Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndingatani Ngati Sindinamvere Lamulo la Makolo Anga?

Kodi Ndingatani Ngati Sindinamvere Lamulo la Makolo Anga?

 Pafupifupi banja lililonse limakhala ndi malamulo, mwina okhudza zinthu ngati nthawi yofikira kunyumba, kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono kapena makhalidwe abwino.

 Koma kodi mungatani ngati mwaphwanya lamulo linalake? Simungasinthe zimene zachitika koma mungathandize kuti zinthu zisaipe kwambiri. Nkhaniyi ikufotokoza zimene mungachite.

 Zimene simuyenera kuchita

 •   Ngati makolo anu sakudziwa kuti simunatsatire lamulo linalake, mwina mungafune kubisa zimene mwachita.

 •   Ngati akudziwa kuti simunamvere lamulolo, mwina mungafune kupereka zifukwa zodzikhululukira kapena kuloza chala munthu wina.

 Si nzeru kuchita zinthu zimenezi. N’chifukwa chiyani tikutero? Zili choncho chifukwa chakuti kubisa zimene mwachita kapena kupereka zifukwa zodzikhululukira n’zachibwana. Zikhoza kuchititsa makolo anu kuganiza kuti simunafike pokhala munthu wodalirika.

 “Si bwino kunama. Pakapita nthawi, zoona zake zidzadziwika ndipo chilango chimene udzapatsidwa chidzakhala chokhwima kwambiri kuposa chimene ukanalandira ngati ukanangonena zoona zake poyamba.”—Diana.

 Zimene zingathandize

 •   Muzivomereza zimene mwalakwitsa. Baibulo limanena kuti: “Wobisa machimo ake zinthu sizidzamuyendera bwino.” (Miyambo 28:13) Makolo anu amadziwa kuti si inu wangwiro. Koma funso n’kumati, Kodi mumachita zinthu moona mtima?

   “Makolo adzakuchitira chifundo ngati unena zoona zake. Ukavomereza zimene wachita, adzayamba kukhulupirira kuti ndiwe woona mtima komanso wokhulupirika.”—Olivia.

 •   Muzipepesa. Baibulo limanena kuti: “Muzichitirana zinthu modzichepetsa.” (1 Petulo 5:5) Kunena kuti “pepani” komanso kupewa kupereka zifukwa zodzikhululukira kumafuna kudzichepetsa.

   “Anthu amene nthawi zonse amapereka zifukwa zodzikhululukira akhoza kuwononga chikumbumtima chawo. Kenako akhoza kusiyiratu kudziimba mlandu akachita zinthu zoipa.”—Heather.

 •   Muzivomereza chilango chimene mwalandira. Baibulo limanena kuti: “Mverani malangizo.” (Miyambo 8:33) Muzipewa kudandaula ndipo muzichita zinthu mogwirizana ndi chilango chimene makolo anu akupatsani.

   “Ukamangodandauladandaula ndi chilango chimene walandira, zinthu zikhoza kuipa kwambiri. Uziyesetsa kungovomereza chilangocho m’malo mochiganizira kwambiri.”—Jason.

 •   Muziyesetsa kukhala wodalirika. Baibulo limanena kuti: “Muvule umunthu wakale umene umagwirizana ndi khalidwe lanu lakale.” (Aefeso 4:22) Muyambe kuchita zinthu zosonyeza kuti ndinu wodalirika.

   “Nthawi zonse ukamayesetsa kusankha zochita mwanzeru n’kumasonyeza makolo ako kuti sudzachitsanso zimene unalakwitsazo, iwo adzayambanso kukukhulupirira.”—Karen.

 ZIMENE ZINGAKUTHANDIZENI: Muzichita zonse zimene mungathe posonyeza kuti ndinu wodalirika. Mwachitsanzo, mukachoka pakhomo, muziuza makolo pamene muli m’njira yobwerera kunyumba ngakhale ngati simufika mochedwa. Izi zingawasonyeze kuti mukufuna kuti iwo azikukhulupirirani.