi.

Musamadziderere. Sukulu ingakuthandizeni kuti luso lanu linalake, lomwe simudziwa kuti muli nalo, lionekere. Mwachitsanzo, Paulo anauza Timoteyo m’kalata imene anamulembera, kuti: “Mphatso ya Mulungu imene ili mwa iwe, . . . uikolezere ngati moto.” (2 Timoteyo 1:6) Apa zikuoneka kuti Timoteyo anapatsidwa mphatso inayake kudzera mwa mzimu woyera. Koma iye anafunika kuchitapo kanthu kuti “mphatso” yakeyo igwire ntchito. Komabe, luso linalake la kusukulu limene inuyo mungakhale nalo sikuti munachita kupatsidwa mwachindunji ndi Mulungu. Ngakhale zili choncho, luso limene muli nalolo ndi la inuyo basi. Choncho, sukulu ingakuthandizeni kuti muzindikire kuti muli ndi luso linalake ndiponso kuti lusolo likule. Zimenezi zingachitike pokhapokha ngati muli pa sukulu.