Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Mboni za Yehova

Chichewa

Kodi Ndisiye Sukulu?

Kodi Ndisiye Sukulu?

Taganizirani kaye izi

Kodi malamulo a boma la dziko lanu amafuna kuti munthu asasiye sukulu asanafike kalasi iti? Kodi inuyo mwafika kalasi imeneyo? Si bwino kusiya sukulu ngati zimenezi zingachititse kuti muphwanye malangizo a m’Baibulo akuti, “munthu aliyense azimvera olamulira akuluakulu.”—Aroma 13:1.

Kodi mwakwanitsa zolinga zanu? Kodi zolinga zanu zopitira kusukulu n’zotani? Kodi mulibe zolinga zenizeni? Mukufunika kudziwa zimenezi chifukwa ngati simutero, mungakhale ngati munthu amene wakwera sitima koma sakudziwa kumene akufuna kupita. Choncho, kambiranani ndi makolo anu nkhani imene ili ndi mutu wakuti, “ Zolinga Zanga pa Nkhani ya Sukulu.” Ngati mukufuna kusiya sukulu ndipo makolo anu akuona kuti simunakwaniritse zolinga zanu zopitira kusukulu, ndiye kuti muyenera kuganizira mozama nkhani imeneyi.

Kusiya sukulu kuli ngati kudumpha musitima musanafike kumene mukupita

N’chifukwa chiyani mukufuna kusiya sukulu? Zina mwa zifukwa zimene zingakuchititseni kufuna kusiya sukulu zingakhale kufuna kuthandiza makolo anu pa nkhani yopeza ndalama kapena kufuna kugwira ntchito inayake mongodzipereka. Koma zifukwa zanu zingakhale zosamveka ngati mukuganiza zosiya sukulu chifukwa choopa mayeso kapena kutopa ndi sukulu. Koma nthawi zambiri zimakhala zovuta kuti mudziwe ngati chifukwa chimene chikukuchititsani kuganiza kuti musiye sukulu chili chomveka kapena ayi. Ngati mukusiya sukulu pofuna kuthawa mavuto a kusukulu, mudzanong’oneza bondo.

Kusiya sukulu kuli ngati kudumpha m’sitima musanafike kumene mukupita. Mwina mungaganize zodumpha m’sitimayo chifukwa chakuti si yawofuwofu komanso anthu amene mwakwera nawo akukusowetsani mtendere. Koma ngati mutachita zimenezi, simungafike kumene mukupita komanso mukhoza kuvulala kwambiri. N’chimodzimodzinso ndi sukulu. Ngati mutaisiyira panjira, mungadzavutike kwambiri kuti mupeze ntchito. Ndipo ngati mutadzapeza ntchito, ikhoza kudzakhala ya malipiro ochepa kwambiri poyerekezera ndi ntchito imene mukanapeza zikanakhala kuti munamaliza sukulu.

M’malo mongosiya sukulu, lezani mtima ndipo phunzirani kuthana ndi mavuto amene mumakumana nawo kusukulu. Mukatero, zinthu zidzakuyenderani bwino kwambiri ndipo muzidzatha kuthana ndi mavuto amene mungadzakumane nawo mukadzayamba ntchito.

 Zolinga Zanga pa Nkhani ya Sukulu

Cholinga chachikulu cha maphunziro n’choti mudzathe kupeza ntchito imene ingadzakuthandizeni kupeza zinthu zimene mumafunikira pa moyo wanu, komanso kuti mudzathe kusamalira banja ngati mungadzakhale nalo m’tsogolo. (2 Atesalonika 3:10, 12) Kodi munasankha kale ntchito imene mumafuna kudzagwira? Nanga kodi sukulu ingakuthandizeni bwanji kukonzekera ntchito imeneyi? Kuti mudziwe ngati sukulu ikukuthandizani kuti mudzakwanitse zimene mumafuna, yankhani mafunso otsatirawa:

  • Kodi ndimachita bwino pa zinthu zotani? (Mwachitsanzo, kodi mumacheza bwino ndi anthu? Kodi mumakonda ntchito zamanja, monga kupanga zinthu zatsopano kapena kukonza zinthu zowonongeka? Mukakumana ndi vuto linalake, kodi mumatha kupeza njira yolithetsera?)

  • Kodi ndi ntchito zotani zimene zingagwirizane ndi zinthu zimene ndimachita bwino?

  • Kodi kudera kwathu kumapezeka ntchito zotani?

  • Kodi panopa ndikutenga maphunziro otani amene angadzandithandize kupeza ntchito?

  • Kodi panopa ndingathe kuchita maphunziro otani amene angandithandize kuti ndisadzavutike kukwanitsa zolinga zanga?

Kumbukirani kuti cholinga chanu n’choti mukamadzamaliza sukulu, mudzathe kupeza chochita. Koma musakhalenso ngati anthu amene amangofuna kumangophunzirabe mpaka kalekale, ngati munthu amene sakufuna kutsika sitima, pongofuna kupewa udindo.