Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndizitani Ndikalakwitsa Zinazake?

Kodi Ndizitani Ndikalakwitsa Zinazake?

 Kodi inuyo mungatani?

Werengani zimene zinachitikira mtsikana wina dzina lake Karina ndipo muyerekezere kuti zikuchitikira inuyo. Kodi mukanakhala kuti zikuchitikira inuyo mukanatani?

Karina: “Tsiku lina ndinkayendetsa galimoto mothamanga kwambiri ndikupita kusukulu moti apolisi anandigwira n’kundilipiritsa ndipo anandipatsa tikiti. Ndinakhumudwa nazo kwambiri. Ndipo nditawafotokozera mayi anga anandiuza kuti ndiuze bambo koma sindinafune kuti ndiwauze.”

 

 1. A: Osanena chilichonse poganiza kuti bambo anu sadziwa.

 2. B: Kuwauza bambo anu zimene zinachitikadi.

Mwina mungakonde kusankha yankho la pa A. Mwinanso mungaganize kuti amayi anu aganiza zoti munawafotokezera bambo anu. Koma pali zifukwa zomveka zosonyeza kuti kuvomereza zimene munthu walakwitsa n’kothandiza.

 Zifukwa zitatu zimene zingakuthandizeni kuvomereza zolakwa zanu

 1. 1. N’chinthu choyenera kuvomereza zimene timalakwitsa. Pofotokoza zokhudza makhalidwe amene Akhristu ayenera kukhala nawo, Baibulo limati: “Tikufuna kuchita zinthu zonse moona mtima.”​—Aheberi 13:18.

  “Ndakhala ndikuyesetsa kuchita zinthu moona mtima ndipo ndimavomereza komanso kukonza zimene ndalakwitsa mwamsanga.”​—Alexis.

 2. 2. Nthawi zambiri anthu amakhululukira anthu amene amavomereza zolakwa zawo. Baibulo limati: “Wobisa machimo ake zinthu sizidzamuyendera bwino, koma woulula n’kuwasiya adzachitiridwa chifundo.”—Miyambo 28:13.

  “N’zoona kuti pamafunika kulimba mtima kuti munthu uvomereze zimene walakwitsa. Koma ukavomereza, anthu amakukhulupirira chifukwa amaona kuti ndiwe woona mtima. Zinthu zingakuyendere bwino ukavomereza mosavuta kuti walakwa.”—Richard.

 3. 3. Chifukwa chachikulu n’chakuti, zimasangalatsa Yehova. Baibulo limati: “Munthu wochita zachiphamaso Yehova amanyansidwa naye, koma amakonda anthu owongoka mtima.”—Miyambo 3:32.

  “Nthawi ina nditalakwitsa zinthu kwambiri, ndinazindikira kuti ndinafunika kuulula. Ndinadziwa kuti Yehova sangandidalitse ngati sindingachite zimene iye amafuna.”​—Rachel.

Kodi Karina anachita chiyani atalakwitsa? Anayesetsa kubisa tikiti yosonyeza kuti apolisi anamulipiritsa chifukwa chothamangitsa kwambiri galimoto. Koma patapita nthawi zinaululika. Iye anati: “Patadutsa pafupifupi chaka, bambo anga ankayang’ana zokhudza inshuwalansi ya galimoto yathu ndipo anapeza tikiti yosonyeza kuti nthawi ina apolisi anandilipiritsa chifukwa chothamangitsa kwambiri galimoto. Anandikalipira kwambiri ndipo ngakhale mayi anga anakwiya chifukwa chakuti sindinatsatire zimene anandiuza.”

Zimene taphunzirapo: Karina ananena kuti: “Munthu ukabisa zimene walakwitsa umapangitsa kuti zinthu ziipe kwambiri. Pakapita nthawi umakumanabe ndi zotsatira za zimene unalakwitsa.”

 Muziphunzirapo kanthu mukalakwitsa zinthu

Munthu aliyense amalakwitsa. (Aroma 3:23; 1 Yohane 1:8) Ndipo monga mmene taonera, munthu umasonyeza kuti ndiwe wodzichepetsa komanso woganiza bwino ukavomereza kuti walakwitsa nthawi yomweyo.

Chinthu china chofunika ndi kuphunzira pa zimene walakwitsazo. Koma ndi zomvetsa chisoni kuti achinyamata ena saphunzirapo kanthu pa zimene alakwitsa. Iwo akalakwitsa amamva ngati mmene mtsikana wina dzina lake Priscilla anamvera. Iye ananena kuti: “Nthawi zambiri ndinkakhumudwa kwambiri ndikalakwitsa zinthu. Ndinkadzikaikira moti zolakwa zanga ndinkaziona ngati katundu wolemera woti sindingakwanitse kumunyamula. Komanso zinkandikhudza kwambiri ndipo ndinkadziona ngati munthu wosafunika kwenikweni.”

Kodi nanunso mumamva choncho nthawi zina? Ngati ndi choncho kumbukirani izi: Kuganizira kwambiri zimene munalakwitsa m’mbuyomu kuli ngati kumangoyang’anitsitsa pagalasi loonera kumbuyo pamene mukuyendetsa galimoto. Ngati mutamangoganizira zinthu zakale, mukhoza kumadziona ngati munthu wopanda ntchito ndipo mungasowe mphamvu zolimbana ndi mavuto amene mungadzakumane nawo.

Koma chofunika n’chakuti muziona zinthu moyenera mukalakwitsa zina zake.

“Muziganizira zimene mwalakwitsa n’kuona zimene mungaphunzirepo n’cholinga choti musadzabwerezenso. Koma musamangoziganizira kwambiri mpaka kumadziona ngati wopanda ntchito.”​—Elliot.

“Ndimayesetsa kumaphunzirapo kanthu pa chilichonse chimene ndingalakwitse kuti zizindithandiza kukhala munthu wabwino komanso kuti ndidzachite mwanzeru ndikadzakumana ndi zinthu zofanana ndi zimene ndalakwitsazo. Ndimaona kuti zimenezi n’zothandiza kuti munthu azichita zinthu ngati wamkulu.”​—Vera.