Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndingatani Kuti Ndizikhala ndi Mpata Womachita Zinthu Pandekha?

Kodi Ndingatani Kuti Ndizikhala ndi Mpata Womachita Zinthu Pandekha?

 N’chifukwa chiyani makolo anga amakonda kumandilondalonda?

Makolo anu amati amangokuderani nkhawa. Koma inuyo mumaona kuti amakulondalondani. Mwachitsanzo:

  • Mtsikana wina dzina lake Erin anati: “Bambo anga amatenga foni yanga, kundiuza kuti ndiwauze pasiwedi yake ndipo amaona mameseji onse. Ndikamakaniza foni yangayo amaganiza kuti chilipo chimene ndikuwabisira.”

  • Denise, yemwe pano ali ndi zaka za m’ma 20 amakumbukira kuti mayi ake ankakonda kuwerengetsera ndalama zomwe waimbira foni. Iye anati: “Ankaona nambala iliyonse yomwe ndaimba n’kundifunsa kuti ndi ndani amene ndinamuimbirayo ndipo ndimayankhulana naye chani.”

  • Mtsikana winanso dzina lake Kayla yemwe mayi ake anawerenga zinthu zake zachinsinsi mu kabuku komwe ankalembamo anati: “Ndinkakonda kulembamo zokhudza mmene ndinkamvera komanso nkhani zina zokhudza mayi angawo. Kuyambira pamenepo ndinasiiratu kulemba zinthu m’kabukumo.”

Mfundo yofunika kwambiri

 Makolo anu ali ndi udindo wokusamalirani ndipo inuyo simungawaletse kukuikirani malamulo owathandiza kukwaniritsa udindowu. Kodi nthawi zina amaoneka kuti amakhwimitsa zinthu kwambiri? Mwinadi. Koma chosangalatsa n’choti pali zinthu zina zomwe inuyo mungachite kuti azikudalirani.

Zimene Mungachite

Muziwamasukira. Baibulo limatilimbikitsa kuti tizichita “zinthu zonse moona mtima.” (Aheberi 13:18) Choncho, muziyesetsa kukhala oona mtima kwa makolo anu. Ndipo mukamayesetsa kumasuka nawo komanso kuchita zinthu moona mtima, makolo anu azikudalirani ndiponso azikupatsani mpata womachita zinthu panokha.

Zoti muganizire: Kodi anthu amakudziwani monga munthu wodalirika? Kodi nthawi zina mumafika panyumba mochedwa? Kodi mumakonda kubisa anthu omwe mumacheza nawo? Kodi anthu ena zimawavuta kudziwa zomwe mumachita?

“Ndimafunika kusangalatsa makolo anga. Sindimawabisira zinthu zomwe zikundichitikira. Akandifunsa zinazake ndimawauza chilungamo ndipo zimenezi zimachititsa kuti azindikhulupirira komanso azindipatsa mpata wochita zinthu pandekha.”​—Delia.

Muzikhala Wodekha. Baibulo limati: “Pitirizani kudziyesa kuti mudziwe kuti ndinu munthu wotani.” (2 Akorinto 13:5) Pamatenga nthawi kuti munthu akhale wodalirika koma mapeto ake zimakhala zothandiza.

Zoti muganizire: Makolo anu analinso achinyamata nthawi inayake. Kodi mumaona kuti zimenezi n’zimene zimawathandiza kuti azichita chidwi ndi zimene zimakuchitikirani?

“Ndimaona kuti makolo anga amakumbukira zinthu zomwe iwowo ankalakwitsa ndipo safuna kuti ana awofe tichite zomwe iwowo analakwitsapo.”​—Daniel.

Muziwamvetsa. Muziyesa kuona zinthu mmene makolo anu amazionera. Baibulo limati mkazi wabwino “amayang’anira zochitika za pabanja pake” ndiponso bambo wabwino amalera ana ake “m’malangizo a Yehova.” (Miyambo 31:27; Aefeso 6:4) Kuti makolo akwanitse kuchita zimenezi, akuyenera kudziwa zimene zikuchitika pamoyo wanu.

Zoti muganizire: Mukanakhala kuti ndinu kholo ndipo mumadziwa zomwe achinyamata amakumana nazo, kodi mungakonde kuti musamadziwe zomwe mwana wanu akuchita osamufunsa ngakhale pang’ono?

  “Ukakhala wachinyamata umaona ngati makolo ako amakulondalonda. Koma panopa ndine wamkulu ndipo ndikumvetsa chifukwa chimene makolo amachitira zimenezi. Zimangosonyeza kuti amakonda ana awo.”​—James.