Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Ndingatani Ngati Makolo Anga Sakundilola Kugwiritsa Ntchito Malo Ochezera a pa Intaneti?

Ndingatani Ngati Makolo Anga Sakundilola Kugwiritsa Ntchito Malo Ochezera a pa Intaneti?

 N’kutheka kuti anzanu onse amagwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti ndipo nthawi zonse amangokhalira kukambirana za malo amenewa. Mwinanso amakusekani chifukwa chakuti mulibe akaunti. Kodi muyenera kudziwa zotani pa nkhani imeneyi? Nanga mungachitepo chiyani?

Zomwe muyenera kudziwa

 Sikuti ndinu nokha. Makolo ambiri samalola anawo kuti azigwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti. Mwina amachita zimenezi podziwa kuti kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti kumabweretsa mavuto otsatirawa:

  •   kuvutika maganizo komanso matenda ena amaganizo.

  •   kuonera zolaula, kutumizirana mauthenga kapena zithunzi zolaula komanso kuvutitsidwa ndi anthu okonda kuchitira ena zachipongwe pa intaneti.

  •   kusemphana maganizo komanso kuyalutsana pa nkhani zosadziwika bwino.

 Achinyamata ambiri asankha kutseka ma akaunti awo a pa intaneti. Iwo anazindikira kuti kugwiritsa ntchito malowa kuli ndi mavuto ambiri poyerekezera ndi maubwino ake. Taonani zomwe zinachitikira achinyamata ena:

  •   Priscilla anazindikira kuti malowa amamulepheretsa kupeza nthawi yochitira zinthu zofunika kwambiri.

  •   Jeremy sankasangalala ndi zinthu zosayenera zomwe zinkangobwera zokha pafoni yake.

  •   Bethany ananena kuti malowa ankamuchititsa kuti aziganizira kwambiri zimene anthu ena akuchita.

 “Ndinasankha kudilita apu ya malo ochezera ndipo ndikuona kuti ndinachita bwino kwambiri. Sindimalakalakanso kugwiritsa ntchito malowa ndipo ndikusangalala kuti ndimagwiritsa ntchito nthawi yanga pa zinthu zofunika kwambiri.”—Sierra.

 Vuto lomwe ndinaona ndi malo ochezera a pa intaneti ndi loti amakomedwetsa komanso ndinkakhumudwa ndi zimene anthu ena ankalemba pa zimene ndaposita. Sizinali zophweka kuti ndidilite akaunti yanga koma nditangoidilita, pompo ndinamva kuti ndatula chimtolo cholemetsa. Panopa ndili ndi wamumtima.”—Kate.

Zimene mungachite

 Muzimvera malamulo amene makolo anu anakhazikitsa. Muziyesetsa kutsatira malangizo popanda kukwiya kapenanso kudandaula ndipo iwo adzazindikira kuti ndinu munthu wamkulu amene amatha kusankha zinthu mwanzeru

 Mfundo ya m’Baibulo: “Munthu wopusa amatulutsa mkwiyo wake wonse, Koma wanzeru amakhala wodekha ndipo amalamulira mkwiyo wake.”—Miyambo 29:11.

 Anthu ena angakuuzeni kuti mutha kumagwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti koma makolo anu asadziwe kapenanso kuti mukhale ndi akaunti yachinsinsi. Kumeneku kungakhale kulakwitsa kwakukulu. Mukamachita zinthu zobisa muzingokhala ndi nkhawa komanso kudziimba mlandu. Mungakumanenso ndi mavuto aakulu ngati makolo anu angakutulukireni komanso angasiye kukukhulupirirani.

 Mfundo ya m’Baibulo: “Tikufuna kuchita zinthu zonse moona mtima.”—Aheberi 13:18.

 Muzisankha nokha zoyenera kuchita pa nkhani imeneyi. Mofanana ndi achinyamata amene atchulidwa munkhaniyi, mwina nanunso mungaganizire zifukwa zambiri zomwe zingakuchititseni kupewa malo ochezera a pa intaneti. Ngati mukuona kuti malo ochezera a pa intaneti akukusokonezani, muzisankha nokha kusiya kuwagwiritsa ntchito, osati chifukwa choti makolo anu akuuzani koma chifukwa choti ndi zimene inuyo panokha mwasankha kuchita. Mukatere simungachite manyazi kuyankha anzanu akakufunsani chifukwa chimene mwasiyira kuwagwiritsa ntchito ndipo sangakusekeni.

 Mfundo yofunika kwambiri: Muzichita zinthu mogwirizana ndi makolo anu ndipo akakhazikitsa lamulo, muziona ubwino wa lamulolo zomwe zidzakuthandizani kuti musavutike kugwirizana nawo. Panopa n’zotheka kukhala popanda kugwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti.