Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndingatani Kuti Ndizipindula ndi Sukulu Ngakhale Pamene Ndikuphunzirira Kunyumba?

Kodi Ndingatani Kuti Ndizipindula ndi Sukulu Ngakhale Pamene Ndikuphunzirira Kunyumba?

 Ana asukulu ambiri asiya kaye kupita kusukulu ndipo ayamba kuzolowera kuphunzira ali kunyumba. Kodi nanunso mukuphunzirira kunyumba? Ngati ndi choncho, mungatani kuti muzipindula ndi maphunziro? Mfundo zotsatirazi zikuthandizani. a

 Mfundo 5 zomwe zingakuthandizeni

  •   Khalani ndi ndandanda yabwino yochitira zinthu. Yesetsani kuti mukhale ndi ndandanda yokhazikika yofanana ndi yomwe munali nayo pamene munkapita kusukulu. Patulani nthawi yochita zinthu zakusukulu, yogwira ntchito zapakhomo komanso zinthu zina zofunika. Koma mukhoza kusintha ndandanda yanu pakafunika kutero.

     Mfundo ya m’Baibulo: “Zinthu zonse zizichitika . . . mwadongosolo.”—1 Akorinto 14:40.

     “Muzichita zinthu ngati mmene munkachitira mukakhala kuti muli kusukulu. Muziyendera nthawi kuti mumalize kuchita zinazake.”—Anatero Katie.

     Zoti muganizire: N’chifukwa chiyani ndi nzeru kulemba ndandanda yanu n’kuiika pamalo oonekera?

  •   Muzichita zinthu mwakhama. Munthu akamakula amayenera kuzindikira kuti akufunika kugwira ntchito mwakhama ngakhale pamene akuona kuti kuchita zimenezi n’kotopetsa. Musamanyalanyaze kuchita zinthu.

     Mfundo ya m’Baibulo: “Musakhale aulesi pa ntchito yanu.”—Aroma 12:11.

     “Kuchita zinthu mwakhama si kophweka. Munthu akhoza kumangodzikhululukira n’kumanena kuti, ‘Ndilemba homuweki imeneyi nthawi ina.’ Ndiyeno nthawiyo ikakwana osalemba kenako ntchito zimangounjikana.”—Anatero Alexandra.

     Zoti muganizire: Kodi kuchita zinthu zakusukulu pamalo omwewo komanso pa nthawi imodzimodziyo tsiku lililonse kungakuthandizeni bwanji kuti muzichita zinthu mwakhama?

  •   Pezani malo abwino ophunzirira. Muziika pafupi zinthu zonse zomwe mukufunikira. Sankhani malo abwino koma osati a wofuwofu kwambiri mpaka kukupangitsani kuti muzifuna kugona. Ngati simungathe kupeza malo apadera oti muziphunzirira mwina mungapeze malo abwino kukhitchini kapena kuchipinda.

     Mfundo ya m’Baibulo: “Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulira.”—Miyambo 21:5.

     “Siyani kaye kusewera magemu a pakompyuta, mpira, gitala komanso tcherani foni yanu kuti isakusokonezeni. Musamakhale ndi zinthu zomwe zingakusokonezeni pophunzira.”—Anatero Elizabeth.

     Zoti muganizire: Kodi mungasinthe zinthu ziti pamalo omwe mumaphunzirira kuti musamasokonezeke?

  •   Muzichita chinthu chimodzi pa nthawi imodzi. Muziganizira zinthu zomwe mukuphunzira pa nthawiyo ndipo musamachite zinthu zambirimbiri pa nthawi imodzi. Mukamachita zinthu zingapo nthawi imodzi, mukhoza kulakwitsa zinthu ndipo zingakutengereni nthawi yaitali kuti mumalize zimene mukupanga.

     Mfundo ya m’Baibulo: “Muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu.”—Aefeso 5:16.

     “Zinkandivuta kuchita chinthu chimodzi pa nthawi imodzi ndikakhala ndi foni yanga pafupi. Ndinataya nthawi yambiri pochita zinthu zosafunika.”—Anatero Olivia.

     Zoti muganizire: Kodi n’zotheka kuwonjezera pang’onopang’ono nthawi yoti muzichita chinthu chimodzi pa nthawi imodzi?

  •   Muzipeza nthawi yopuma. Muzikawongola miyendo, kukwera njinga kapena kuchita masewera olimbitsa thupi. Komanso muzichita zinthu zomwe mumakonda. Buku lakuti, School Power linati: “Koma muziyamba kaye kugwira ntchito. Mukakhala kuti mwamalizitsa ntchito zanu zonse m’pamene mumaona kuti muli ndi ufulu wochita zimene mukufuna.”

     Mfundo ya m’Baibulo: “Kupuma pang’ono kuli bwino kuposa kugwira ntchito mwakhama ndi kuthamangitsa mphepo.”—Mlaliki 4:6.

     “Ukakhala kusukulu umatha kuphunzira kuimba pogwiritsa ntchito zida zoimbira kapena ukhoza kumaphunzira m’kalasi. Ndikulakalaka kuchitanso zimenezi ngakhale kuti panopa sitikupitanso kusukulu. Ndi bwino kumachitanso zinthu zinazake zimene umakonda m’malo momangopanga zasukulu zokhazokha.”—Anatero Taylor.

     Zoti muganizire: Kodi ndi zinthu ziti zomwe mungachite pa nthawi yopuma zimene zingakuthandizeni kuti mupezenso mphamvu zopitiriza ntchito zanu zakusukulu?

a Pali njira zosiyanasiyana zomwe mungagwiritse ntchito pophunzira muli kunyumba. Munkhaniyi muli mfundo zosiyanasiyana zothandiza ndipo musankhe zomwe zikugwirizana ndi mmene zinthu zilili ndi inuyo.